Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 2/15 tsamba 8-11
  • Makolo Tetezerani Ana Anu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo Tetezerani Ana Anu!
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malingaliro a mu Afirika Ponena za Maphunziro a Zakugonana
  • Nkuwalangiziranji?
  • Kulankhulana Kwabwino
  • Otetezeredwa ndi Achimwemwe
  • Muzikambirana ndi Ana Anu Nkhani Zokhudza Kugonana
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Ndingatani Ngati Anzanga Akundikakamiza Kugonana?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Tetezerani Banja Lanu ku Zisonkhezero Zowononga
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Mungatani Kuti Aliyense Azisangalala M’banja Lanu?​—Mbali Yachiwiri
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 2/15 tsamba 8-11

Makolo Tetezerani Ana Anu!

PA SUKULU ina yasekondale ku Nigeria, mtsikana wina wodziŵika chifukwa cha kuchita zachiwerewere anali kukonda kulangiza ophunzira anzake aakazi pankhani za kugonana. Amodzi mwa mankhwala ake otayira mimba anali moŵa wachimera wosasa wosanganiza ndi chikonga cha fodya chochuluka. Nkhani zake, zimene anali kuzitenga m’magazini a zamaliseche, zinali kuchititsa chidwi ophunzira anzake ambiri. Ena anayamba kuyesa kuchita nawo zogonana, ndipo mmodzi mwa iwo anatenga mimba. Kuti ataye mimbayo, anamwa msanganizowo wa moŵa ndi fodya. Patangopita maola ochepa, anayamba kusanza mwazi. Masiku angapo pambuyo pake, anamwalira m’chipatala.

M’dziko lamakonoli, achinyamata ambiri amangokhalira kusimba zogonana, kuwononga omvetsera otengeka maganizo msanga. Kodi achinyamata ayenera kupita kwa yani kuti akapeze chidziŵitso cholongosoka chimene chidzawatetezera? Zimakhala bwino chotani nanga ngati apita kwa makolo awo oopa Mulungu, amene ali ndi udindo wowalera “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”​—Aefeso 6:4.

Malingaliro a mu Afirika Ponena za Maphunziro a Zakugonana

Kuzungulira dziko lonse, makolo ambiri zimawavuta kwambiri kuti akambitsirane ndi ana awo ponena za kugonana. Zimenezi zili choncho makamaka mu Afirika. Donald, atate wina wa ku Sierra Leone, anati: “Sizimachitika nkomwe. Kulankhula nkhani zimenezi sichikhalidwe cha mu Afirika.” Mkazi wina wa ku Nigeria wotchedwa Confident anavomereza kuti: “Makolo anga amaona kuti nkhani ya kugonana njosayenera kuitchula poyera; mogwirizana ndi mwambo kutchula zimenezo nkulaula.”

M’miyambo ina yachiafirika, kutchula mawu okhudza kugonana monga mbolo, ubwamuna, kapena kukhala kumwezi amakuona ngati kulaula. Mayi wina wachikristu analetsa mwana wake wamkazi kuti asamatchule mpang’ono pomwe mawu akuti “kugonana,” ngakhale anamuuza kuti angatchule mawu akuti “chigololo.” Mosiyana ndi zimenezo, Mawu a Mulungu Baibulo amanena mosabisa za kugonana ndi ziŵalo zogonanira. (Genesis 17:11; 18:11; 30:16, 17, NW; Levitiko 15:2, NW) Cholinga chake sindicho kulaula kapena kudzutsa chilakolako koma kutetezera ndi kulangiza anthu a Mulungu.​—2 Timoteo 3:16.

Kusiyapo zonena kuti mwamwambo nkulaula, chifukwa china chimene makolo ena samanenerapo kalikonse chinafotokozedwa ndi atate wina wa ku Nigeria kuti: “Ngati ndikambitsirana ndi ana anga ponena za kugonana, akhoza kusonkhezereka kuti akachite zachiwerewere.” Koma kodi chidziŵitso chaulemu, chochokera m’Baibulo chonena za kugonana chimasonkhezera ana kukachita zachiwerewere? Ayi, sichimatero. Ndipotu zitha kuchitika kuti pamene ana sadziŵa zambiri, mpamenenso angaloŵe msanga m’mavuto. “Nzeru [yozikidwa pachidziŵitso cholongosoka] ichinjiriza.”​—Mlaliki 7:12.

M’fanizo la Yesu, mwamuna wochenjera, atadziŵa kuti mikuntho ingabwere mtsogolo, anamanga nyumba yake pathanthwe pamene kuli kwakuti mwamuna wopusa anamanga pamchenga ndipo nyumba yake inagwa. (Mateyu 7:24-27) Mofananamo, makolo achikristu ochenjera, podziŵa kuti ana awo adzakumana ndi zitsenderezo zonga mikuntho zofuna kuwakakamiza kutsatira malingaliro olakwika a dziko okhudza zakugonana, amalimbitsa ana awo ndi chidziŵitso cholongosoka ndi kumvetsetsa, zinthu zimene zidzawathandiza kukhalabe olimba.

Chifukwa chinanso chimene makolo ambiri samakambitsirana ndi ana awo ponena za kugonana chinafotokozedwa ndi mkazi wina wachiafirika kuti: “Pamene ndinali wachinyamata, makolo anga amene anali Mboni sanalankhulepo nane ponena za kugonana, choncho inenso sindimaganizira zokambitsirana nkhanizi ndi ana anga.” Komabe, achinyamata amakono akukumana ndi mavuto aakulu kuposa amene achinyamata anakumana nawo zaka 10 kapena 20 zapitazo. Zimenezi nzosadabwitsa. Mawu a Mulungu ananeneratu kuti “masiku otsiriza . . . anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.”​—2 Timoteo 3:1, 13.

Chimene chikuwonjezera vutolo nchakuti ana ambiri samafuna kapena samatha kukambitsirana zakukhosi ndi makolo awo. Makolo ndi ana sakambitsirana kwenikweni ngakhale pankhani zazing’ono. Wachinyamata wina wazaka 19 anadandaula kuti: “Palibe zimene timakambitsirana ndi makolo anga. Ineyo ndi atate wanga sitimalankhulana kwenikweni. Iwo samamvetsera.”

Achinyamata angaopenso kuti kufunsa zinthu zokhudza kugonana kungadzetse zotsatirapo zoipa. Mtsikana wina wazaka 16 anati: “Makolo anga sindimakambitsirana nawo za mavuto okhudza zakugonana chifukwa cha mmene amaonera nkhani zimenezi. Kumbuyoku mkulu wanga anafunsa Amayi mafunso ena okhudza kugonana. M’malo moti amayi amthandize pavuto lakelo, iwo anayamba kukayikira zolinga zake. Nthaŵi zambiri amayi anali kundiitana ndi kundifunsa za mkulu wanga, nthaŵi zina kumanena kuti mkulu wanga alibe khalidwe labwino. Sindikufuna kutaya chikondi cha amayi pa ine, choncho sindimawauza za mavuto anga.”

Nkuwalangiziranji?

Kulangiza ana athu mokwanira pankhani zakugonana sikuli chabe chinthu choyenera kuchichita komanso chinthu chokoma mtima kuchichita. Ngati makolo saphunzitsa ana awo ponena za kugonana, ena adzawaphunzitsa​—kaŵirikaŵiri zimachitika mwamsanga kwambiri kuposa mmene makolo akuganizira ndipo pafupifupi nthaŵi zonse zimakhala zosagwirizana ndi mapulinsipulo aumulungu. Mtsikana wina wazaka 13 anachita chisembwere chifukwa cha zimene mnzake wa kusukulu anamuuza kuti ngati sataya unamwali wake, adzamva kupweteka koopsa mtsogolo. “Unamwali wako adzaudula ndi sizala,” anamuuza motero. Atamfunsa pambuyo pake chifukwa chimene sanauzire amayi wake wachikristu zimene anamva, mtsikanayo anayankha kuti nkhani ngati zimenezi sizimatchulidwa kwa akulu.

Mtsikana wina wa ku Nigeria anati: “Anzanga a kusukulu anayesetsa kundiumiriza kukhulupirira kuti kugonana ndi chinthu chimene anthu onse athanzi ayenera kuchita. Anandiuza kuti ngati sindimachita zakugonana tsopano, ndikadzafika zaka 21 zakubadwa, ndidzayamba kudwala matenda amene adzawononga kwambiri chikhalidwe changa chachikazi. Choncho kuti ndipeŵe ngozi yoipitsitsa imeneyi, iwo anati kuli bwino kuchita zakugonana ndisanaloŵe mu ukwati.”

Pokhala anali kukambitsirana bwino ndi makolo ake, nthaŵi yomweyo anaona kuti zinali zowombana ndi zimene anaphunzira kunyumba. “Monga mwa nthaŵi zonse, ndinabwerera kunyumba ndi kuuza amayi zimene anandiuza kusukulu.” Amayi wake anatsutsa bodzalo.​—Yerekezerani ndi Miyambo 14:15.

Mwa kupatsa ana chidziŵitso chofunikira kuti chiwathandize kukhala ndi nzeru zaumulungu pankhani zokhudza kugonana, makolo amawakonzekeretsa kuzindikira mikhalidwe yangozi ndi kuzindikira anthu amene akufuna kuwawononga. Zimathandiza kuwatetezera ku kusweka mtima chifukwa cha matenda opatsirana mwa kugonana ndi mimba zapathengo. Zimawathandiza kukhala odzilemekeza ndi kuchititsa ena kuwalemekeza. Zimawachititsa kusakhala ndi malingaliro olakwika ndi nkhaŵa. Zimawachititsa kukhala ndi malingaliro abwino ndiponso oyenera ponena za kugonana koyenerera, zimene zidzawapatsa chimwemwe akadzakwatira kapena kukwatiwa mtsogolo. Zingawathandize kukhalabe ndi kaimidwe kabwino pamaso pa Mulungu. Ndipo pamene ana aona chisamaliro chachikondi pa iwo, zingawasonkhezere kulemekeza kwambiri makolo awo ndi kuwakonda.

Kulankhulana Kwabwino

Kuti makolo apereke uphungu malinga ndi zosoŵa za ana awo, onse aŵiri makolo ndi anawo ayenera kumalankhulana. Ngati makolo sakudziŵa zimene zili m’maganizo a ana awo ndi m’mitima yawo, ngakhale uphungu wabwino ungakhale wopanda phindu, monga momwe zingakhalire ngati dokotala akuyesa kupereka mankhwala asanadziŵe matenda a wodwala. Kuti makolo akhale aphungu abwino, iwo ayenera kudziŵa zimene ana awo amalingaliradi ndiponso mmene amakhudzidwira. Iwo ayenera kudziŵa bwino zitsenderezo ndi mavuto amene ana awo akuyang’anizana nawo ndi mafunso amene akuwavutitsa. Nkofunika kwambiri kuwamvetsera mosamalitsa ana, kukhala “wotchera khutu, wodekha polankhula.”​—Yakobo 1:19; Miyambo 12:18; Mlaliki 7:8.

Zimafuna nthaŵi, kuleza mtima, ndi kuyesayesa kuti makolo akulitse ndi kukhalabe ndi unansi wathithithi kwambiri ndi ana awo, unansi umene ana amakhala omasuka kuulula zonse zakukhosi kwawo. Komano zimakhala zosangalatsa chotani nanga pamene zimenezi zatheka! Atate wina wa ana asanu wa Kumadzulo kwa Afirika anati: “Ndine ponse paŵiri atate ndi bwenzi lapamtima. Ana amalankhula nane nkhani zonse momasuka, kuphatikizapo nkhani zokhudza kugonana. Ngakhale atsikana amandiuza zakukhosi zawo. Timakhala ndi nthaŵi yokambitsirana za mavuto awo. Iwo amandifotokozeranso zonse zimene zikuwasangalatsa.”

Bola, mmodzi mwa ana ake aakazi, anati: “Atate sindimawabisira kanthu. Atate ndi munthu woganizira ena ndiponso wachikondi. Samatimenya kapena kutikalipira, ngakhale pamene talakwa. M’malo mokwiya, iwo amaipenda nkhani yake ndi kutisonyeza zimene tiyenera kuchita kapena zimene sitinali kuyenera kuchita. Nthaŵi zambiri amagwiritsira ntchito buku la Youth ndi buku la Chimwemwe cha Banja.”a

Ngati nkotheka, kuli bwino kuti makolo aziyamba kukambitsirana ndi ana awo ponena za kugonana anawo adakali aang’ono ndithu. Zimenezi zimayala maziko a makambitsirano ena opitirizabe pausinkhu umene nthaŵi zambiri umakhala wovuta wa zaka zapakati pa 13 ndi 19. Ngati simunayambe kukambitsirana nkhanizo mwamsanga, nthaŵi zina mumachita manyazi kuti muyambe kukambitsirana pambuyo pake, koma mukhoza kuyamba. Mayi wina wa ana asanu anati: “Ndinadzikakamiza kulankhula nkhani zimenezo mpaka pamene manyazi anga ndi a mwana wanga anatha.” Popeza kuti ubwino wa mwana wanu uli pangozi, kuyesayesa kotero kulidi koyenerera.

Otetezeredwa ndi Achimwemwe

Ana amayamikira makolo amene mwachikondi amawakonzekeretsa ndi chidziŵitso chimene chidzawatetezera. Talingalirani za ndemanga za Mboni zina za Yehova zachiafirika:

Mojisola wazaka 24 anati: “Nthaŵi zonse ndidzawathokoza amayi wanga. Anandiphunzitsa panthaŵi yake ponena za kugonana. Ngakhale kuti ndinali kuchita manyazi kalelo pamene anali kundiuza nkhani zimenezo, tsopano ndikuona kuti amayi anandichitira zinthu zabwino.”

Iniobong anawonjezera kuti: “Nthaŵi zonse ndikakumbukira ndi kuganiza zimene Amayi andichitira mwa kundiphunzitsa zonse ponena za kugonana ndimakondwera. Zandithandiza kwambiri kukhala mkazi weniweni. Inenso ndili wotsimikiza kudzachita chimodzimodzi ndi ana anga mtsogolo.”

Kunle wazaka 19 anati: “Makolo anga anandithandiza kulimbana ndi zitsenderezo za akazi akudziko ongofuna zakugonana. Chipanda maphunziro amene anandiphunzitsa, ndikanaloŵa m’tchimo. Sindidzaiŵala zabwino zimene anandichitira.”

Christiana anati: “Ndimapindula kwambiri mwa kukambitsirana ndi amayi nkhani zokhudza kugonana. Zanditetezera ku matenda akupha ndi mimba zapathengo, ndipo abale anga ndi alongo anga aang’ono ndawaikira chitsanzo chabwino choti atsanzire. Komanso anthu ayamba kundilemekeza, ndipo mwamuna wanga wamtsogolo nayenso adzandilemekeza. Ndipo chofunika kwambiri nchakuti ndili ndi unansi wabwino ndi Yehova Mulungu chifukwa cha kusunga malamulo ake.”

Bola, wotchulidwa poyamba, anati: “Ndinali ndi mnzanga wina m’kalasi amene anali kunena kuti munthu ayenera kusangalala ndi kugonana popanda kudzipereka mu ukwati. Kwa iye, kugonana kunali maseŵera. Komabe, anadziŵa kuti sanali maseŵera atatenga mimba ndi kulephera kulemba nafe mayeso a boma. Chikhala kuti ndinalibe atate wabwino wonditsogolera, mwina ndikanakhala ngati iyeyo, kuzindikira nditaloŵa kale m’mavuto.”

Lilidi dalitso pamene makolo achikristu athandiza ana awo kukhala ndi “nzeru kufikira chipulumutso” m’dziko lino lotengeka maganizo ndi kugonana! (Timoteo 3:15) Malangizo awo ochokera m’Baibulo ali ngati mkanda wamtengo wapatali wokometsera ndi kukongoletsa ana pamaso pa Mulungu. (Miyambo 1:8, 9) Ana amadzimva kukhala osungika, ndipo makolo amakhala okhutira kwambiri. Atate wina wachiafirika amene nthaŵi zonse amayesetsa kukambitsirana zakukhosi ndi ana ake aang’ono anati: “Tili ndi mtendere wamaganizo. Tili ndi chidaliro chakuti ana athu akudziŵa zimene zimakondweretsa Yehova; sangasokeretsedwe ndi anthu akunja. Ndife otsimikiza kuti sadzachita zinthu zimene zidzakhumudwitsa banja lathu. Ndikuthokoza Yehova kuti chidaliro chathu mwa iwo chakhala chopindulitsa.”

[Mawu a M’munsi]

a Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 10]

Akristu achinyamata amene amalandira chidziŵitso cha m’Baibulo kuchokera kwa makolo awo akhoza kukana nkhani zabodza zimene achinyamata ena amasimba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena