Chipulumutso Zimene Chimatanthauza Kwenikweni
‘KODI mwapulumutsidwa?’ Nthaŵi zambiri, amene amafunsa funso limeneli amaganiza kuti iwo anapulumutsidwa chifukwa chakuti ‘analandira Yesu kukhala Mpulumutsi wawo.’ Komanso ena amaganiza kuti pali njira zambiri za kuchipulumutso ndiponso kokha ngati ‘Yesu ali mumtima mwako,’ basi zilibe kanthu kuti kaya chikhulupiriro chako nchotani kapena ndiwe wa tchalitchi chiti.
Baibulo limafotokoza kuti chifuniro cha Mulungu nchakuti “anthu a mtundu uliwonse apulumuke.” (1 Timoteo 2:3, 4, NW) Choncho, onse amene avomereza chipulumutso adzachipeza. Komabe, kodi kupulumutsidwa kumatanthauzanji? Kodi ndi chinthu chimene chimangochitika kwa inu popanda kuyesayesa kulikonse kumbali yanu?
Liwulo “chipulumutso” limatanthauza “kulanditsidwa kungozi kapena chiwonongeko.” Choncho, chipulumutso chenicheni si kungodekha m’maganizo chabe. Chimatanthauza kupulumutsidwa pachiwonongeko cha dongosolo la zinthu loipa lilipoli ndipo pomalizira pake kupulumutsidwa ku imfa yeniyeniyo! Koma, kodi Mulungu adzapulumutsa ndani kwenikweni? Kuti tiyankhe, tiyeni tipende zimene Yesu Kristu anaphunzitsa ponena za nkhani imeneyi. Zotulukapo za kufufuza kwathu zingakudabwitseni.
Chipulumutso—Kodi Chimapezeka m’Zipembedzo Zonse?
Nthaŵi ina yake, Yesu anali kukambitsirana ndi mkazi wachisamariya. Ngakhale kuti sanali Myuda, iye anakhulupirira kotheratu kuti Mesiya “wotchedwa Kristu” adzadza. (Yohane 4:25) Kodi chikhulupiriro chimenecho chinali chokwanira kuti apulumutsidwe? Ayi, popeza kuti Yesu anatsimikizira mkaziyo kuti: “Inu mulambira chimene simuchidziŵa.” Yesu anadziŵa kuti ngati mkaziyu ati apeze chipulumutso, ayenera kusintha njira yake yakulambira. Choncho Yesu anafotokoza kuti: “Koma ikudza nthaŵi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake.”—Yohane 4:22, 23.
Nthaŵi ina pamene Yesu anafotokoza maganizo ake ponena za chipulumutso ndi pamene anali kukambitsirana ndi Afarisi, kagulu kachipembedzo chachiyuda kotchuka. Afarisiwo anayambitsa njira yawoyawo yolambirira ndipo anaganiza kuti Mulungu anaivomereza. Koma tamverani mawu a Yesu kwa Afarisiwo: “Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.”—Mateyu 15:7-9.
Nanga bwanji ponena za zipembedzo zambiri lerolino zimene zimati zimakhulupirira Kristu? Kodi Yesu amavomereza kulambira konse kukhala koyenerera chipulumutso? Sitiyenera kulotera konse pa nkhani imeneyi popeza kuti Yesu ananena zomveka kuti: “Siyense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.”—Mateyu 7:21-23.
Chidziŵitso Cholongosoka Chonena za Yesu Nchofunika Kuti Tipulumuke
Mawu ameneŵa a Yesu angatipangitse kulingalira mofatsa. Iwo akusonyeza kuti anthu ambiri opembedza akulephera ‘kuchita chifuniro cha Atate.’ Nanga munthu angachipeze bwanji chipulumutso chenicheni? Timoteo woyamba 2:3,4 akuyankha motere: “[Mulungu] afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira [nakhale ndi chidziŵitso cholongosoka cha, NW] choonadi.”—Yerekezerani ndi Akolose 1:9, 10.
Chidziŵitso chimenecho nchofunika kwambiri kuti tipulumuke. Pamene mdindo wachiroma anafunsa mtumwi Paulo ndi mnzake Sila, kuti: “Ndichitenji kuti ndipulumuke?” iwo anayankha kuti: “Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.” (Machitidwe 16:30, 31) Kodi zimenezo zinatanthauza kuti mdindoyo ndi apabanja ake anafunikira kungokhala ndi mkhalidwe winawake m’mitima yawo? Ayi, kunena zoona, iwo ‘sakanakhulupirira Ambuye Yesu’ pokhapokha ngati anali ndi chidziŵitso chinachake chonena za Yesu kuti anali yani, anachitanji ndipo anaphunzitsanji.
Mwachitsanzo, Yesu anaphunzitsa za kukhazikitsidwa kwa boma lakumwamba—“Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Iye anakhazikitsanso mapulinsipulo achikristu amakhalidwe abwino. (Mateyu, machaputala 5-7) Iye anafotokoza zimene ophunzira ake anayenera kuchita ponena za nkhani zandale. (Yohane 15:19) Anakhazikitsa programu yophunzitsa ya dziko lonse ndipo analangiza ophunzira ake kutengamo mbali. (Mateyu 24:14; Machitidwe 1:8) Inde, ‘kukhulupirira Yesu’ kunatanthauza kudziŵa zinthu zambiri! Apa nzosadabwitsa konse, kuti Paulo ndi Sila “anamuuza iye [mdindoyo] mawu a Ambuye [“Yehova,” NW] pamodzi ndi onse apabanja pake” okhulupirira atsopano ameneŵa asanabatizidwe.—Machitidwe 16:32,33.
Chidziŵitso Cholongosoka Chonena za Mulungu Chilinso Chofunika
Mbali yofunika ya kukhulupiriradi Yesu imaphatikizapo kulambira Mulungu amene Yesu amamlambira. Yesu anapemphera motere: “Moyo wosatha ndi uwu, kumaloŵetsa kwawo chidziŵitso cha inu, Mulungu yekha woona, ndi cha iye amene munamtuma, Yesu Kristu.”—Yohane 17:3, NW.
Mu utumiki wake wa padziko lapansi, Mwana wa Mulungu nthaŵi zonse anasonya kwa Atate ake osati kwa iye mwini. Iye sananenepo kuti anali Mulungu Wamphamvuyonse. (Yohane 12:49, 50) Mobwerezabwereza, Yesu anafotokoza momveka bwino za malo ake m’makonzedwe a Mulungu mwa kunena kuti iye anali wamng’ono kwa Atate ake. (Luka 22:41, 42; Yohane 5:19) Eetu, Yesu anati: “Atate ali wamkulu ndi Ine.” (Yohane 14:28) Kodi tchalitchi chanu chakuphunzitsani za unansi weniweni wa Mulungu ndi Kristu? Kapena mwasonkhezeredwa kukhulupirira kuti Yesu yemweyo ndiye Mulungu Wamphamvuyonse? Chipulumutso chanu chimadalira pa kukhala kwanu ndi chidziŵitso cholongosoka.
M’Pemphero la Ambuye, Yesu analangiza ophunzira ake kupemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ma Baibulo ambiri abisa dzina la Mulungu, namangoti ndi “Ambuye.” Komatu m’makope oyambirira a “Chipangano Chakale,” dzina la Mulungu linaoneka nthaŵi zoposa 6,000! Nchifukwa chake pa Salmo 83:18 timaŵerenga motere: ‘Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.’ Kodi mwaphunzitsidwa kugwiritsira ntchito dzina la Mulungulo, Yehova? Ngati sichoncho, chipulumutso chanu chili pangozi, popeza kuti “yense amene akaitana pa dzina la Ambuye [“Yehova,” NW] adzapulumutsidwa”!—Machitidwe 2:21; yerekezerani ndi Yoweli 2:32.
Mumzimu ndi m’Choonadi
Yesu Kristu anasonyanso ku Mawu a Mulungu, Baibulo. Pofotokoza malingaliro a Mulungu pa nkhani zina, nthaŵi zonse ananena kuti: “Kwalembedwa.” (Mateyu 4:4,7, 10; 11:10; 21:13) Usiku uja asanafe, Yesu anapempherera ophunzira ake motere: “Patulani iwo m’choonadi; mawu anu ndi choonadi.”—Yohane 17:17.
Kukhala ndi chidziŵitso cha ziphunzitso za Mawu a Mulungu, Baibulo, nkofunikanso kuti tipulumuke. (2 Timoteo 3: 16) Ndi Baibulo lokha limene limayankha mafunso onga awa: Kodi cholinga cha moyo nchiyani? Kodi Mulungu waloleranji kuipa kupitirizabe kwa nthaŵi yaitali chotere? Kodi chimachitika nchiyani kwa munthu atafa? Kodi Mulungu amazunzadi anthu m’helo wamoto? Kodi Mulungu akufuna kuchitanji padziko lapansi?a Munthu sangalambire Mulungu bwino lomwe ngati alibe chidziŵitso cholongosoka cha zinthu zimenezo, popeza kuti Yesu anati: “Olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi.”—Yohane 4:23.
Chikhulupiriro Chimasonkhezera Kuchitapo Kanthu
Chipulumutso chimafuna zinthu zambiri, osati kungokhala ndi chidziŵitso chokha. Chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu chimadzetsa chikhulupiriro mwa munthu wa mtima wolabadira. (Aroma 10:10, 17; Ahebri 11:6) Chikhulupiriro chimenecho chimasonkhezera munthu kuchitapo kanthu. Mwachitsanzo, Baibulo limalangiza kuti: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.”—Machitidwe 3:19.
Zoonadi, kuti tipulumuke, tiyenera kutsatira malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino. Mwa mphamvu yosintha zinthu ya Mawu a Mulungu, zizoloŵezi zakalekale monga kunama ndi chinyengo zimaloŵedwa m’malo ndi kuona mtima ndi choonadi. (Tito 2:10) Makhalidwe oipa, monga mathanyula, chigololo, ndi chisembwere, zimalekedwa ndipo zimaloŵedwa m’malo ndi makhalidwe oyera. (1 Akorinto 6:9-11) Uku si kusiya kwakanthaŵi chabe kochitika chifukwa cha kutengeka maganizo ayi, koma kusintha kwachikhalire kochitika chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu mozama ndi kuwagwiritsira ntchito.—Aefeso 4:22-24.
M’kupita kwa nthaŵi, chikondi chake ndi kuyamikira zimene Mulungu wamchitira, zimasonkhezera munthu woona mtima kuti adzipatulire kotheratu kwa Mulungu, ndi kusonyeza kudzipatulira kwake mwa ubatizo wa m’madzi. (Mateyu 28:19,20; Aroma 12:1) Akristu obatizidwa ali opulumutsidwa pamaso pa Mulungu. (1 Petro 3:21) Pachiwonongeko chikudzachi cha dziko loipa lilipoli, Mulungu adzawapulumutsa kotheratu kupyola chisautso chimenecho.—Chivumbulutso 7:9,14.
Zimene Chipulumutso Chingatanthauze kwa Inu
Pazimene tafotokoza mwachidulezi, taona bwino lomwe kuti chipulumutso si ‘kukhala ndi Ambuye Yesu mumtima mwanu’ basi. Chimatanthauza kumaloŵetsa chidziŵitso cholongosoka chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndi kupanga masinthidwe oyenerera m’moyo wako. Kuchita zimenezi kungaoneke kukhala kovuta, koma Mboni za Yehova zili zokonzeka kukuthandizani pankhani imeneyi. Mwa phunziro la Baibulo lapanyumba, izo zingakuthandizeni kuti muyambe kuyenda m’njira ya kuchipulumutso chenicheni.b
Kuchita zotero kuli kofunika mwamsanga kuposa ndi kale lonse, poona kuyandikira kwa tsiku la Mulungu la chiweruzo likudzalo! Ino ndiyo nthaŵi yolabadira mawu awa a mneneri: “Lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova, funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”—Zefaniya 2:2, 3.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mukufuna mafotokozedwe pankhani zimenezi, chonde onani Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Ngati mungakonde kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, chonde kafikeni ku mpingo wa Mboni za Yehova wa kwanuko. Kapena lemberani ofalitsa magazini ino.
[Bokosi patsamba 6]
Chipulumutso Chimadza mwa . . .
◻ Kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu ndi Yesu.—Yohane 17:3.
◻ Kukhala ndi chikhulupiriro.—Aroma 10:17; Ahebri 11:6.
◻ Kulapa ndi kubwerera.—Machitidwe 3:19; Aefeso 4:22-24.
◻ Kudzipatulira ndi kubatizidwa.—Mateyu 16:24; 28:19,20.
◻ Kupitirizabe kupanga chilengezo chapoyera.—Mateyu 24:14; Aroma 10:10.
[Zithunzi patsamba 7]
Kuphunzira Baibulo, kuchita mogwirizana ndi zimene taphunzira, kudzipatulira, ndi kubatizidwa zili masitepe otsogolera kuchipulumutso