Kodi Amene Akuzunzika Adzakhaladi ndi Mtendere?
KODI mukufuna kuti mavuto athe? Osati mavuto anu okha koma a anthu onse? Taonani zitsanzozi:
Sonia wavutikapo ndithu.a Choyamba, anadzadziŵa kuti mwamuna wake anali kuyenda ndi mkazi wina zaka khumi. Ndiyeno mwana wake wamwamuna wothera anatenga kachilombo ka HIV namwalira ndi AIDS. Patapita zaka ziŵiri, mwana wake wina wamwamuna anadwala, ndipo iyenso, posakhalitsa, anamwalira ndi AIDS. “Matsiriziro a matenda ake anatenga nthaŵi yaitali kwambiri,” akukumbukira Sonia. “Anachita tondovi kwambiri, tsitsi lake lonse linatha kukudzuka, ndipo sanali kuona bwino. Zinali zachisoni.”
Fabiana, Mbrazilu wophunzira payunivesite, anada nkhaŵa ndi chisalungamo cha anthu m’dziko. Kenako, tsoka linamgwera. Mbale wake, amene anachita tondovi, anadzipha. Pamene Fabiana anachotsedwa ntchito, mnzake anamlimbikitsa kukafunsira kwa pai-de-santo (sing’anga), poganiza kuti panali wina amene anamlodza Fabiana kuti masoka otero amgwere! Koma pai-de-santo ameneyo sanampatse mpumulo ayi. M’malo mwake, Fabiana anazunzika, nalephera kumagona chifukwa cha mavuto ake.
Ana mavuto ake anayamba akali mwana. “Pamene ndinali ndi chaka chimodzi,” akutero, “amayi anandisiya, choncho agogo aakazi ndiwo anayamba kundilera.” Ndiyeno, pamene Ana anali ndi zaka zitatu zokha, agogo akewo anamwalira. Anayo anampereka kunyumba ya amasiye ku Rio de Janeiro, kumene anakhala mpaka atakwanitsa zaka 13. “Kumeneko sanatisunge bwino ayi, choncho ndinakhala wosamvera,” akutero. “Pamene ndinali kukula, sindinafune zilizonse.”
Mazunzo akuoneka ngati amakhudza moyo wa munthu aliyense m’njira zosiyanasiyana. Inde, timamva nkhani za masoka a anthu masiku onse—paliponse pamene tionerera, kuŵerenga, kapena kumvetsera nkhani. “M’nyengo yathu ino . . . ya njira zambiri zoulutsira nkhani kuposa ndi kale lonse, kwakhala kosatheka konse kupeŵa mbiri yoipa youlutsidwa kosaleka,” akulemba Dr. Mary Sykes Wylie. “Nkhondo, masoka achilengedwe, ngozi za m’maindasitale, ngozi za pamsewu, upandu, uchigaŵenga, kugona ana, kuchita mizambi, chiwawa m’banja—zonsezo zimachititsa nsautso kukhala chizindikiro choipa ndi chamasiku onse m’zaka za zana la 20 zino.” Paulo mtumwi wachikristu, pofotokoza mwachidule zimene anthu akumana nazo, anati mosabisa: “Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi.”—Aroma 8:22.
Nanga inu bwanji? Kodi mukuzunzika? Kodi ndi mpumulo wanji umene mungayembekeze? Kodi mudzaupeza mtendere weniweni? Sonia, Fabiana, ndi Ana anapeza chitonthozo chenicheni ndi mtendere wambiri ndithu! Ŵerengani zimenezo m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Maina a m’nkhani ino asinthidwa.