Olengeza Ufumu Akusimba
“Anthu Anu Adzadzipereka Eni Ake”
KAZEMBE wankhondo wamphamvu wa Aramu, Namani, ali ndi khate. Ngati sichiritsidwa, nthenda yoopsa imeneyi ingamlumaze ndiponso kumupha. Kodi Namani ayenera kuchitanji? Pakati pa a m’banja la Namani pali mtsikana wamng’ono, ‘wandende wochokera kudziko la Israyeli.’ Iye akulankhula molimba mtima ndipo akufotokoza kuti mneneri Elisa ndiye amene angachiritse Namani.—2 Mafumu 5:1-3.
Chifukwa cha kulimba mtima kwa mtsikanayu, Namani afunafuna Elisa ndipo akuchiritsidwa. Ndiponso, Namani akukhala wolambira Yehova! Chokumana nacho chimenechi, cholembedwa m’Baibulo, chinachitika m’zaka za zana lakhumi B.C.E. (2 Mafumu 5:4-15) Lerolino, achinyamata ambiri akusonyeza kulimba mtima kofananako polankhula za zinthu za Ufumu. Chokumana nacho chotsatirachi chochokera ku Mozambique chikusonyeza zimenezi.
Nuno wazaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa ali wofalitsa wosabatizidwa wa uthenga wabwino. Ngakhale pamene anali asanakhale nkomwe wofalitsa wosabatizidwa, Nuno anali kusonkhanitsa ana anzake oyandikana ndi nyumba yawo, kupereka pemphero, ndi kuwaphunzitsa Baibulo, akumagwiritsira ntchito buku lotchedwa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.
Nthaŵi zambiri Nuno amadzuka mmamaŵa kwambiri Loŵeruka ndi kukumbutsa banja lake kuti: “Lerotu tipita ku utumiki wakumunda.” Changu chake pa utumiki chimasonyezedwa m’njira zinanso. Pamene atsagana ndi makolo ake mu utumiki wa mumsewu ku Maputo, Nuno nthaŵi zambiri amafikira anthu ali yekha. Tsiku lina, mwamuna wina wazamalonda anakumana naye ndi kumfunsa kuti: “Kodi nchifukwa ninji ukugulitsa magazini ameneŵa?” Nuno anayankha kuti: “Sindikugulitsa magaziniwa, koma ndimalandira chopereka chothandizira ntchito yolalikira.” Wazamalondayo anati: “Ngakhale kuti sindikuwafuna magaziniwa, ndachita chidwi ndi malingaliro ako ndi luso lako. Ndikufuna kupereka chopereka chothandizira ntchito imeneyi.”
Nthaŵi inanso, Nuno anafikira mwamuna pamsewu ndi kumsonyeza buku lotchedwa Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani? Mwamunayo anafunsa kuti: “Kodi suphunzira pasukulu iyo ili apoyo?” “Inde,” anayankha chotero Nuno, “Ndimaphunzira pasukulu imeneyo, koma lero ndikulalikira uthenga wofunika wochokera m’bukuli. Likusonyeza kuti mungakhale m’dziko latsopano limene Mulungu adzabweretsa, monga momwe chikusonyezera chithunzi chimene chili m’bukuli.” Nuno sanadziŵe nkomwe kuti munthu amene anali kulankhula nayeyo anali mphunzitsi wa pasukulu yake. Mphunzitsiyo sanangolandira chabe bukulo ayi koma tsopano amalandiranso magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthaŵi zambiri kuchokera kwa Nuno.
Nuno akafunsidwa kuti afotokoze chifukwa chimene amakondera ntchito yolalikira, iye amayankha kuti: “Ndimafuna kulankhula kwa anthu ndi kuwaphunzitsa za Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu.” Iye amanenanso kuti: “Ndipo ngati anthu samvetsera, palibe chifukwa chokhumudwira.”
Kuzungulira dziko lonse lapansi, achinyamata zikwi zambiri monga Nuno ‘akudzipereka eni ake’ kuti aphunzitse ndi kulalikira za Ufumu wa Mulungu. (Salmo 110:3) Koma zimenezi sizimangochitika mwamwayi. Makolo amene amaphunzitsa ana awo za Yehova kuyambira paukhanda wawo, kupereka chitsanzo chabwino mu utumiki, ndiponso kulondola mwachangu zinthu za Ufumu adzapeza mapindu ochuluka.