Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/1 tsamba 24-27
  • Kufooka kwa Anthu Kusonyeza Mphamvu ya Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufooka kwa Anthu Kusonyeza Mphamvu ya Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kupirira Mayesero
  • Kupirira Zophophonya
  • Mphamvu Yolalikira
  • Kulimbana ndi “Munga M’thupi”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Muli ndi “Munga m’Thupi”?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Paulo Anali ndi “Munga M’thupi”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/1 tsamba 24-27

Kufooka kwa Anthu Kusonyeza Mphamvu ya Yehova

“Aliyense ankandiona monga mtumiki wanthaŵi zonse wachimwemwe ndi waumoyo. Nthaŵi zonse ndine ndinali kuthandiza ena pamavuto awo. Komabe, nthaŵi imodzimodziyo, ndinali kumva monga ndidzafa mumtima. Malingaliro osautsa ndi kuzunzika mtima zinali kundidya. Ndinayamba kudzipatula pa anthu. Ndinali kungofuna kugona kunyumba. Kwa miyezi yambiri, ndinampempha Yehova kuti andisiye ndife.”​—Vanessa.

MOFANANA ndi chochitika chofotokozedwa pamwambapa, nkwachibadwa kuti nthaŵi zina atumiki a Yehova amamva kuipa kwa kukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino. (2 Timoteo 3:1) Ndiponso ena amachita tondovi. (Afilipi 2:25-27) Kuchita tondovi kutapitiriza nthaŵi yaitali kungatilande mphamvu yathu, popeza Baibulo limati: “Ukalefuka tsiku latsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 24:10) Inde, pamene talefulidwa, timafunikira mphamvu​—mwinamwake ngakhale ija yomwe mtumwi Paulo anaitcha “mphamvu yoposa yachibadwa.”​—2 Akorinto 4:7, NW.

Yehova Mulungu ndiye mwini mphamvu yopanda malire. Zimenezi zimaoneka tikapenda chilengedwe chake. (Aroma 1:20) Titenge dzuŵa, mwachitsanzo. Nthaŵi zonse dziko limatsekereza mphamvu ya dzuŵa yokwanira ma horsepower 240,000,000,000,000. Komabe, nambala imeneyi imaimira chigawo chimodzi chabe mwa zigawo mamiliyoni zikwi ziŵiri za mphamvu yonse imene dzuŵa limatulutsa. Ndipo dzuŵa nlaling’ono poliyerekezera ndi nyenyezi zina zimene amati ma supergiants. Ina mwa zimenezi ndi Rigel, nyenyezi ya m’gulu la Orion imene ukulu wake umaposa ukulu wa dzuŵa lathu nthaŵi 50 ndipo imatulutsa mphamvu yoposa ya dzuŵa lathu nthaŵi 150,000!

Mlengi wa zinthu zotulutsa mphamvu zimenezi za kumwamba ayenera kuti iyeyo ali ndi ‘mphamvu zazikulu.’ (Yesaya 40:26; Salmo 8:3, 4) Nchifukwa chakedi mneneri Yesaya ananena kuti Yehova “salefuka konse, salema.” Ndipo Mulungu ali wofunitsitsa kugaŵira mphamvu yake kwa alionse amene akuona kuti akulefuka chifukwa cha kufooka kwaumunthu. (Yesaya 40:28, 29) Nkhani ya mtumwi wachikristu Paulo ikusonyeza mmene Yehova amachitira zimenezi.

Kupirira Mayesero

Paulo anauza Akorinto za chopinga chimene anafunikira kupirira. Anachitcha “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7) “Munga” umenewu uyenera kuti unali vuto lina la thanzi, mwinamwake kufa maso. (Agalatiya 4:15; 6:11) Kapena mwinamwake Paulo anali kunena za atumwi onyenga ndi osokoneza ena amene ankatsutsa utumwi wake ndi ntchito yake. (2 Akorinto 11:5, 6, 12-15; Agalatiya 1:6-9; 5:12) Sitikudziŵa kuti unali chiyani, koma “munga m’thupi” umenewu unamsautsa mtima kwambiri Paulo, ndipo anapemphera mobwerezabwereza kuti uchotsedwe.​—2 Akorinto 12:8.

Komabe, Yehova sanapereke chimene Paulo anapempha. M’malo mwake, anauza Paulo kuti: “Chisomo changa chikukwanira.” (2 Akorinto 12:9) Kodi Yehova anatanthauzanji ndi zimenezi? Eya, titalingalira za zimene Paulo ankachita kale zozunza Akristu, kunali kokha mwa chisomo cha Mulungu kuti akhale naye paunansi​—ngakhale kutumikira monga mtumwi!a (Yerekezerani ndi Zekariya 2:8; Chivumbulutso 16:5, 6.) Mwinamwakenso Yehova anali kuuza Paulo kuti mwaŵi wake wokhala wophunzira unali ‘wokwanira.’ Sanafunikire kumchotseranso mozizwitsa mavuto ake a m’moyo. Kunena zoona, mavuto ena amadza chifukwa cha maudindo owonjezereka. (2 Akorinto 11:24-27; 2 Timoteo 3:12) Mulimonse mmene zinalili, Paulo anangofunikira kupirira ‘munga wake wa m’thupi.’

Komabe, sikuti Yehova anamsiyiratu Paulo mopanda chifundo. M’malo mwake, anamuuza kuti: “Mphamvu yanga ithedwa mu ufoko.” (2 Akorinto 12:9) Inde, Yehova mwachikondi anali kumpatsa nyonga Paulo yoti apirire vuto lake. Choncho, ‘munga wa m’thupi’ wa Paulo unakhala chochitika chopereka chitsanzo. Chinamphunzitsa kusadalira nyonga yake koma ya Yehova. Mwachionekere Paulo analiphunziradi bwino phunziroli, popeza patapita zaka zingapo analembera Afilipi kuti: “Ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:11, 13.

Inuyo bwanji? Kodi mukupirira chinachake chonga “munga m’thupi,” mwinamwake matenda kapena vuto linalake m’moyo limene likukudetsani nkhaŵa kwambiri? Ngati zili choncho, tontholani. Pamene kuli kwakuti mwina Yehova sadzachotsapo chopingacho mozizwitsa, atha kukupatsani nzeru ndi nyonga yoti muchipirire pamene mupitirizabe kuika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo.​—Mateyu 6:33.

Musataye mtima ngati matenda kapena ukalamba ukuletsani kuchita zambiri mu utumiki wachikristu monga momwe mungakondere. M’malo moona chiyeso chanu kuti chikuchepetsa utumiki wanu kwa Yehova, chioneni monga mwaŵi wokulitsira chidaliro chanu pa iye. Kumbukiraninso kuti kufunika kwa Mkristu sikumapimidwa ndi unyinji wa ntchito zake, koma ndi chikhulupiriro chake ndi ukulu wa chikondi chake. (Yerekezerani ndi Marko 12:41-44.) Kukonda Yehova ndi moyo wanu wonse kumatanthauza kuti mukumtumikira ndi mphamvu yanu yonse​—osati ya wina.​—Mateyu 22:37; Agalatiya 6:4, 5.

Ngati ‘munga wanu m’thupi’ ndi vuto linalake lopsinja maganizo m’moyo monga imfa ya wokondedwa, mverani uphungu wa Baibulowu: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Mkazi wina wachikristu wotchedwa Sylvia anachita zimenezi. Pazaka zochepa zokha, mwamuna wake anafa atakhala naye mu ukwati zaka 50 ndiponso achibale ena asanu ndi anayi​—kuphatikizapo adzukulu ake aŵiri aang’ono. Sylvia akuti: “Popanda Yehova, bwenzi ndikulira mosaletseka. Koma pemphero limanditonthoza kwambiri. Nthaŵi zonse ndimalankhulana ndi Yehova. Ndikudziŵa kuti amandipatsa nyonga yoti ndipirire.”

Kudziŵa kuti “Mulungu wa chitonthozo chonse” angapatse olira mphamvu yoti apirire nkolimbikitsa zedi! (2 Akorinto 1:3; 1 Atesalonika 4:13) Pozindikira zimenezi, tikumvetsa mamalizidwe a Paulo a nkhaniyo. Iye analemba kuti: “Ndisangalala m’maufoko, m’ziwawa, m’zikakamizo, m’mazunzo, m’zipsinjiko, chifukwa cha Kristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.”​—2 Akorinto 12:10.

Kupirira Zophophonya

Tonsefe tinalandira choloŵa cha kupanda ungwiro kuchokera kwa makolo athu oyamba aumunthu. (Aroma 5:12) Choncho, tili pankhondo yolimbana ndi zikhumbo za thupi lochimwa. Zingakhaledi zolefula kwambiri titazindikira kuti makhalidwe ena a “munthu wakale” akali amphamvu kwambiri mwa ife kuposa mmene tinali kuganizira! (Aefeso 4:22-24) Zikatere timamva monga momwe anamvera mtumwi Paulo, amene analemba kuti: “Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.”​—Aroma 7:22, 23.

Apanso, tingagwiritsire ntchito mphamvu yochokera kwa Yehova. Polimbana ndi chifooko chanu, musaleke kupita kwa iye m’pemphero, kupempha mochokera pansi pa mtima kuti akukhululukireni kaya mumfikire kangati konse pavuto limodzimodzilo. Chifukwa cha chisomo chake, Yehova, amene “ayesa mitima” ndipo amene angaone kuti ndinu woona mtima motani, adzakupatsani chikumbumtima choyera. (Miyambo 21:2) Mwa mzimu wake woyera, Yehova angakupatseni nyonga yoti muyambenso kulimbana ndi zofooka za thupi.​—Luka 11:13.

Timafunanso nyonga yochokera kwa Yehova pochita ndi zophophonya za ena. Mwachitsanzo, Mkristu mnzathu angatilankhule “mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.” (Miyambo 12:18) Zimenezi zingatipweteke kwambiri, makamaka ngati amene wachita zimenezo ndi munthu amene timaona kuti ali ndi chidziŵitso. Tingasokonezeke kwambiri. Ena agwiritsira ntchito milandu imeneyi monga zifukwa zosiyira Yehova​—kulakwitsa kwakukulu kuposa zonse!

Komabe, maganizo abwino adzatithandiza kukhala ndi kaonedwe koyenera pa zophophonya za ena. Sitingayembekezere anthu opanda ungwiro kuchita zinthu mwangwiro. “Palibe munthu wosachimwa,” akutikumbutsa motero mwamuna wanzeruyo Solomo. (1 Mafumu 8:46) Arthur, Mkristu wina wodzozedwa amene anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka ngati makumi asanu ndi aŵiri, anati: “Zofooka za atumiki anzathu zimatipatsa mwaŵi wosonyeza kukhulupirika kwathu, kuyesa mtima wathu wachikristu. Ngati tilola zonena kapena zochita za anthu kusokoneza utumiki wathu kwa Yehova, ndiye kuti tikutumikira anthu. Ndi iko komwe, nawonso abale athu amamkonda Yehova. Ngati tiyang’anira ubwino mwa iwo, sitimachedwa kuona kuti si oipa monga tinaganizira.”

Mphamvu Yolalikira

Asanakwere kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”​—Machitidwe 1:8.

Mongadi Yesu ananenera, ntchitoyi ikuchitidwa tsopano ndi Mboni za Yehova m’maiko 233 kuzungulira dziko lonse lapansi. Onse pamodzi, amataya maola oposa mamiliyoni chikwi chimodzi chaka chilichonse kuthandiza ena kudziŵa Yehova. Kuchita ntchito imeneyi sikwapafupi. M’maiko ena ntchito yolalikira Ufumuyi njoletsedwa kapena anaiikira ziletso. Ganizaninso za amene akuichita ntchitoyi​—anthu ofooka, opanda ungwiro, amene aliyense wa iwo ali ndi mavuto ake ndi nkhaŵa zake. Koma ntchito ikupitirizabe, ndipo chifukwa cha zimenezo, pazaka zitatu zapitazi, anthu oposa miliyoni imodzi apatulira moyo wawo kwa Yehova ndipo asonyeza kudzipatulira kwawo mwa ubatizo wa m’madzi. (Mateyu 28:18-20) Ndithudi, ntchitoyi ikuchitika kokha mwa nyonga ya Mulungu. Kudzera mwa mneneri Zekariya, Yehova anati: “Ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi Mzimu wanga.”​—Zekariya 4:6.

Ngati ndinu wofalitsa wa uthenga wabwino, mukukhala ndi mbali​—kaya ioneke ngati yaing’ono motani​—pa chipambano chachikulucho. Mosasamala kanthu za ‘minga’ imene mukupirira, dziŵani kuti Yehova sadzaiŵala “ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Choncho pitirizanibe kudalira Wopereka mphamvuyo kuti akuchirikizeni. Kumbukirani kuti tingapirire kokha ngati tili ndi nyonga ya Yehova; mphamvu yake ikwaniritsidwa pa zofooka zathu.

[Mawu a M’munsi]

a Komabe, popeza “onse anachimwa, napereŵera paulemerero wa Mulungu,” kungokhala chabe paunansi ndi Mulungu kwa munthu aliyense kumasonyeza chifundo chake.​—Aroma 3:23.

[Chithunzi patsamba 26]

Ntchito yolalikira ikuchitika kokha mwa mphamvu ya Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena