Olengeza Ufumu Akusimba
Mulungu Akulitsa Mbewu ku Alaska
PANSI pa chipale chofeŵa ndi madzi oundana okuta nthaka, kambewu kakang’ono kamayembekezera mpata woti kakule kukhala chomera chokhwima. Pamiyezi itatu yaifupi yachilimwe imeneyo ku Alaska, kambewu ka kabichi ka mamilimita atatu kamakula kukhala pafupifupi makilogalamu 40! Inde, dzikoli limene ambiri kale ankaliona ngati losabala ndiponso lodzala ndi mitsinje ya madzi oundana lingatulutse zipatso za mwana alirenji.
Zilidi motero makamaka ndi munda wauzimu ku Alaska. Kumeneko, kudziko la nyengo zazitali zachisanu, Mboni za Yehova zikupitirizabe kufesa mbewu za Ufumu. Monga m’mbali zina za dziko lapansi, Mulungu akukulitsa mbewu m’mitima yachonde.—1 Akorinto 3:6, 7.
● Pamene anali m’basi yasukulu, Vanessa, Mboni yachinyamata, anaona wophunzira mnzake, Ann, amene nthaŵi zonse anali kukhala payekha m’basimo. Ann anaoneka kukhala wachisoni, choncho Vanessa anaitana Ann kuti adzakhale naye. Ann anayeneradi kukhala wachisoni! Amayi ake anamwalira ndi nthenda ya mtima, kenako posapita nthaŵi, atate ake anamwalira ndi matenda a kansa. Ndiye chifukwa chake Ann anali kukhala ndi achibale ake ku Alaska.
Vanessa anadzera panyumba ya bwenzi lake latsopanolo pamene anali mu utumiki wakumunda Loŵeruka lina namsiyira brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Lolemba lotsatira kusukulu, Ann anafunafuna Mboni yachinyamatayo. Ann anali ndi mafunso ambiri okhudza za m’Baibulo, amene Vanessa anayankha. “Kodi mumapempherera kuti?” anafunsa motero. Madzulowo Ann anafika pamsonkhano kwa nthaŵi yoyamba pa Nyumba ya Ufumu.
Sipanapite nthaŵi mwana wamasiyeyu wazaka zakubadwa 17 asanapeze “atate” ndi “amayi” ambiri, mongadi momwe Yesu analonjezera. (Mateyu 19:29) Ndipo inali nthaŵi yosangalatsa chotani nanga kuona Ann akumwetulira mwachimwemwe posonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi pa Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu”!
● Kumadera akumidzi a m’chigawo chachikulu cha Arctic ku Alaska—kumene midzi ili yotalikirana ndi mitunda yachipululu yamakilomita mazana ambiri—ndege ya mainjini aŵiri ya Watch Tower Society aigwiritsira ntchito kufesa mbewu za Ufumu m’midzi yoposa 150. Koma kukula kwauzimu mwa kuchita phunziro la Baibulo lokhazikika kumadalira pa kulemberana makalata. Popeza kuti kulemba makalata kumawavuta ambiri, mphunzitsi wa Baibulo amafunikira kukhala waluso kuti achititse wophunzira kukhalabe wachidwi. Kodi zimenezi zingachitike motani?
Kathy anachititsa phunziro la Baibulo lopita patsogolo kwa Edna, ngakhale kuti Edna anali kukhala pamtunda wamakilomita oposa 600! M’malo mongojambula mafunso a m’buku lophunziridwa, Kathy analemba mafunso papepala lina ndi kusiya madanga olembamo mayankho. Edna atalembamo mayankho, Kathy anali kuyankha ndi kulembamonso ndemanga zina ngati akufuna kumveketsa mfundo iliyonse. Kathy anati: “Ndinasankha kuti tizichita ‘phunziro’ lathu Lachitatu madzulo, ndipo ndinayesetsa kusunga nthaŵiyo monga momwe ndingasungire nthaŵi ina iliyonse yokachititsa phunziro la Baibulo. Ndiponso ndinali kutumizira Edna envulopu yokhala ndi keyala yanga ndiponso yoikapo kale sitampu. Popeza kuti makalata anali kutenga milungu iŵiri kuti akafike, phunziro lochita mwa kulemberana makalata linaoneka monga likuchedwa.”
Tangolingalirani za chimwemwe chawo pamene Kathy ndi Edna anaonana maso ndi maso pamsonkhano wachigawo ku Anchorage atachita phunziro mwa kulemberana makalata kwa miyezi khumi! Mboni zinasangalalanso kuti ophunzira Baibulo ndi okondwerera ochokera kumidzi yakutali ya Alaska anapezekapo.
Ngakhale kuti nthaŵi zina kukula kungaoneke monga kukuchedwa, “mbewu” zina zimamera msanga ngati pali kuunika kwa choonadi. Pa avareji, atamandi atsopano a Yehova oposa zana limodzi amabatizidwa chaka chilichonse ku Alaska! Tikuti, “Zikomo, Yehova,” pokulitsa mbewuzo!