Kodi Ndinu Munthu Woyembekezera Zabwino Kapena Woyembekezera Zoipa?
“INALI nthaŵi yabwino kwambiri, inali nthaŵi yoipa kwambiri, . . . inali nthaŵi yokulitsa chiyembekezo, inali nthaŵi yakufa kwa chiyembekezo, zonse tinali nazo, zonse tinalibe.” Mawu oyamba amenewo a buku la katswiri Charles Dickens lakuti A Tale of Two Cities (Nkhani ya Mizinda Iŵiri) amasiyanitsa mwaluso mmene zochitika zimakhudzira kaganizidwe, kamvedwe ndi kaonedwe kathu ka zinthu.
Mizinda iŵiri yotchulidwayo inali London ndi Paris panthaŵi ya chipwirikiti cha Chipanduko cha Afalansa. Kwa nzika zoponderezedwa za France m’zaka za zana la 18, inalidi “nthaŵi yokulitsa chiyembekezo” pakuti chipandukocho chinali kulengeza za ufulu wa chibadwidwe wa anthu. Koma kwa awo a muulamuliro wakale, kapena a dongosolo la ndale lomwe linali kuchoka, inali “nthaŵi yakufa kwa chiyembekezo,” yotsogolera ku imfa ndi chiwonongeko.
Kuyembekezera zabwino kapena kuyembekezera zoipa? Zinadalira pa mbali imene munthu anaiyanja. Ndipo zikuterobe.
Nthaŵi ya Kudzipenda
Kodi ndinu munthu woyembekezera zabwino? Kodi mumaona mbali yosangalatsa ya moyo, nthaŵi zonse kuyembekezera zabwino? Kapena mumakonda kuyembekezera zoipa, mukumaoneratu zinthu molakwika, kumayembekezera zinthu zabwino kwambiri koma panthaŵi imodzimodziyo kumayembekezeranso zinthu zoipa kwambiri?
Zaka 60 zapitazo, wolemba mabuku a nthano wa ku America, James Branch Cabell, anafotokoza malingaliro aŵiri otsutsanaŵa motere: “Munthu woyembekezera zabwino amati tikukhala m’dziko labwino kwambiri; ndipo munthu woyembekezera zoipa amada nkhaŵa kuti ngati zimenezi ndi zoona ndiye kuti kulibe zabwino.” Ngati mukuona kuti zimenezi nzosadalirika, pendani zifukwa zochirikiza ndi zotsutsa za mbali zitatu chabe za zochitika za dziko lerolino monga mmene zalongosoledwera pansipa. Kenako pendani kaonedwe kanu ka zimenezi ndipo dzifunseni kuti, ‘Kodi ndine munthu woyembekezera zinthu zabwino kapena woyembekezera zoipa?’
Mtendere Wokhalitsa: Kodi mungatchule malo angati padziko lapansi mmene muli mavuto? Ireland, dziko limene kale linali Yugoslavia, Middle East, Burundi, Rwanda—amenewa amangobwera m’maganizo. Kodi mavutowa ndi mikangano ina zingathetsedwe kuti pakhale mtendere wokhalitsa padziko lonse? Kodi dziko lidzakhala ndi mtendere?
Kukhazikika kwa Chuma: Pakuyembekezera kugwirizana m’zachuma pofika 1999, maiko a m’bungwe la European Union akulimbana mwamphamvu ndi mavuto a kutha mphamvu kwa ndalama ndi maboma kubwereka ndalama kwa anthu. Kwina, ziphuphu zimawononga mkhalidwe wa zachuma wa maiko ochuluka a ku America ndi Afirika kumene kutha mphamvu kwa ndalama kuli pafupifupi vuto losatha ndipo mavuto autundu adakagaŵanitsabe anthu. Kodi kukhazikika kwa chuma padziko lonse kuli patsogolopa?
Kusoŵa kwa Ntchito: Pachisankho cha m’dziko lonse mu 1997, matchalitchi a ku Britain anagwirizana kuti aumirize zipani zonse zandale kuti ziike nkhani ya kulemba ntchito anthu onse pamalo oyamba pazokambitsirana zawo. Koma pokhala ndi pafupifupi 30 peresenti ya anthu ofunikira ntchito padziko lonse amene sali pantchito kapena akugwira ntchito yosayenererana ndi luso lawo, kodi pangakhaledi ntchito ya anthu onse yokhalitsa—makamaka kwa achinyamata?
Ndi kosavuta chotani nanga kuyembekezera zinthu zoipa! Komatu pali mbali yosangalatsa, ndipo tikukupemphani kuti mulingalire mmene kulili kotheka kuyembekezera zinthu zabwino.
[Chithunzi patsamba 3]
Chipanduko cha Afalansa
[Mawu a Chithunzi]
Kuchokera m’buku lakuti Pictorial History of the World