Chikhulupiriro mwa Mulungu Kodi Chimalira Chozizwitsa?
ALBERT anali wazaka zoyambirira za ma 20 pamene anayamba kufunafuna Mulungu. Anayesa zipembedzo zingapo koma sanakhutirebe iyayi. Poŵerenga zigawo za Baibulo, anamva mmene Mulungu anachitira ndi anthu onga Nowa, Abrahamu, Sara, ndi Mose. Albert anakopeka ndi Mulungu wa Baibulo. Komabe, kodi akanatsimikiza kuti Mulungu alikodi?
Madzulo ena Albert anapita ndi galimoto kumalo obisika kumene anapemphera kuti, “Chonde Mulungu, ndipatseni chizindikiro—chilichonse chosonyeza kuti muliko.” Albert anadikira chidikirire. Akukumbukira kuti pamene sanaone chilichonse, chiyembekezo chake “chinasanduka chisoni, kunyong’onyeka, ndi mkwiyo.”
Mofanana ndi Albert, ambiri amamva kuti afunafuna Mulungu pachabe. Amasokonezedwa ndi maulaliki a atsogoleri achipembedzo kapena kugwiritsidwa mwala ndi alaliki a pawailesi yakanema ochita malonda. Poona chinyengo choonekeratu mwa anansi awo ochuluka, ena sakudziŵa kuti akhulupirire chiti. Komabe, Mfumu Davide wa Israyeli wakale anamtsimikizitsa mwana wake Solomo kuti: “Ukamfunafuna [Mulungu], udzampeza.”—1 Mbiri 28:9.
Chabwino, tsopano kodi Mulungu amadzivumbula yekha motani? Kodi muyenera kuyembekezera chizindikiro—chochitika chozizwitsa chimene chidzakusonyezani kuti Mulungu aliko? Malinga ndi kuŵerengera kwa posachedwapa kolembedwa m’magazini ya Time, Aamereka oposa zigawo ziŵiri mwa zitatu amakhulupirira zozizwitsa. Nkhaniyo inanenanso kuti “matchalitchi okula msanga ku America ndiwo mipingo ya Machiritso ndi ya Pentekoste imene kulambira kwake nkwa ‘zizindikiro ndi zozizwitsa.’”
Kodi kukhulupirira Mulungu kuyeneradi kulira “zizindikiro ndi zozizwitsa”? Anagwiritsira ntchito zizindikiro m’nthaŵi zakale. Mwachitsanzo: Saulo wa ku Tariso, yemwe anali kuzunza atsatiri a Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anaona zodabwitsa ali panjira pochokera ku Yerusalemu kumka ku Damasiko. Kuonana ndi Yesu woukitsidwayo mwanjira yozizwitsa imeneyi kunamtembenuza Saulo. (Machitidwe 9:1-22) Choncho yemwe anali wozunza anakhala mtumwi Paulo—mmodzi wa achirikizi amphamvu a Chikristu!
Koma kodi zozizwitsa nthaŵi zonse zimachititsa anthu kukhala ndi chikhulupiriro? Kodi kukhulupirira Mulungu moonadi kumadalira pakuona chozizwitsa?
[Chithunzi patsamba 3]
Mwana wa Mulungu analankhula ndi Saulo wa ku Tariso mozizwitsa. Kodi muyenera kuyembekezera chozizwitsa?