Maukwati Olemekeza Yehova
khani Yotsatirayi Pamaukwati Achikristu Inakonzedwa Ku Ethiopia Kuti Ipereke Chitsogozo M’chiamhara Kuthandiza Ambiri M’dzikolo Omwe Akhala Mboni Za Yehova Posachedwa. Ikufotokoza Miyambo Yawo Ndi Machitidwe Amene Angakhale Osiyana Ndi Akwanuko. Mosakayika, Mudzachita Nako Chidwi Kusiyana Kumeneko. Komanso, Nkhaniyi Ikupereka Uphungu Wabwino Wa M’baibulo Umene Mudzapeza Kuti Umagwiranso Ntchito Ngakhale Ngati Miyambo Ya Ukwati Kwanuko Ili Yosiyana Ndi Imeneyi.
NKHANI yabwino yophunzira mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1984 inali ndi mutu wakuti, “Mapwando Aukwati Wachikristu Amene Amasangalatsa.” Nkhani yotsatira m’kopelo inali ndi mutu wakuti, “Pezani Chisangalalo Chachikatikati pa Mapwando Aukwati.” (Aliyense amene akuganiza zokwatira angapeze uphungu wina wanzeru m’buku la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe, mutu 2, ndi Your Youth—Getting the Best Out Of It, mitu 19 ndi 20.)a Ambiri akhala Mboni za Yehova kuyambira pamene nkhanizo zinatuluka, choncho tikufuna kubwereza mfundo zina m’nkhani zimenezi zimene zimagwira ntchito makamaka kuno kwathu, limodzinso ndi mfundo zina zoyenera zimene zidzatithandiza kuchititsa mapwando a ukwati kukhala nthaŵi yolemekeza Yehova, Myambitsi wa ukwati.
Funso lomwe tingayambe nalo nlakuti, Kodi ukwati uyenera kukhalako liti? Kodi tsiku lake liyenera kusankhidwa malinga ndi masiku a nyengo yamwambo ya maukwati akwanuko? Kuno amakhulupirira kuti ngati ukwati uchitika panthaŵi ina ya chaka sudzakhala bwino ayi. Chikhulupiriro chimenechi chilibe maziko, pakuti mabanja ambiri amene ali achimwemwe ndipo akutumikira Yehova mogwirizana sanakwatirane panyengo yamwambo. Ife sitimakhulupirira mwaŵi kapena tsoka. (Yesaya 65:11; Akolose 2:8) Sitingawathandize achibale athu osakhulupirira kuona kusiyana kwa choonadi ndi bodza ngati tisankha tsiku la ukwati malinga ndi zikhulupiriro zawo. Choonadi nchakuti, Akristu angakwatirane mwezi uliwonse.
Ngati kudzakhala nkhani ya ukwati pambuyo potchata kuboma, kungakhale kwanzeru kusalola masiku ambiri kupita. Ngati amene akukwatiranawo afuna kuti nkhani ya ukwati wawo ikakambidwe m’Nyumba ya Ufumu, ayenera kuonana ndi akulu a mpingo kukali nthaŵi yokwanira kuwapempha holoyo kuti akaigwiritsire ntchito. Akuluwo adzafuna kutsimikiza kuti makonzedwe a ukwatiwo adzawasiya ndi chikumbumtima chabwino. Ayenera kusankha nthaŵi imene sidzawombana ndi zochita za mpingo. Mbale wosankhidwa kukakamba nkhani ya ukwati ayenera kuonana ndi mkwati ndi mkwatibwi wake pasadakhale kuwapatsa uphungu wothandiza ndi kutsimikiza kuti palibe nkhani ya makhalidwe kapena ya zamalamulo imene ingaletse ukwatiwo ndi kuti akugwirizana nawo makonzedwe onse a madyerero otsatirapo. Nkhani ya ukwati iyenera kukhala yautali ngati theka la ola ndipo iyenera kukambidwa mwaulemu, kugogomezera zauzimu. Nkhani ya ukwati njofunika kwambiri kuposa madyerero alionse omwe angatsatirepo.
Ukwati wachikristu ndiyo nthaŵi yabwino yosonyezerapo kuti ‘sitili a dziko lapansi.’ (Yohane 17:14; Yakobo 1:27) Kukhala kwathu adongosolo kuyenera kuonekera. Zimenezi zikutanthauza kuti tidzafika panthaŵi yake m’malo motayira anthu nthaŵi kuyembekezera, mwina kusokoneza ndi zochitika za mpingo zomwe. Makamaka mkwatibwi afunikira kusamala zimenezi, pakuti achibale ake akunja angamlimbikitse kuchedwa—kuyesa kuonetsa kuti ali wamtengo wapatali. Mwa kusunga nthaŵi, mlongo wachikristu wokhwima mwauzimu angasonyeze kuti amaona mikhalidwe yauzimu, monga kudzichepetsa ndi kulingalira ena, kukhala yofunika kwa iye! Ndiponso, pamene wojambula zithunzithunzi waitanidwa, ayenera kutsata dongosolo. Tiyenera kumuuza kubwera atavala jekete, tayi, ndi talauza labwino ndi kuti sayenera kusokoneza nkhaniyo potenga zithunzithunzi. Sayenera kujambula zithunzithunzi popemphera. Kutsata kwathu dongosolo kudzalemekeza Yehova ndi kupereka umboni wabwino. Palibe chifukwa chotsatirira miyambo ya anthu imene ingasokoneze tanthauzo lenileni la chochitikacho.
Sipachitofunikira madyerero kuti ukwati ukhale wachipambano, komanso Malemba saletsa nthaŵi yosangalala imeneyo. Komabe, macheza otero a Akristu oona ayenera kusiyana ndi madyerero akunja amene amakhala opambanitsa, omwetsa moŵa, madyaidya, nyimbo zophokosera, kavinidwe konyanyula, ndi ndewu zomwe. Baibulo limati “mchezo” ndi ntchito ya thupi. (Agalatiya 5:21) Nkwapafupi kuyang’anira zinthu bwino pamene gululo si lalikulu kwambiri. Sipafunikira kuika hema kutsata miyambo yofala. Ngati ena asankha kuika hema chifukwa cha malo kapena mvula, imeneyo ndi nkhani yaumwini.
Zochitika zasonyeza kuti njira yabwino yochepetsera chiŵerengero cha opezekapo ndiyo mwa kuwalembera makhadi. Kuli bwino kuitana munthu payekhapayekha kuposa kuitana mpingo wonse, ndipo pokhala Akristu adongosolo, tiyenera kulemekeza makonzedwewo oitana anthu ochepa. Makhadi makamaka amathandizanso kupeŵa kukhala ndi wochotsedwa pamadyereropo, zimene zingasokoneze zinthu, pakuti ngati iye angabwerepo, abale ndi alongo ambiri angachokepo. (1 Akorinto 5:9-11) Ngati amene akukwatiranawo aitana achibale osakhulupirira kapena mabwenzi, mosakayika ameneŵa adzakhala ochepa, popeza ofunika makamaka ndi aja “apabanja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Ena aitanira achibale ndi mabwenzi akunja ku nkhani yaukwati chabe osati kumadyerero. Chifukwa ninji? Eya, zachitika nthaŵi zina kuti achibale akunja achita zamanyazi kwambiri pamadyerero a ukwati moti abale ndi alongo ambiri anachokapo. Ena amene akukwatirana akonza chakudya chochepa cha iwo okha ndi mabanja awo ndi mabwenzi achikristu basi.
Mogwirizana ndi Yohane 2:8, 9, zimathandiza kusankha “mkulu wa phwando.” Mkwati ayenera kusankha Mkristu amene amdalira kwambiri, amene adzatsimikiza kuti pali dongosolo ndi khalidwe labwino kwambiri. Ngati mabwenzi adzapereka mphatso, ayenera kuchita zimenezo popanda “matamandidwe a moyo.” (1 Yohane 2:16) Nyimbo zingakhale zosangalatsa ngati zilibe mawu okayikitsa, si zaphokoso kwambiri, kapenanso zamaimbidwe osadekha. Ambiri apeza kuti zimathandiza kupempha mkulu kuti amvetsere nyimbo zimene zidzaimbidwazo pasadakhale. Kuvina kuli ndi mbuna zake, pakuti mavinidwe ambiri amwambo anatengedwa kumavinidwe a madzoma a kubala ndipo amanyanyula. “Nthaŵi yodula keke ndi kupereka moŵa wa champagne” nthaŵi zina yakhala chizindikiro chakuti anthu akunja amasuke kuchita mulimonse mmene afunira. Kwenikweni, Akristu ambiri amene akukwatirana asankha kusakhala ndi moŵa uliwonse pamadyerero a ukwati, ndipo apeŵa mavuto.
Popeza tikufuna kulemekeza Yehova, tidzapeŵa kudzionetsera kuti ena atione. Ngakhale mabuku a dziko atsutsa mzimu wofala wochita zinthu monkitsa. Kungakhale kusoŵa nzeru chotani nanga ngati amene akukwatirana aloŵa m’ngongole chifukwa cha ukwati wambambande ndiyeno nkumavutika zaka zambiri kuti alipirire zimene anawononga tsiku limodzi lokhalo! Inde, chovala chilichonse chomwe munthu avala panthaŵiyo chiyenera kukhala chaulemu ndi chokonzeka, choyenera munthu amene amati amaopa Mulungu. (1 Timoteo 2:9, 10) Nkhani yakuti “Maukwati Achikristu Akhale Oyenera” (Nsanja ya Olonda ya January 15, 1969, yachingelezi) inanena mfundo izi zofunika:
“Ukwati wa munthu umakhala chochitika chapadera, chotero mwachibadwa iye amasamala kwambiri kuti aoneke wosangalala ndi wokongola. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti afunikira kuvala malaya kapena suti ya mtundu wina wake. Angachite bwino kulingalira za masitayelo akwawo, ndalama ndi zimene amakonda. . . . Koma kodi kungakhale koyenera kugula zovala zokwera mtengo kwambiri zimene zingaloŵetse iwo kapena ena m’mavuto a ndalama? . . . Akwatibwi ena agwiritsira ntchito malaya a bwenzi lawo kapena a wachibale. Ena akhutira kwambiri ndi kudzipangira okha zovala za ukwati, mwina motero kukhala ndi chovala chimene angamachivale panthaŵi zina mtsogolo. Ndipo zili bwino kwambiri kwa omwe akukwatirana kuvala zovala zawo zamasiku onse zabwino koposa . . . Ena amene angakhoze kuchita ukwati wambambande amasankha kuchita ‘ukwati wosafuna zambiri’ chifukwa cha zovuta za nthaŵi zino.”
Momwemonso, operekeza akwati (mabwenzi a mkwati ndi anzake a mkwatibwi) sayenera kuchuluka. Iwonso sadzafunikira kudzionetsera ndi kavalidwe ndi zochita zawo. Pamene munthu wochotsedwa angaloledwe kupezekapo pankhani m’Nyumba ya Ufumu, Nsanja ya Olonda ya October 15, 1984, inati: ‘Nkosayenera kukhala ndi munthu wochotsedwa pa operekeza akwati kapena munthu amene mbiri yake imawombana ndi mapulinsipulo a Baibulo.’
Ngakhale kuti Yesu anapezeka paukwati, sitingaganize kuti akanalola mwambo wofala wokhala ndi magalimoto omazungulira mzinda ndi kumaphokosera kwambiri; apolisi alipiritsadi faindi adilaivala oliza mabelu m’magalimoto a ukwati. (Onani Mateyu 22:21.) Mwachidule, m’malo mwa matamandidwe a moyo kapena zochita zozoloŵereka za anthu akunja, Akristu amasonyeza nzeru imene ili ndi odzichepetsa.—Miyambo 11:2.
Nanga bwanji za kupita kuukwati wa mabwenzi, anzathu akuntchito akunja, kapena achibale ndi achinansi? Mkristu aliyense ayenera kudzisankhira yekha zochita. Ndi bwino kukumbukira kuti nthaŵi yathu njamtengo wapatali, popeza timafuna nthaŵi ya utumiki wathu, phunziro laumwini, ndi ntchito zina za banja ndi za mpingo. (Aefeso 5:15, 16) Loŵeruka ndi Sande timakhala ndi misonkhano ndi utumiki wakumunda zimene sitiyenera kuphonya. (Ahebri 10:24, 25) Nthaŵi ya maukwati ambiri imawombana ndi misonkhano kapena utumiki wakumunda wapadera wapanthaŵi ya Mgonero wa Ambuye. Tisachenjenekedwe ndi kulephera kuchita khama limene abale athu padziko lonse akuchita kuti apezeke pa Mgonero wa Ambuye. Tisanadziŵe choonadi, timataya nthaŵi yochuluka ndi anthu akunja, mwinamwake pazochitika zosalemekeza Mulungu. (1 Petro 4:3, 4) Tsopano zimene timayesa zinthu zofunika nzosiyana ndi zimenezo. Nthaŵi zonse zimatheka kufunira dalitso amene akukwatiranawo mwa kuwatumizira khadi kapena kukawachezera pang’ono tsiku lina. Ena agwiritsira ntchito nthaŵi zotero kupereka umboni, kukambitsirana nawo malemba ena oyenerera okwatirana chatsopano.
Ukwati umene pamachuluka zauzimu m’malo mwa njira za dziko umalemekezadi Yehova. Mwa kutsimikiza kuti akulekana ndi dziko ndi miyambo yake ndiponso ndi mzimu wake wochita zinthu monkitsa, mwa kusalola ukwati kusokoneza zochita zanthaŵi zonse zateokrase, ndi mwa kusonyeza chifatso m’malo mwa matamandidwe a moyo, Akristu adzakondwa nacho chochitikacho. Ndiponso, pokumbukira chochitikacho chitapita, adzakhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo adzakondwera. Mwa kusonyeza nzeru ndi kusamala, maukwati athu onse achikristu apereketu umboni kwa anthu oona mtima openyerera.
[Mawu a M’munsi]
a Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Akristu samatsata mwaukapolo mwambo wakwawo uliwonse wa ukwati