Kulimbitsa Chikhulupiriro Chathu m’Mawu a Mulungu
BAIBULO laŵerengedwa ndi anthu ambiri kuposa buku lina lililonse. Koma kodi ndi angati amene asonyeza chikhulupiriro mu uthenga wake? Baibulo lenilenilo limafotokoza kuti “si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Ndithudi, chikhulupiriro sitimabadwa nacho. Tiyenera kuchilandira. Ngakhale awo amene ali ndi chikhulupiriro sayenera kuchitenga mopepuka. Chikhulupiriro chikhoza kunyonyosoka ndi kufa. Chotero, tiyenera kuyesayesa kuti tikhalebe “olama m’chikhulupiriro.”—Tito 2:2.
Choncho, pachifukwa chabwino, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linasankha kuti misonkhano yawo yachigawo ya 1997/98 ikhale ndi mutu wakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu.” Chotero Mboni mamiliyoni ambiri akhala ndi mwaŵi wa kusonkhana pamodzi kuti alimbitse chikhulupiriro chawo m’Mawu a Mulungu.
Mawu a Mulungu ndi Choonadi—Maziko a Chikhulupiriro Chathu
Umenewu ndiwo unali mutu wa tsiku loyamba la msonkhanowu. Linayamba ndi chithokozo kwa onse opezekapo. Kupezeka kwawo pamsonkhanopo kunali umboni wakuti amalemekeza Baibulo. Komabe, mafunso awa ochititsa chidwi okhudza mtundu wa chikhulupiriro chathu anafunsidwa: ‘Kodi timatha kufotokoza bwino zikhulupiriro zathu titafunsidwa, mwakugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu monga umboni wake? Kodi timayamikira chakudya chauzimu, popanda kutenga Baibulo, misonkhano ya mpingo, ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo mopepuka? Kodi tikukulitsa chikondi chathu, chidziŵitso cholongosoka, ndi kuzindikira?’ Wokamba nkhaniyo analimbikitsa onse kumvetsera mosamalitsa, nanena kuti “Msonkhano Wachigawo uno wa ‘Kukhulupirira Mawu a Mulungu’ wakonzedwa kuti utithandize kupenda ndi kufufuza ukulu ndi mtundu wa chikhulupiriro umene aliyense wa ife ali nawo.”
Nkhani yaikulu inali ndi mutu wakuti “Kuyenda mwa Chikhulupiriro, Osati mwa Chionekedwe.” (2 Akorinto 5:7) “Chikhulupiriro cha aja amene amakhala Mboni za Yehova sichili chongokhulupirira mosadziŵa,” anatero mlankhuli. Ndipo zimenezi nzoonadi. Chikhulupiriro chenicheni si chakhungu. Chimazikidwa pa zinthu zenizeni. Ahebri 11:1 amati: “Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” Mlankhuliyo anati: “Kuti tiyendedi mwa chikhulupiriro, tifunikira chikhulupiriro chimene chili ndi maziko olimba.” Chifukwa chakuti timayenda mwa chikhulupiriro, osati mwa chionekedwe, sitimafunikira kudziŵa tsatanetsatane wa mmene Yehova adzakwaniritsira mbali iliyonse ya chifuno chake ndi nthaŵi imene adzazikwaniritsa. Zimene tikudziŵa kale ponena za iye zimatipangitsa kudalira mphamvu yake kotheratu kuti idzakwaniritsa malonjezo ake mwachikondi ndiponso mwachilungamo.
Nkhani yakuti “Akristu Achinyamata—Mbali Yofunika ya Mpingo” inakumbutsa achinyamata za mmene iwo alili amtengo wapatali kwa Yehova. Iwo analimbikitsidwa kukula mwauzimu mwa kulondola zolinga monga kuŵerenga Baibulo lonse ndi kufitsa ziyeneretso kuti adzipatulire ndi kubatizidwa. Kulondola maphunziro owonjezera ndi nkhani yaumwini imene ili chosankha cha makolo a munthu, koma ngati asankha kulondola maphunzirowo, nthaŵi zonse cholinga chake chiyenera kukhala kukonzekera kutumikira Mulungu mogwira mtima kwambiri. Maphunziro akudziko angakhale ndi chifuno chopindulitsa pamene ‘titsimikizira zinthu zofunika kwambiri’ zogwirizana ndi chikhulupiriro chathu.—Afilipi 1:9, 10, NW.
Kenako panatsatira nkhani yosiyirana yambali zitatu yamutu wakuti “Kodi Mumatsatira Miyezo ya Yani?” Kukhulupirira Mawu a Mulungu kumatisonkhezera kutsatira mosamalitsa miyezo ya Baibulo. Akristu amamvera malamulo ndi mapulinsipulo a Yehova. Mwachitsanzo, Malemba amatilangiza kuti tisagwiritsire ntchito kalankhulidwe konyansa ndi kotukwana. (Aefeso 4:31, 32) Mlankhuli anafunsa kuti: “Ngati akuputani kapena kukukwiyitsani, kodi mumamzazira mnzanu wa muukwati kapena ana anu?” Ndithudi chimenecho si Chikristu. Mulungu alinso ndi miyezo yokhudza kaonekedwe kathu. Akristu ayenera kudziveka “ndi chovala choyenera, ndi manyazi.” (1 Timoteo 2:9, 10) Liwu lakuti “manyazi” limapereka lingaliro la kudzilemekeza, kukhala wolemekezeka, kuganiza bwino, ndi kusapambanitsa. Chikondi cha pa ena ndicho chimatisonkhezera ndipo timatsogozedwa ndi mapulinsipulo a Baibulo ndi kudziŵa chimene chili choyenera.
Mbali ziŵiri zomaliza zotsatizanazo zinaphatikizapo kupenda vesi lililonse la Ahebri 3:7-15 ndi 4:1-16. Ndime za Baibulo zimenezi zimatichenjeza za ngozi ya kukhala ‘woumitsidwa ndi chenjerero la uchimo.’ (Ahebri 3:13) Kodi tingapambane motani polimbana ndi uchimo? Yehova amatithandiza kudzera mwa Mawu ake. Ndithudi, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.”—Ahebri 4:12.
Nkhani yomaliza patsiku loyamba la msonkhanowu inali yakuti “Buku la Anthu Onse.” Iyo inafotokoza za kudalirika, kulongosoka ndi ubwino wa Baibulo. Kunali kosangalatsa chotani nanga kumva mlankhuli akulengeza kutulutsidwa kwa brosha latsopano lamasamba 32 lamutu wakuti Buku la Anthu Onse! Chofalitsa chatsopano chimenechi chinakonzedwera makamaka anthu amene, ngakhale kuti ngophunzira, iwo sadziŵa zambiri ponena za Baibulo. Nkhaniyo inamaliza ndi mawu akuti: “Anthu ayenera kudzifufuzira okha Mawu a Mulungu. Tili ndi chidaliro chakuti akafufuza Baibulo lenilenilo, adzafika pozindikira kuti buku lapadera limeneli, Baibulo, lilidi buku la anthu onse!”
Tsanzirani “Wokwaniritsa Chikhulupiriro Chathu”
Mutu umenewu wa tsiku lachiŵiri la msonkhano unafotokoza za Yesu Kristu, “wokwaniritsa chikhulupiriro chathu.” Tiyenera ‘kulondola mapazi ake.’ (Ahebri 12:1, 2, NW; 1 Petro 2:21) Ambiri m’Dziko Lachikristu amauzidwa kuti: ‘Khulupirira mwa Ambuye Yesu, ndipo udzapulumutsidwa!’ Koma kodi chikhulupiriro chimangofuna zokhazo? Baibulo limanena kuti “chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.” (Yakobo 2:26) Choncho, kuwonjezera pa kukhulupirira mwa Yesu, tiyenera kuchita ntchito zimene iye anachita, makamaka mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.
Programu ya mmaŵa inakhudza kwambiri ntchito yolalikira. Monga Paulo, tiyenera kukhala ofunitsitsa kulengeza uthenga wabwino wa chipulumutso. (Aroma 1:14-16) Yesu analalikira kwa anthu kulikonse. Ngakhale kuti utumiki wathu wa kunyumba ndi nyumba wanthaŵi zonse ukukhala ndi zotsatirapo zabwino, anthu ambiri sitimawapeza panyumba zawo titafikapo. (Machitidwe 20:20) Ambiri amakhala ali kusukulu, kuntchito, kokagula zinthu, kapena pamaulendo. Choncho, tiyenera kulalikiranso m’malo a anthu onse ndi kulikonse kumene anthu angapezeke.
Nkhani yakuti “Zikani Mizu ndi Kukhazikika m’Choonadi” inatikumbutsa za chiŵerengero chachikulu cha ophunzira atsopano amene akubatizidwa—avareji ya ophunzira oposa 1,000 tsiku lililonse! Nkofunika kwambiri kuti atsopano ameneŵa azike mizu mozama ndi kukhazikika m’chikhulupiriro. (Akolose 2:6, 7) Mlankhuliyo anafotokoza kuti mizu yeniyeni imatsopa madzi ndi zakudya ndipo panthaŵi imodzimodziyo imalimbitsanso kapena kuchirikiza chomera. Mofananamo, mwa kukhala ndi phunziro labwino ndiponso mayanjano abwino, ophunzira atsopano angakhale okhazikika m’choonadi.
Uphungu umenewu unali woyenerera makamaka kwa opita kuubatizo. Inde, patsiku lachiŵiri la msonkhanowo, makamu a ophunzira atsopano anabatizidwa potsatira chitsanzo cha Yesu. Nkhani yakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu Kumatsogolera ku Ubatizo” inakumbutsa opita ku ubatizo kuti kumizidwa m’madzi kuli chizindikiro choyenerera chakuti moyo wawo wakale wadyera wafa. Kutulutsidwa kwawo m’madzi kumatanthauza kuti iwo akhalanso ndi moyo kuti achite chifuniro cha Mulungu.
Nkhani yakuti “Menyani Zolimba Nkhondo ya Chikhulupiriro” inatengedwa m’buku la Baibulo la Yuda. Tinalimbikitsidwa kutetezera chikhulupiriro chathu mwa kukana makhalidwe oipitsa munthu, monga chiwerewere, upandu, ndi mpatuko. Ndiyeno, nkhani yakuti “Samalirani Banja Lanu” inakhudza kwambiri makolo, makamaka atate. Kusamalira zosoŵa za banja zauzimu, zakuthupi, ndi zamalingaliro ndi udindo wa m’Malemba. (1 Timoteo 5:8) Zimenezi zimafuna nthaŵi, kulankhulana, ndi kukhala oyandikana. Ndithudi Yehova Mulungu amakondwera nayo ntchito yonse yaikulu imene makolo achikristu amachita kuti alere ana awo m’choonadi.
Nkhani yosiyirana yotsatira yakuti, “Tiyeni ku Nyumba ya Yehova,” inakulitsa chiyamikiro chathu cha misonkhano yachikristu. Iyo imatimasula pankhaŵa za dzikoli. Pamisonkhano timakhala ndi mpata wolimbikitsana, ndipo tingasonyeze chikondi chathu kwa okhulupirira anzathu. (Ahebri 10:24, 25) Misonkhano imatithandizanso kuwonjezera maluso athu monga aphunzitsi, ndipo imawonjezera kumvetsa kwathu chifuno cha Mulungu. (Miyambo 27:17) Tisayese kupatukana ndi mpingo, ndiponso tiyeni tikumbukire mawu a Yesu akuti: “Kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pawo.”—Mateyu 18:20.
Nkhani yomaliza patsikulo inali yakuti “Mtundu wa Chikhulupiriro Chanu—Ukuyesedwa Tsopano.” Chikhulupiriro chosayesedwa chilibe umboni wa mtengo wake, ndipo mtundu wake umakhala wosadziŵika. Chili ngati cheke chimene sichinasinthidwebe. Kodi chilidi ndi mtengo wolembedwapo? Mofananamo, chikhulupiriro chathu chiyenera kuyesedwa kuti titsimikize kuti chili cholimba ndipo mtundu wake ndi weniweni. (1 Petro 1:6, 7) Mlankhuliyo anati: “Nthaŵi zina, ofalitsa nkhani pamodzi ndi akuluakulu a boma amanyengedwa ndi atsogoleri achipembedzo ndi ampatuko kuti atinenere zonama, kupotoza zikhulupiriro zathu zachikristu ndi khalidwe lathu. . . . Kodi tidzalola aja ochititsidwa khungu ndi Satana kuti atichititse mantha ndi kutifooketsa ndi kutipangitsa kuchita manyazi ndi uthenga wabwino? Kodi tidzalola mabodza onena za choonadi kutilepheretsa kufika pamisonkhano ndi kugwira ntchito yathu yolalikira nthaŵi zonse? Kapena kodi tidzachirimika ndi kukhala olimba ndi otsimikiza mtima kuposa ndi kale lonse kuti tipitirize kulengeza choonadi chonena za Yehova ndi Ufumu wake?”
Khalani ndi Moyo mwa Chikhulupiriro
Mutu wa tsiku lachitatu la msonkhanowu unazikidwa pa mawu a Paulo akuti: “Chidziŵikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.” (Agalatiya 3:11) Nkhani yosiyirana yakuti, “Mawu a Ulosi wa Yoweli Onena za Tsiku Lathu,” inali imodzi mwa nkhani zochititsa chidwi mmaŵa. Buku la Yoweli limanena za nthaŵi yathu ndipo limati mosonyeza changu: “Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.” (Yoweli 1:15) Mofanana ndi dzombe losatopa, Akristu odzozedwa sanalole chilichonse kuwatsekereza polengeza za Ufumu m’nthaŵi ino yamapeto.
Buku la Yoweli limaperekanso chiyembekezo pamene limati: “Aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.” (Yoweli 2:32) Zimenezi sizikutanthauza kungoitana pa dzina la Yehova basi. Kulapa kochokera pansi pa mtima nkofunika, ndipo kulapaku kumaphatikizapo kusiya kuchita zoipa. (Yoweli 2:12, 13) Palibe nthaŵi yozengereza chifukwa Yehova adzaweruza mitundu posachedwapa, monga momwe anachitira ndi Moabu, Amoni, ndi a m’phiri la Seiri m’nthaŵi ya Mfumu Yehosafati wa Yuda.—2 Mbiri 20:1-30; Yoweli 3:2, 12.
Onse analimbikitsidwa ndi nkhani yakuti “Sonyezani Chikhulupiriro Mwa Kuyembekeza Yehova.” Tsopano pamene tili mkati mwenimweni mwa nthaŵi yamapeto, tingakumbukire kukwaniritsidwa kwa ambiri mwa malonjezo a Yehova, ndipo tikufunitsitsa kuona zinthu zimene zidzakwaniritsidwabe. Anthu a Yehova ayenera kupitirizabe kukhala oleza mtima, pokumbukira kuti zonse zimene Mulungu analonjeza zidzachitika.—Tito 2:13; 2 Petro 3:9, 10.
Programu ya mmaŵa inatha ndi seŵero lakuti “Khalani ndi Diso la Kumodzi.” Seŵero limeneli losonyeza zinthu zimene zimachitika linatilimbikitsa kupenda zimene timaganiza ponena za kulondola zinthu zakuthupi. Mosasamala kanthu kuti kaya timakhala kuti, ngati tikufunadi kuti moyo wathu ukhale wopanda nkhaŵa, tiyenera kutsatira uphungu wa Yesu wakuti tikhale ndi diso lakumodzi, losumika bwino lomwe pa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 6:22.
Nkhani yapoyera inali ndi mutu wochititsa chidwi wakuti “Chikhulupiriro ndi Mtsogolo Mwanu.” Iyo inapereka umboni wosonyeza kuti atsogoleri aumunthu sangathetse mavuto a dziko. (Yeremiya 10:23) Zochitika m’mbiri ya munthu zikubwerezabwereza—pamlingo waukulu ndipo wowononga kwambiri. Kodi ndi motani mmene Mboni za Yehova zimaonera mtsogolo? Timakhulupirira kuti kutsogoloku mtundu wa anthu okhulupirika udzakhala wosangalala mu Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 5:5) Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake kaamba ka phindu la onse amene ali ndi chikhulupiriro m’Mawu ake, amene amatilimbikitsa kuti: “Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi.”—Yesaya 55:6.
Yesu anafunsa funso lofunika kwambiri ponena za tsiku lathu. Iye anafunsa kuti: “Mwana wa munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?” (Luka 18:8) Nkhani yomaliza inapenda programu ya msonkhano ndipo inasonyeza mmene programuyo inaperekera umboni womvekera bwino wakuti anthu okhulupirira Mawu a Mulungu alipo, ngakhale kuti tikukhala m’dziko lopanda chikhulupiriro ndiponso losapembedza.
Komabe, aliyense payekha angadzifunse kuti, ‘Kodi ndili pakati pa awo amene ali ndi chikhulupiriro chosagwedera mwa Mulungu ndi Mawu ake?’ Msonkhano Wachigawo wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” uyenera kutithandiza kuyankha funsolo kuti inde. Ndipo tikumthokozadi kwambiri Yehova polimbitsa chikhulupiriro chathu mwa iye ndi Mawu ake, Baibulo!
[Zithunzi patsamba 24]
Ambiri anadzipereka mokondwa kulandira nthumwi zikwi zambiri m’nyumba zawo
[Zithunzi patsamba 25]
Mabwalo aakulu kwambiri a maseŵero monga awa anagwiritsiridwa ntchito padziko lonse
[Chithunzi patsamba 25]
L. A. Swingle wa m’Bungwe Lolamulira akutulutsa brosha latsopano
[Chithunzi patsamba 26]
Ambiri anabatizidwa monga chizindikiro cha kudzipatulira kwawo kwa Yehova
[Zithunzi patsamba 27]
Osonkhana anaimba nyimbo za Ufumu mokondwera. Chithunzi chamkati: seŵero lakuti “Khalani ndi Diso la Kumodzi”