Kodi Tidzafunikira Magulu Ankhondo Nthaŵi Zonse?
MAGULU ankhondo awononga chuma chochuluka kwambiri cha anthu ndi kuwononga kwambiri chimwemwe cha anthu. Choncho anthu ena afunsa kuti, ‘Kodi anthu angapeze chisungiko cha padziko lonse moti magulu ankhondo nkuthetsedwa?’ Tsopano pamene kuli kotheka kuti zida zankhondo zowononga kwambiri zingafafanize moyo wonse, funsolo likufuna yankho mwamsanga. Kodi kuyembekezera dziko lopanda magulu ankhondo nkuyembekezeradi zenizeni?
Zinthu zimene zachitikapo kale zambiri zikupereka umboni wakuti pamene unansi wabwino wa maiko uwachititsa kudalirana, pangakhale kutula pansi zida zankhondo. Mwachitsanzo, ubwenzi wapakati pa maiko a Canada ndi United States wachititsa kuti malire awo a mtunda wamakilomita 5,000 asakhale otetezeredwa ndi asilikali kwa zaka zoposa zana limodzi ndi theka. Maiko a Norway ndi Sweden nawonso akhala paubwenzi wotero, monganso maiko ena ambiri. Kodi kumvana pakati pa maiko onse kungapangitse dziko lapansi kusakhala ndi magulu ankhondo? Chifukwa cha kuopsa kwa Nkhondo Yadziko I, anthu ochuluka kuposa ndi kale lonse analikonda lingaliro limenelo.
Atapangana za mtendere mu 1918, chimodzi mwa zifuno za pangano lamtendere la ku Versailles chinali “kutheketsa kuti maiko onse ayambe kuchepetsa zida zankhondo.” M’zaka zotsatira, anthu ochuluka anayamba kukana nkhondo. Ena okana nkhondo ankanena kuti nkhondo ndicho chinthu choipitsitsa chimene chingagwere mtundu choncho njoipa kuposa kugonjetsedwa. Otsutsana ndi anthu okana nkhondo sanavomerezane nazo zimenezo, akumanena kuti kwa zaka mazana ambiri, Ayuda m’madera aakulu sanamenyane kwenikweni ndi owaukira, komabe kuyesayesa kwankhanza kuti Ayudawo afafanizidwe kunapitirizabe. Aafirika sanamenyane ndi awo amene anawabweretsa ku maiko a ku America monga akapolo, komabe anazunzidwa koopsa kwa zaka mazana ambiri.
Komabe, pamene Nkhondo Yadziko II inaulika, ambiri okana nkhondo anafika palingaliro lakuti maiko akufunikira chitetezo. Choncho pamene United Nations inakhazikitsidwa Nkhondo Yadziko II itatha, analimbikira kunena za kugwirizana kwa maiko kuti pasakhale kuputana ndipo osati za kutula pansi zida zankhondo. Mamembala ake anali ndi chiyembekezo chakuti chisungiko choperekedwa m’njira imeneyo chidzapatsa mitundu chidaliro choti atule pansi zida zankhondo.
Vuto lina linayamba kuonekera kwambiri. Kaŵirikaŵiri kuyesayesa kwa mtundu wina kuti ukhale wotetezereka kunachititsa mtundu woyandikana nawo kudzimva kuti sunatetezereke. Kusadalirana kumeneku kunayambitsa mpikisano wopanga zida zankhondo. Koma posachedwapa, maunansi abwino pakati pa mitundu ikuluikulu alimbitsa chiyembekezo cha kutula pansi zida zankhondo. Kuchokera pamenepo, Nkhondo ya ku Gulf ndiponso mavuto a kudziko limene kale linali Yugoslavia kwa ambiri zafafaniza chiyembekezo cha kutula pansi zida zankhondo. Zaka ngati zisanu zapitazo, magazini yotchedwa Time inakambapo kuti: “Ngakhale kuti nkhondo ya mawu yatha, dziko lapansi lakhala malo oopsa kwambiri m’malo mokhala malo osaopsa kwenikweni.”
Kukhumba Kukhala ndi “Wapolisi” Wapadziko Lonse
Anthu ambiri amene aona zochitikazi afika polingalira kuti pakufunikira ulamuliro umodzi wapadziko lonse wokhala ndi gulu lankhondo lamphamvu kwambiri lotha kutetezera aliyense. Popeza kuti bungwe la United Nations kapena maulamuliro amphamvu koposa m’zankhondo padziko lonse lapansi satha kuchita zimenezi, ena amaganiza kuti palibe chiyembekezo chenicheni chamtsogolo. Koma ngati mumalandira Baibulo monga Mawu a Mulungu, mwina munadzifunsapo ngati Mulungu Wamphamvuyonse adzakhutiritsa chosoŵa chofunika mwamsanga chimenechi.
Kodi Iye amene Baibulo limamutcha kuti “Mulungu wa chikondi ndi mtendere” angagwiritsire ntchito mphamvu ya zankhondo posungitsa chilungamo? Ngati zili motero, ndi gulu lankhondo liti? Magulu ankhondo ambiri lerolino amati Mulungu akuwachirikiza, koma kodi akuchitadi chifuniro cha Mulungu? Kapena kodi Mulungu ali ndi njira ina yothandizira ndiponso yoperekera mtendere ndi chisungiko?—2 Akorinto 13:11.
Zimene Mulungu Wamphamvuyonse anachitira Adamu ndi Hava atapanduka kunali kuwachotsa m’Edene ndi kutumiza akerubi kukawatsekera kuti asabwerere. Analengezanso chifuno chake cha kuwononga onse opandukira uchifumu wake. (Genesis 3:15) Kodi zimenezo zidzafuna kuti Mulungu agwiritsire ntchito gulu lankhondo?
Baibulo limasimba za nthaŵi pamene Mulungu anagwiritsira ntchito magulu ankhondo pokwaniritsa ziweruzo zake. Mwachitsanzo, anthu a m’maufumu a m’dziko la Kanani anali kugonana ndi nyama, kupereka ana nsembe, ndi kuchita nkhondo zankhanza. Mulungu analamula kuti adzawonongedwe kotheratu ndipo anagwiritsira ntchito gulu lankhondo la Yoswa pokwaniritsa chiweruzocho. (Deuteronomo 7:1, 2) Mofananamo, gulu lankhondo la Mfumu Davide linakwaniritsa chiweruzo cha Mulungu kwa Afilisti monga chitsanzo cha mmene Mulungu adzawonongera kuipa konse patsiku lake lomaliza lachiweruzo.
Zochitika zimenezo zinali zopereka phunziro. Yehova anasonyeza kuti angagwiritsire ntchito gulu lankhondo popatsa anthu chisungiko. Ndithudi, Yehova ali ndi gulu lankhondo losiyana kwambiri limene lidzawononga opandukira ulamuliro wake m’chilengedwe chonse.
“Yehova wa Makamu”
Baibulo limagwiritsira ntchito mawu akuti “Yehova wa makamu” nthaŵi zoposa 250. Mawuwo kwenikweni amanena za malo a Mulungu monga kazembe wa khamu lalikulu la angelo. Panthaŵi ina mneneri Mikaya anauza Mfumu Ahabu ndi Mfumu Yehosafati kuti: “Ndinaona Yehova alikukhala pampando wake wachifumu, ndi khamu lonse [“gulu lonse lankhondo,” NW] la Kumwamba lili chilili m’mbali mwake, kudzanja lamanja ndi lamanzere.” (1 Mafumu 22:19) Pano akutchula magulu ankhondo a angelo. Yehova anagwiritsira ntchito magulu ameneŵa potetezera anthu ake. Mzinda wa Dotana utazingidwa ndi asilikali, mnyamata wa Elisa anataya chiyembekezo. Komabe, kuti amlimbikitse, Mulungu anamuonetsa masomphenya ozizwitsa a gulu lake lankhondo la zolengedwa zauzimu. “Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magareta amoto.”—2 Mafumu 6:15-17.
Kodi zochitika zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu amachirikiza magulu ankhondo lerolino? Magulu ena ankhondo m’Dziko Lachikristu angamanene kuti ali magulu a Mulungu. Ambiri apempha atsogoleri achipembedzo kuwadalitsa. Koma magulu ankhondo a Dziko Lachikristu nthaŵi zambiri amamenyana iwo okha, kumenyana ndi okhulupirira anzawo. Nkhondo zadziko ziŵiri za m’zaka za zana lino zinayambira pakati pa magulu ankhondo odzinenera kuti ndi achikristu. Zimenezi sizingakhale zochita za Mulungu. (1 Yohane 4:20) Pamene kuli kwakuti magulu ankhondo ameneŵa angamanene kuti akumenyera mtendere, kodi Yesu analangiza otsatira ake kusonkhanitsa magulu otero pofuna kutsekereza zinthu zofuna kusokoneza mtendere padziko lapansi?
Mtendere unasokonezedwa kwambiri pamene khamu la anthu okhala ndi zida anagwira Yesu m’munda mmene anali kupemphera ndi ophunzira ake. Mmodzi wa ophunzirawo anakantha mwamuna wina wa m’khamulo ndi lupanga. Yesu anagwiritsira ntchito chochitikacho kufotokoza pulinsipulo lofunika kwambiri. Iye anati: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga. Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri?” Yesu anali mkulu wa gulu lankhondo lalikulu kwambiri, koma Petro sanalembedwe usilikali m’gululo, ndipo palibe munthu aliyense amene walembedwa. M’malo mwake, Petro ndi otsatira a Yesu ena onse anali ataitanidwa kuti akhale “asodzi a anthu.” (Mateyu 4:19; 26:47-53) Patapita maola ochepa, Yesu anammasulira Pilato nkhaniyo. Iye anati: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.” (Yohane 18:36) Mosiyana ndi ufumu wa Davide umene unakhazikitsidwa padziko lapansi, Ufumu umene Mulungu wapatsa Yesu uli kumwamba ndipo uzadzetsa mtendere padziko lapansi.
Magulu Ankhondo a Mulungu Aloŵa m’Nkhondo
Magulu ankhondo a Mulungu adzachitapo kanthu posachedwapa. Pofotokoza nkhondo imene ili mtsogolomu, Chivumbulutso chikutcha Yesu kuti “Mawu a Mulungu.” Timaŵerenga kuti: “Magulu ankhondo okhala m’Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbu. Ndipo m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu.” Baibulo limanena kuti nkhondo imeneyi idzathetsa “mafumu a dziko, ndi magulu ankhondo awo.” Ponena za ena amene akulephera kukhala okhulupirika kwa Mulungu, ulosiwo umawonjezera kuti: “Otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo.” Ngakhale Satana Mdyerekezi adzatha ntchito. Zimenezi zidzachititsadi kuti dziko lapansi likhale lamtendere popanda magulu ankhondo.—Chivumbulutso 19:11-21; 20:1-3.
Talingalirani za Dziko Lopanda Nkhondo
Kodi mungathe kuyerekezera m’maganizo dziko lachisungiko kwambiri moti magulu ankhondo sadzafunika? Salmo la Baibulo limati: “Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa padziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.”—Salmo 46:8, 9.
Zimenezi zidzakhala zopumulitsa chotani nanga! Talingalirani za zimene anthu adzatha kuchita amene pomalizira pake amasulidwa ku mtolo wolemaza wa kulipirira magulu ankhondo ndi zida zawo! Anthu adzatha kugwiritsira ntchito nyonga yawo kuti akonze kakhalidwe ka munthu aliyense, kuyeretsa dziko lapansi ndi kubzalamonso zomera zake. Padzakhala mpata watsopano wopanga zinthu zimene zidzakhala zothandizadi kwa mtundu wa anthu.
Pangano limeneli lidzakwaniritsidwa padziko lonse lapansi: “Chiwawa sichidzamvekanso m’dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m’malire ako.” (Yesaya 60:18) Sikudzakhalanso mamiliyoni a anthu osoŵa chochita othaŵa kwawo kumene kuli nkhondo, kuthaŵa nyumba zawo ndi katundu wawo kukakhala m’misasa yosautsa. Anthu sadzaliranso chifukwa cha okondedwa awo ophedwa kapena olemazidwa m’nkhondo za mitundu. Mfumu yakumwamba ya Yehova idzakhazikitsa mtendere wosatha padziko lapansi. “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Adzawombola moyo wawo kuchinyengo ndi chiwawa.”—Salmo 72:7, 14.
Ndiponso chosangalatsa kwambiri chidzakhala kukhala ndi moyo pakati pa anthu amene aphunzira kutsanzira njira za Mulungu za chikondi, osati kudana. Mawu a Mulungu amaneneratu kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” Kodi zidzakhala motani kukhala pakati pa anthu odziŵa Yehova ndiponso amene amamkonda? Buku limodzimodzilo limalosera kuti: “Ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthaŵi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala m’malo amtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.”—Yesaya 11:9; 32:17, 18.
Anthu amene chikhulupiriro chawo chamangidwa pachidziŵitso cha m’Baibulo ngozindikira kuti magulu ankhondo a Mulungu ali okonzekera kusesa adani onse a mtendere padziko lapansi. Chidziŵitso chimenechi chimawapatsa chidaliro cha kuchita zimene Baibulo limanena kuti ‘zidzakhalako m’masiku otsiriza.’ Ndipo ndizo izi: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:2-4.
Anthu ochokera m’mitundu yambiri amene akhala Mboni za Yehova akupeŵa ‘kuphunzira nkhondo’ panopo. Iwo akudalira chitetezo cha magulu ankhondo akumwamba a Mulungu. Mwa kuphunzira nawo Baibulo, inunso mungakhale ndi chidaliro chofananacho.
[Mawu a Chithunzi patsamba 28]
Chithunzithunzi cha U.S. National Archives