Madalitso a Utumiki Waupainiya
“Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—MIYAMBO 10:22.
1, 2. (a) Kodi mpainiya wina anafotokoza motani malingaliro ake ponena za utumiki wa nthaŵi zonse? (b) Nchifukwa ninji apainiya ali ndi mwaŵi wopeza chimwemwe chokulirapo popanga ophunzira?
“KODI pangakhalenso chisangalalo china choposa kuona winawake amene mumaphunzira naye akukhala wotamanda Yehova wokangalika? Nkosangalatsa ndi kolimbitsa chikhulupiriro kuona mmene mphamvu ya Mawu a Mulungu imasonkhezerera anthu kusintha miyoyo yawo kuti akondweretse Yehova.” Analemba motero mpainiya wa ku Canada amene wakhala mu utumiki wa nthaŵi zonse kwa zaka zoposa 32. Ponena za utumiki wake waupainiya, iye akuti: “Sindiganizanso zochita chinthu china chilichonse. Zoonadi sindiganiza kuti palinso chinthu china chimene chingandipatse chimwemwe chotere.”
2 Kodi inuyo mukukhulupirira kuti mungapeze chimwemwe chachikulu mwa kuthandiza winawake kupeza njira ya ku moyo? Ndithudi, si apainiya okha amene amapeza chimwemwe chimenechi. Atumiki onse a Yehova ali pantchito ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse,’ ndipo amayesetsa kuchita zimenezo. (Mateyu 28:19) Komabe, popeza kuti apainiya amathera maola ochuluka mu utumiki wakumunda, iwo kaŵirikaŵiri ali ndi mwaŵi wopeza chimwemwe chokulirapo popanga ophunzira. Komatu upainiya ulinso ndi madalitso ena. Tachezani ndi apainiya, ndipo adzakuuzani kuti kuchita upainiya ndi njira yabwino kwambiri yopezera ‘madalitso a Yehova amene alemeretsa.’—Miyambo 10:22.
3. Kodi chingatisonkhezere nchiyani pamene tipitirizabe kutumikira Yehova?
3 Posachedwapa, apainiya a kumbali zosiyanasiyana za dziko lapansi anafunsidwa kuti afotokoze za madalitso amene apeza mu utumiki wa nthaŵi zonse. Tiyeni tione zimene iwo ananena. Komabe, musade nkhaŵa ngati mulephera kuchita utumiki wanu mokwanira chifukwa cha matenda, ukalamba, kapena mikhalidwe ina. Kumbukirani, chinthu chofunika ndicho kutumikira Yehova ndi mtima wonse, mulimonse mmene mungathere. Komabe, kumva ndemanga za apainiya ena kudzawonjezera chilakolako chanu chofuna kuchita nawo ntchito yopindulitsa imeneyi ngati kungatheke.
Chikhutiro ndi Chimwemwe Chenicheni
4, 5. (a) Nchifukwa ninji kugaŵana uthenga wabwino ndi ena kuli ntchito yopindulitsa? (b) Kodi apainiya amakuona motani kuchita utumiki wa nthaŵi zonse?
4 “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira,” anatero Yesu. (Machitidwe 20:35) Zoonadi, kupatsa mooloŵa manja kuli ndi madalitso ake. (Miyambo 11:25) Izi zilidi choncho makamaka pamene tigaŵana uthenga wabwino ndi ena. Ndithudi, kodi ndi mphatso yabwino iti imene tingapatse munthu mnzathu yoposa kumthandiza kupeza chidziŵitso chonena za Mulungu, chimene chimatsogolera ku moyo wosatha?—Yohane 17:3.
5 Nzosadabwitsa konse kumva amene akuchita nawo utumiki wa nthaŵi zonse akufotokoza nthaŵi zambiri za chimwemwe ndi chikhutiro chenicheni chimene amapeza mu utumiki wawo. “Ndikudziŵa kuti palibenso ntchito ina imene ikanandipatsa chikhutiro chimene ndapeza mwa kugaŵana choonadi ndi ena,” akutero mpainiya wa ku Britain wazaka 64 zakubadwa. Mkazi wamasiye wa ku Zaire anafotokoza mmene upainiya wamthandizira kuti: “Utumiki waupainiya unali chitonthozo chenicheni kwa ine pamene mwamuna wanga wokondedwa anamwalira. Nthaŵi zonse pamene ndipita ku utumiki kukathandiza ena, ndimaiŵala za mavuto ameneŵa. Ndimakhulupirira malonjezo a Yehova ndipo kwenikweni ndimasinkhasinkha za mmene ndingathandizire amene ndikuphunzira nawo kusintha miyoyo yawo. Usiku uliwonse, ndimakhala ndi tulo tabwino, ndipo mtima wanga umadzaza ndi chimwemwe.”
6. Kodi ndi chimwemwe chapadera chiti chimene apainiya ena akhala nacho?
6 Ena amene akhala akuchita upainiya kwa zaka makumi ambiri akhala ndi chimwemwe chapadera cha kutumikira m’madera akumidzi, kukhazikitsa mipingo, imene pomalizira inakula mpaka kukhala madera. Mwachitsanzo, ku Abashiri, Hokkaido (chisumbu cha kumpoto kwenikweni kwa Japan), kuli mlongo amene wakhala mpainiya kwa zaka 33. Iye akukumbukira kuti pamsonkhano wadera umene iye anapezekapo kwa nthaŵi yoyamba—msonkhano wa Hokkaido yense—panasonkhana anthu 70 okha. Nanga lero? Pali madera 12 pachisumbu chimenecho, ndi ofalitsa oposa 12,000. Tangolingalirani za mmene mtima wake umadzazidwira ndi chimwemwe pamene iye apita kumisonkhano yadera ndi yachigawo pamodzi ndi gulu la olengeza Ufumu anzake pachisumbu chimenecho!
7, 8. Kodi apainiya ambiri amene agwira ntchito imeneyi kwa nthaŵi yaitali akhala ndi chimwemwe chotani?
7 Apainiya ena amene agwira ntchitoyi kwa nthaŵi yaitali akhala ndi chimwemwe cha kuona ophunzira Baibulo akubatizidwa ndipo kenaka kukalimira mwaŵi wokulirapo wa utumiki. Ku Japan mlongo wina amene watumikira m’magawo osiyanasiyana asanu ndi anayi kuyambira mu 1957 akukumbukira kuti anagaŵira magazini ya Galamukani! kwa msungwana wogwira ntchito m’banki. Patangopita miyezi isanu ndi inayi msungwanayo anabatizidwa. Kenaka anakwatiwa, ndipo iyeyo ndi mwamuna wake anakhala apainiya apadera. Anasangalala chotani nanga mlongo mpainiya ameneyu pamene, m’gawo lake lachitatu, mpingo wake unachezeredwa ndi woyang’anira dera watsopano ndi mkazi wake—amene kale anali wophunzira Baibulo wake!
8 Nzosadabwitsa kuti amene asankha utumiki waupainiya kukhala ntchito yawo amauona kukhala “mwaŵi wamtengo wapatali koposa wokondeka,” mongadi momwe wina amene wakhala mpainiya kwa zaka 22 ananenera!
Umboni wa Chisamaliro cha Yehova
9. Monga Mpatsi Wamkulu, kodi Yehova akulonjeza chiyani kwa atumiki ake, ndipo zimenezi zikutanthauzanji kwa ife?
9 Yehova, Mpatsi Wamkulu, akulonjeza kuchirikiza atumiki ake, kuwasamalira mwauzimu ndiponso mwakuthupi. Mfumu Davide yakaleyo inanena bwino kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” (Salmo 37:25) Ndithudi, lonjezo la Mulungu limeneli silikutanthauza kuti tisiye udindo wathu wosamalira mabanja athu mwakuthupi, komanso silikutipatsa chilolezo chakuti tizingoyembekezera kupatsidwa mooloŵa manja ndi abale athu achikristu. (1 Atesalonika 4:11, 12; 1 Timoteo 5:8) Komabe, ngati mofunitsitsa tisiya zinthu zina m’moyo wathu ncholinga chakuti titumikire Yehova mokwanira, iye sadzatisiya konse.—Mateyu 6:33.
10, 11. Malinga nzimene iwo aona, kodi apainiya ambiri akudziŵa chiyani ponena za mmene Yehova amapatsira?
10 Apainiya padziko lonse adzionera okha kuti Yehova amasamala amene amadziika m’manja mwake. Talingalirani za mwamuna wina ndi mkazi wake, apainiya amene anasamukira kutauni yaing’ono kumene kunali kusoŵa kwakukulu kwa olalika Ufumu. Patapita miyezi yoŵerengeka, ntchito yolembedwa inawasoŵa, ndipo ndalama zinawathera. Kenaka analandira chikalata chowauza kuti ayenera kulipira inshuwalansi ya galimoto yokwanira $81. “Tinalibe ndalama zilizonse,” akufotokoza motero mbaleyo. “Tinapemphera zolimba usiku umenewo.” Tsiku lotsatira, analandira khadi kuchokera ku banja lina limenenso linali pamavuto azachuma. Banja limenelo linalandira ndalama za msonkho zimene zinabwerera chifukwa chakuti zinachulukitsa, khadilo linafotokoza motero, ndipo popeza kuti zinawachulukira, iwo anafuna kuti agaŵireko apainiya okwatiranawo. Mkati mwake munali cheke cha $81! “Tsiku limenelo sindidzaliiwala—ndinali ndi chimwemwe chosaneneka!” akutero mbale mpainiyayo. “Tinaliyamikira kwambiri banja limeneli chifukwa cha kuoloŵa manja kwawo.” Yehova amayamikiranso kukoma mtima kotero, kumene kumasonyezadi mzimu wopatsa mooloŵa manja umene iye amalimbikitsa atumiki ake kukhala nawo.—Miyambo 19:17; Ahebri 13:16.
11 Apainiya ambiri angafotokoze zokumana nazo zofananazo. Afunseni, ndipo iwo adzakuuzani kuti “sanasiyidwe.” Pokumbukira utumiki wake wanthaŵi zonse wochitidwa kwa zaka zoposa 55, mpainiya wazaka 72 zakubadwa akunena kuti, “Yehova sanandigwiritse mwala.”—Ahebri 13:5, 6.
“Njira Yabwino Koposa Yoyandikirira kwa Yehova”
12. Nchifukwa ninji ntchito yolengeza uthenga wabwino ili mwaŵi waukulu?
12 Pempho la Yehova lakuti tilengeze uthenga wabwino wa Ufumu wake limatipatsa mwaŵi. Iye amationa—ngakhale kuti ndife anthu opanda ungwiro—ngati “antchito anzake” m’ntchito imeneyi yopulumutsa miyoyo. (1 Akorinto 3:9; 1 Timoteo 4:16) Pamene tilalikira kwa ena za Ufumu wa Mulungu, pamene tilengeza za mapeto a kuipa, pamene tifotokozera anthu za chikondi chake chosaneneka potipatsa dipo, pamene titsegula Mawu ake amoyo ndi kuphunzitsa anthu oona mtima zamkati mwake za mtengo wapatali, mwachibadwa timayandikana ndi Mlengi wathu, Yehova.—Salmo 145:11; Yohane 3:16; Ahebri 4:12.
13. Kodi ena asimba zotani ponena za mmene utumiki wawo waupainiya umakhudzira unansi wawo ndi Yehova?
13 Apainiya amathera nthaŵi yaitali mwezi uliwonse kuphunzira ndi kuphunzitsa za Yehova. Kodi amamva bwanji poona kuti zimenezi zimakhudza unansi wawo ndi Mulungu? “Kuchita upainiya ndi njira yabwino koposa yoyandikirira kwa Yehova,” akuyankha motero mkulu wina wa ku France amene wakhala mpainiya kwa zaka zoposa khumi. Mpainiya wina wa m’dzikolo, amene watha zaka 18 mu utumiki wa nthaŵi zonse, akuti: “Utumiki waupainiya umatithandiza ‘kulaŵa ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino,’ tsiku ndi tsiku kupanga unansi wolimba ndi Mlengi wathu.” (Salmo 34:8) Mlongo wina ku Britain amene wakhala mpainiya kwa zaka 30 akunena zofananazo. “Kuyembekeza mzimu wa Yehova kaamba ka chitsogozo mu utumiki wanga kumandiyandikizitsa kwa iye,” akutero iye. “Ndikutsimikiza kuti mzimu wa Yehova nthaŵi zambiri wanditsogoleradi ku nyumba ina panthaŵi yake.”—Yerekezerani ndi Machitidwe 16:6-10.
14. Kodi apainiya amapindula motani mwa kugwiritsira ntchito Baibulo ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo tsiku lililonse pophunzitsa ena?
14 Apainiya ambiri aona kuti kugwiritsira ntchito Baibulo ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo tsiku lililonse pofotokoza ndi kuphunzitsa za choonadi cha Malemba kumawathandiza kukula m’chidziŵitso cha Mawu a Mulungu. Mbale wazaka 85 zakubadwa ku Spain amene wakhala mpainiya kwa zaka 31 akunena kuti: “Upainiya wandithandiza kupeza chidziŵitso chozama cha Baibulo, chidziŵitso chimene ndagwiritsira ntchito kuthandiza anthu ambiri kudziŵa Yehova ndi zifuno zake.” Mlongo wina wa ku Britain amene wakhala akuchita upainiya kwa zaka 23 akuti: “Utumiki wa nthaŵi zonse wandithandiza kukulitsa chilakolako chachikulu cha chakudya chauzimu.” Kufotokozera anthu ena “chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu” kungalimbitse chidaliro chanu pa chikhulupiriro chimene mwachigwiritsitsa ndi mtima wonse. (1 Petro 3:15) Mpainiya wina wa ku Australia akunena kuti: “Upainiya umalimbitsa chikhulupiriro changa pamene ndiphunzitsa ena.”
15. Kodi ambiri achita chiyani mofunitsitsa kuti ayambe utumiki waupainiya ndi kupitirizabe kutumikira, ndipo nchifukwa ninji?
15 Zoonadi, apainiya ameneŵa ali ndi chikhutiro chakuti asankha utumiki umene umadzetsa madalitso osaŵerengeka ochokera kwa Yehova. Nchifukwa chake ambiri asintha miyoyo yawo mofunitsitsa, ngakhale kusiya ntchito yolembedwa ndiponso chuma chakuthupi, kuti ayambe utumiki waupainiya ndi kupitirizabe kutumikira!—Miyambo 28:20.
Kodi Mtima Wanu Ukufunitsitsa Kuchita Zowonjezereka?
16, 17. (a) Ngati mukufuna kudziŵa kuti kaya mungathe kuchita upainiya, kodi mungachitenji? (b) Kodi ena amalingaliranji pamene alephera kuchita upainiya?
16 Mutasinkhasinkha za zimene apainiya amanena ponena za madalitso a utumiki waupainiya, mwinamwake mungafune kudziŵa ngati inuyo mungakwanitse kutero. Ngati zili choncho, bwanji osafunsa mpainiya amene wapindula ndi utumiki wa nthaŵi zonse? Mungapezenso thandizo mutafunsa mmodzi wa akulu a mumpingo, munthu amene amakudziŵani bwino—thanzi lanu, zofooka zanu, ndiponso udindo wanu wapabanja. (Miyambo 15:22) Ndemanga zoonadi za anthu ena zingakuthandizeni kupenda bwino ngati inuyo mungathe kuchita upainiya. (Yerekezerani ndi Luka 14:28.) Ngati muli ndi mwaŵi wochita upainiya, mudzapezadi madalitso ochuluka.—Malaki 3:10.
17 Komabe, bwanji nanga za ofalitsa Ufumu ambiri okhulupirika amene sangathe kuchita upainiya, ngakhale kuti angafune kuchita zambiri mu utumiki? Mwachitsanzo, talingalirani za maganizo a mlongo wina wachikristu amene akulera ana ake anayi movutikira. “Ndimamva chisoni,” iye akutero, “chifukwa chakuti kale ndinali mpainiya wokhazikika, koma lero, chifukwa cha mavuto anga, ndikulephera kupita ku utumiki wakumunda monga momwe ndinali kuchitira.” Mlongoyu amawakonda kwambiri ana ake ndipo amafuna kuwasamalira. Panthaŵi imodzimodziyo, amafunitsitsa kuchita zowonjezereka m’ntchito yolalikira. “Ndimaukonda utumiki,” iye akufotokoza motero. Akristu enanso odzipereka amene kukonda kwawo Mulungu kumawasonkhezera kufuna kutumikira Yehova ‘ndi mtima wawo wonse’ alinso ndi malingaliro ofananawo.—Salmo 86:12.
18. (a) Kodi Yehova amafunanji kwa ife? (b) Nchifukwa ninji sitiyenera kukhumudwa ngati tilephera kuchita zimene timafuna chifukwa cha mavuto ena?
18 Kumbukirani kuti chimene Yehova amafuna kwa ife ndicho utumiki wa mtima wonse. Ungachitidwe pamlingo wosiyanasiyana pakati pa wina ndi mnzake. Ena amatha kusintha zochita zawo kuti atumikire monga apainiya okhazikika. Enanso ambiri alembetsa monga apainiya othandiza mwa apa ndi apo kapena mosalekeza, akumathera maola 60 mwezi uliwonse mu utumiki. Komabe, anthu a Yehova ambiri amadzipereka pantchito yolalikira ndi kuphunzitsa ndi mtima wonse monga ofalitsa a mumpingo. Choncho ngati inuyo mukulepheradi chifukwa cha matenda, ukalamba, udindo wapabanja, kapena mavuto ena, musakhumudwe. Malinga ngati mukuchita zonse zomwe mungathe, utumiki wanu amauyamikira Mulungu, mongadi momwe amayamikirira amene akuchita utumiki wa nthaŵi zonse!
Onse Angasonyeze Mzimu Waupainiya
19. Kodi mzimu waupainiya nchiyani?
19 Ngakhale kuti mungalephere kulembetsa monga mpainiya, mungasonyezebe mzimu waupainiya. Kodi mzimu waupainiya nchiyani? Utumiki Wathu Waufumu wa July 1988 unati: “Ungalongosoledwe monga kukhala ndi mkhalidwe weniweni kulinga ku lamulo la kulalikira ndi kupanga ophunzira, kukhala wotanganitsidwa mokwanira kusonyeza chikondi ndi kudera nkhaŵa kaamba ka anthu, kukhala [wodzimana], kupeza chisangalalo m’kutsatira Ambuye mwathithithi, ndi kukhala ndi chisangalalo m’zinthu zauzimu, osati zakuthupi.” Kodi mungausonyeze bwanji mzimu waupainiya?
20. Kodi makolo angasonyeze motani mzimu waupainiya?
20 Ngati ndinu kholo la ana ang’onoang’ono, mungawalimbikitse ndi mtima wonse kuti ayenera kudzakhala apainiya. Kuyamikira kwanu utumiki kungawachititse kupanga kutumikira Yehova kukhala chinthu chofunika koposa m’miyoyo yawo. Mungaitanire apainiya ndi oyang’anira oyendayenda pamodzi ndi akazi awo kunyumba kwanu kuti ana anu aphunzire pazitsanzo za anthu amene apeza chimwemwe mu utumiki wa nthaŵi zonse. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:7.) Ngakhale m’mabanja osiyana zipembedzo, makolo okhulupirira, kupyolera m’mawu ndi chitsanzo chabwino, angathandize ana awo kukhala ndi cholinga chodzachita utumiki wa nthaŵi zonse m’moyo wawo.—2 Timoteo 1:5; 3:15.
21. (a) Kodi tonsefe tingawathandize motani amene akuchita upainiya? (b) Kodi akulu angachitenji kuti alimbikitse apainiya?
21 Mumpingo, tonsefe tingathandize ndi mtima wonse anthu amene ali ndi mwaŵi wochita upainiya. Mwachitsanzo, kodi mungayesetse kukagwira ntchito ndi mpainiya mu utumiki, makamaka nthaŵi zimene mpainiyayo mwina akugwira ntchitoyo yekha? Mungathedi kuona kuti padzakhala ‘kutonthozana wina ndi mnzake.’ (Aroma 1:11, 12) Ngati ndinu mkulu, mungachitenso zochuluka kuti mulimbikitse apainiya. Pamene bungwe la akulu likumana, nthaŵi ndi nthaŵi ayenera kukambitsirana za zosoŵa za apainiya. Pamene mpainiya akubwerera mmbuyo kapena pamene akulimbana ndi mavuto ena, musafulumire kupereka malingaliro akuti iye asiye kuchita upainiya. Ngakhale kuti nthaŵi zina kupereka malingaliro otero kungakhale kofunika, musaiŵale kuti upainiya ndi mwaŵi wamtengo wapatali umene mtumiki wanthaŵi zonse angauyamikire kwambiri. Chilimbikitso pamodzi ndi uphungu wogwira ntchito kapena chithandizo mwina ndizo zokha zimene zingafunike. Ofesi yanthambi ya Sosaite ku Spain ikulemba kuti: “Pamene akulu alimbikitsa kuchita upainiya, kuthandiza apainiya mu utumiki wakumunda, ndi kuwalimbikitsa nthaŵi ndi nthaŵi, apainiya amakhala ndi chimwemwe chochuluka, amadziona kuti ndi ofunika, ndipo amafuna kupitirizabe kuchita upainiya mosasamala kanthu za zovuta zina.”
22. M’nthaŵi yovuta ino ya mbiri ya anthu, kodi tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chiyani?
22 Tikukhala m’nthaŵi yovuta ya mbiri ya anthu. Yehova watipatsa ntchito yopulumutsa miyoyo yoti tichite. (Aroma 10:13, 14) Kaya tikuchita kapena sitikuchita nawo ntchito imeneyi nthaŵi zonse monga apainiya, tiyeni tisonyeze mzimu waupainiya. Tiyeni tichite changu ndipo tikhale ndi mzimu wodzimana. Tiyeni titsimikizire kuti tikupatsa Yehova zimene iyeyo akufuna kwa ife—utumiki wa mtima wonse. Ndiponso tikumbukire kuti pamene tipereka mmene tingathere, kaya zikufanana ndi timakobiri ta mkazi wamasiye kapena mafuta a mtengo wapatali a Mariya, utumiki wathu ukhale wa mtima wonse, ndipotu Yehova amayamikira utumiki wathu wa mtima wonse!
Kodi Mukukumbukira?
◻ Nchifukwa ninji utumiki wa nthaŵi zonse umadzetsa chikhutiro ndiponso chimwemwe?
◻ Malinga nzimene aona, kodi apainiya ambiri akudziŵa chiyani ponena za mmene Yehova amasamalirira atumiki ake?
◻ Kodi apainiya amaganiza kuti utumiki wawo wakhudza motani unansi wawo ndi Yehova?
◻ Kodi mungausonyeze motani mzimu waupainiya?
[Chithunzi patsamba 23]
Apainiya amapeza chimwemwe chachikulu popanga ophunzira
[Chithunzi patsamba 23]
Ana anu angapindule mwa kuyanjana ndi olengeza Ufumu a nthaŵi zonse
[Chithunzi patsamba 23]
Akulu angalimbikitse apainiya mu utumiki wakumunda