Olengeza Ufumu Akusimba
Kugonjetsa Zothetsa Nzeru “m’Dziko la Zochitika Zosayembekezeka”
MTUMWI Paulo anafunsa Akristu a m’zaka za zana loyamba ku Korinto kuti: “Ngati lipenga lipereka mawu osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo? Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mawu omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa.”—1 Akorinto 14:8, 9.
Ku Papua New Guinea, nthaŵi zina kotchedwanso kuti Dziko la Zosayembekezeka, Mboni za Yehova zimakumana ndi zopinga zogwetsa mphwayi polengeza uthenga womveka bwino wa m’Baibulo. Zimalalikira kwa anthu olankhula zilankhulo 700 zosiyanasiyana ndiponso okhala ndi miyambo yambiri yosiyanasiyana. Komanso Mboni zimalimbana ndi malo a mapirimapiri, kusoŵeka kwa misewu, ndi kuwonjezeka kwa upandu. Kuwonjezera pa zovuta zonsezi, palinso chitsutso chochokera kwa magulu ena achipembedzo, ndiponso, nthaŵi zina, ngakhale kwa aziphunzitsi a m’masukulu.
Komabe, malangizo abwino auzimu ndi kuwonjezereka kwa laibulale ya mabuku othandizira kuphunzira Baibulo m’zilankhulo za komweko kukutheketsa Mboni kulengeza uthenga wabwino monga lipenga lozindikirika. Kaŵirikaŵiri pamakhala zotulukapo zabwino, monga momwe malipoti otsatirawa akusonyezera:
• Atatsegulira sukulu chaka chatsopano, mphunzitsi anafuna kudziŵa kuti nchifukwa ninji ana a Mboni za Yehova sachitira suluti mbendera kapenanso kuimba nyimbo ya fuko. Funso lakelo analipereka kwa Maiola, wophunzira wazaka za kubadwa 13 yemwe ndi Mboni yobatizidwa. Maiola analongosola momveka bwino mogwiritsira ntchito Malemba. Mphunzitsiyo anavomera yankho lakelo popeza linali lochokera m’Baibulo. Aphunzitsi ena onse a pasukulupo nawonso anauzidwa za yankholo.
Pambuyo pake, pamene ophunzirawo anauzidwa kulemba chimangirizo, Maiola anasankha nkhani yonena za Utatu. Chimangirizo chake chinapeza mamalikisi ambiri m’kalasilo, ndipo mphunzitsiyo anamfunsa kumene anapeza mfundozo. Anamuonetsa buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi lachingelezi. Mphunzitsiyo anasonyeza bukulo kwa kalasi yonseyo, ndipo ambiri anafuna buku lawolawo. Tsiku lotsatira, Maiola anagaŵira mabuku 14 ndi magazini 7 kwa anzake apasukulu, ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo kwa atatu a iwo. Cholinga cha Maiola ndi kudzakhala mtumiki wa nthaŵi zonse.
• Kagulu ka Mboni za Yehova komwe kali kutali kwambiri ndi mudzi wa m’mphepete mwa nyanja kufupi ndi Port Moresby kakhala kakukumana ndi chitsutso kuyambira kuchiyambi kwa ma 1970. Komabe, posachedwa, analandira thandizo ku magwero osayembekezeka. Bishopu wa United Church kumeneko, yemwe kwawo nkomweko ku Papua New Guinea yemwe anaphunzira ku maiko a kutsidya kwa nyanja, analola omvetsera m’tchalitchi kufunsa mafunso tsiku lina. Munthu wina anafunsa kuti: “M’mudzi mwathu muli zipembedzo ziŵiri—United Church ndi Mboni za Yehova. Kodi tizichita chiyani Mboni zikabwera pakhomo pathu?” Atakhala chete kwa nthaŵi yaitali, bishopuyo anayankha kuti: “Mudziŵa, sindikudziŵa choti ndikuuzeni. Posachedwa, Mboni ziŵiri zachinyamata zinabwera pakhomo panga. Zinandifunsa funso, koma ndimaphunziro anga a ku yunivesite onseŵa, sindinadziŵe yankho. Koma mosavuta anandipatsa yankho kuchokera m’Baibulo. Choncho sindikuuzani choti muzichita—ndisiya zimenezi m’manja mwanu. Simuyenera kumvetsera ngati simufuna kutero, koma osamachita nawo chiwawa.”
Woimira Watch Tower Society woyendayenda amene pambuyo pake anachezera gulu la Mbonili anapereka lipoti lakuti: “Pafupifupi aliyense m’mudzimo amamvetsera Mboni zikapita kolalikira. Ena amaziitanira m’nyumba zawo. Ndi paradaiso wa ulaliki tsopano.”