‘Timafuna Anthu Oona Mtima’
KUONA MTIMA nkovuta kupeza m’dziko lero. Komabe, ndiko chinthu chachikulu chofunika kwa Akristu. Paulo analemba kuti: “Takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m’zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.” (Ahebri 13:18) Izi nzimene anafuna kuchita Wilma, mmodzi wa Mboni za Yehova mu Faenza, ku Italy.
Nyuzipepala ya Il Resto del Carlino inati pamene iye anapeza chikwama mmene munali ndalama zambiri panja pa supamaketi mumzinda wa kwawo, anachipereka kupolisi “mosazengereza” konse kotero kuti akachibwezere kwa mwini wake.
Bwanamkubwa atamva zimenezi, mwamsanga anatumiza kalata yachidule yomuyamikira Wilma. “M’dzina la Mzindawu,” anatero kulemba kwake, “ndikuthokozani kwabasi pakachitidwe kanu kokomako. Mzinda wathu wolemekezekawu wa Faenza umafuna anthu abwino ndi oona mtima.”
Kaya machitidwe abwino adziŵike kapena ayi, nthaŵi zonse tiyenera kuyesa kukhala oona mtima. Monga amalimbikitsira Malemba Oyera, “pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.”—2 Akorinto 8:21.