Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 5/15 tsamba 30-31
  • Epafra “Mtumiki Wokhulupirika wa Kristu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Epafra “Mtumiki Wokhulupirika wa Kristu”
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mlaliki wa ku Chigwa cha Lycus
  • Lipoti la Epafra
  • Munthu Woona Pemphero Kukhala la Mtengo Wapatali
  • Thandizani Ena Kuyenda Moyenera Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • “Ngati Zimenezi Mukuzidziwa, Ndinu Odala Mukamazichita”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Yehova Akhoza Kukulimbikitsani
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 5/15 tsamba 30-31

Epafra “Mtumiki Wokhulupirika wa Kristu”

NDANI anayambitsa mipingo yachikristu ku Korinto, Efeso, ndi ku Filipi? Mwinamwake simungakayikire poyankha kuti: ‘Paulo, “mtumwi wa anthu amitundu.”’ (Aroma 11:13) Ndiye kuti mwakhoza.

Komabe, ndani anakhazikitsa mipingo ku Kolose, Herapoli, ndi Laodikaya? Ngakhale kuti sitingatsimikizire kwenikweni, ayenera kukhala munthu wotchedwa Epafra. Mulimonse momwe zingakhalire, mwina inu mungakonde kudziŵa zambiri za mlaliki ameneyu, popeza akutchedwa “mtumiki wokhulupirika wa Kristu.”​—Akolose 1:7.

Mlaliki wa ku Chigwa cha Lycus

Dzinalo Epafra ndi chidule cha Epafrodito. Koma tisasokoneze Epafra ndi Epafrodito wa ku Filipi. Epafra anali wa ku Kolose, amodzi mwa malo atatu mmene munali mipingo yachikristu m’chigwa cha Mtsinje wa Lycus, ku Asia Minor. Kolose anali pa mtunda wa makilomita 18 kuchokera ku Laodikaya ndi makilomita 19 kuchokera ku Herapoli, m’chigawo cha Frugiya wakale.

Baibulo silinena mwachindunji mmene uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu unafikira ku Frugiya. Komabe, anthu a ku Frugiya analipo mu Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E., mwinamwake ena mwa iwo anali a ku Kolose. (Machitidwe 2:1, 5, 10) Panthaŵi ya utumiki wa Paulo ku Efeso (pafupifupi 52-55 C.E.), umboni woperekedwa m’dera limenelo unali wamphamvu ndi wobala zipatso mwa kuti si Aefeso okha komanso “onse akukhala m’Asiya anamva mawu a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene.”(Machitidwe 19:10) Kukuoneka kuti Paulo sanalalikire Uthenga wabwino m’Chigwa chonse cha Lycus, chifukwa ambiri amene anakhala Akristu m’dera limenelo sanamuone.​—Akolose 2:1.

Malinga nkunena kwa Paulo, yemwe anaphunzitsa Akolose za “chisomo cha Mulungu m’choonadi” anali Epafra. Popeza Paulo akutcha wantchito mnzakeyu kuti “mtumiki wokhulupirika wa Kristu chifukwa cha ife” ndiye kuti Epafra anali mlaliki wamphamvu m’deralo.​—Akolose 1:6, 7.

Onse aŵiri mtumwi Paulo ndi mlalikiyo Epafra anali ndi nkhaŵa yaikulu pa za mkhalidwe wauzimu wa okhulupirira anzawo m’Chigwa cha Lycus. Monga “mtumwi wa anthu amitundu” Paulo ayenera kuti anakondwera kulandira uthenga wa kupita kwawo patsogolo. Sikwawinanso kumene Paulo anamva za mkhalidwe wauzimu wa Akolose koma kwa Epafra.​—Akolose 1:4, 8.

Lipoti la Epafra

Akolose anakumana ndi mavuto akulu kwambiri kwakuti Epafra anakakamizika kupanga ulendo wautali wopita ku Roma ncholinga chokakambitsirana zimenezo ndi Paulo. Lipoti latsatanetsatane la Epafra mwachionekere ndilo linasonkhezera Paulo kulemba makalata aŵiri kwa abalewo amene mwinamwake sankaŵadziŵa. Imodzi inali kalata yopita kwa Akolose. Kalata inayi, imene mwachionekere sinasungidwe, inatumizidwa kwa Alaodikaya. (Akolose 4:16) Nkwanzeru kulingalira kuti makalatawo analembedwa pofuna kusamalira zofunikira kwa Akristuwo monga momwe Epafra adazionera. Kodi iye anaona zofunikira zotani? Ndipo kodi zimenezi zikutiuzanji za umunthu wake?

Kalata ya kwa Akolose imasonyeza ngati kuti Epafra anali ndi nkhaŵa yakuti Akristu a ku Kolose anali pangozi chifukwa cha ziphunzitso zachikunja monga kudzikana, kukhulupirira mizimu, kuopa mafano. Kuwonjezera apo, chiphunzitso chachiyuda cha kusala zakudya ndi kusunga masiku ena mwina chinali chitakhudza mamembala ena mumpingowo.​—Akolose 2:4, 8, 16, 20-23.

Popeza Paulo analemba za zimenezi ndiye kuti Epafra anali watcheru pa zofunikira kwa Akristu anzake. Iye anada nkhaŵa mwachikondi ndi mkhalidwe wawo wauzimu, atadziŵa bwino lomwe za kuopsa kwa malo amene amakhalako. Epafra anafuna uphungu wa Paulo, ndipo ichi chimavumbula kuti iye anali wodzichepetsa. Mwinamwake anaona kufunikira kwa chithandizo cha winawake wozoloŵera. Mulimonse momwe zinalili, Epafra anachita mwanzeru.​—Miyambo 15:22.

Munthu Woona Pemphero Kukhala la Mtengo Wapatali

Pomaliza kalata imene anatumiza kwa Akristu a ku Kolose, Paulo akuti: “Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Yesu Kristu, wakulimbira chifukwa cha inu m’mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m’chifuniro chonse cha Mulungu. Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziŵaŵitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a m’Laodikaya, ndi iwo a m’Herapoli.”​—Akolose 4:12, 13.

Inde, ngakhale pamene anali ‘wandende mnzake’ wa Paulo m’Roma, Epafra anali kuganiza za abale ake okondedwa ku Kolose, Laodikaya, ndi Herapoli ndi kuwapempherera. (Filemoni 23) Kwenikweni, ‘iye analimbikira’ chifukwa cha iwo m’pemphero. Malinga nkunena kwa katswiriyo D. Edmond Hiebert, liwu lachigiriki logwiritsidwa ntchito pano limasonyeza “ntchito yolimba ndi yolira zambiri,” mwinamwake yofanana ndi ‘kupsinjika’ maganizo komwe kunachitikira Yesu Kristu pamene ankapemphera m’munda wa Getsemani. (Luka 22:44) Epafra analakalaka kwambiri kuti abale ndi alongo ake auzimu afike pa kulimba ndi uchikulire wachikristu. Mbale wamalingaliro auzimu ameneyu anali dalitso kumipingo bwanji!

Popeza Epafra ankatchedwa “kapolo mnzathu wokondedwa,” sipangakhale zikayikiro kuti anadzipangitsa yekha kukhala wosiririka kwa Akristu anzake. (Akolose 1:7) Kukakhala kotheka, onse mumpingo ayenera kudzipereka okha mwaufulu mofunitsitsa ndi mwachikondi. Mwachitsanzo, chisamaliro chingaperekedwe kwa odwala, okalamba, kapenanso ena okhala ndi zosoŵa zapadera. Pangakhale ntchito zosiyanasiyana zoyenera kusamalira mumpingo, mwina kungakhalenso kotheka kuthandiza pa ntchito yomanga.

Kupempherera ena, monga momwe Epafra anachitira, ndi mtundu wa utumiki wopatulika umene onse angachite. Mmapemphero otero mungaphatikizemo nkhaŵa yanu pa alambiri a Yehova omwe ali pangozi kapena zovuta zosiyanasiyana za uzimu mwina zakuthupi. Podzipereka ife eni mwamphamvu chotero, tidzakhala ngati Epafra. Aliyense wa ife angakhale ndi mwaŵi ndi chimwemwe chosonyeza kukhala “kapolo mnzathu wokondedwa” m’banja la atumiki okhulupirika a Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena