Msonkhano wa 1998-1999 wa “Njira ya Moyo ya Mulungu” Wayandikira!
KU United States kokha kudzakhala misonkhano yachigawo yokwanira 198 yomwe idzachitika kuyambira m’May mpaka m’September. Mosakayika konse, umodzi mwa misonkhano ya masiku atatu imeneyi udzachitika m’dera lapafupi ndi kwanuko. M’madera ambiri, tsiku lililonse—kuyambira Lachisanu mpaka Lamlungu—programu izidzayamba ndi nyimbo panthaŵi ya 9:30 mmaŵa.
Programu ya Lachisanu mmaŵa idzafotokoza za malipoti a kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira Ufumu m’maiko osiyanasiyana a dziko lapansi. Ndipo mutu wamsonkhanowo udzagogomezeredwa ndi nkhani yaikulu yakuti, “Dipo la Kristu—Njira ya Mulungu ya Chipulumutso.”
Masana, nkhani yosiyirana yakuti, “Makolo—Phunzitsani Ana Anu Njira ya Mulungu,” idzapereka malingaliro a mmene mungalimbikitsire ana anu kukonda ndi kutumikira Yehova. Programu yamasanayo idzamaliza ndi nkhani yakuti, “Kodi Moyo Umakhalakobe Pambuyo pa Imfa?”
Programu ya Loŵeruka mmaŵa idzafotokoza za ntchito ya Mboni za Yehova yopanga ophunzira, ndipo idzakhala ndi mbali zitatu zotsatizana zakuti, “Kuthandiza Anthu Kuyenda m’Njira ya Moyo,” “Ntchito Yovuta ya Kufikira Anthu,” ndiponso “Kuphunzitsa Ophunzira Zinthu Zonse Zimene Kristu Analamulira.” Pamapeto a programu yammaŵayo, padzakhala makonzedwe a kubatiza ophunzira atsopano.
Nkhani yoyamba ya Loŵeruka masana yakuti, “Kutumikira Kufikira Moyo Wosatha,” idzatilimbikitsa kuti tizisinkhasinkha mwapemphero pazifukwa zimene timatumikirira Mulungu. Nkhani zakuti, “Kuyamikira ‘Mphatso mwa Amuna,’ Amene Amaphunzitsa Njira ya Mulungu,” ndi “Umunthu—Vulani Wakale Ndipo Valani Watsopano,” zidzatiunikira mwa kusanthula vesi lililonse la Aefeso chaputala 4. Kenaka, uphungu wabwino wa m’Malemba udzaperekedwa m’nkhani yakuti, “Khalani Osachititsidwa Maŵanga ndi Dziko” ndiponso m’nkhani yosiyirana yambali zitatu yakuti, “Achinyamata—Tsatirani Njira ya Mulungu.” Programu yamasana idzamaliza ndi nkhani yakuti, “Mlengi—Umunthu Wake ndi Njira Zake.”
Programu ya Lamlungu mmaŵa idzakhala ndi nkhani yosiyirana yambali zitatu imene idzafotokoza za machaputala omaliza a buku la m’Baibulo la Ezekieli ndipo idzafotokozanso za kukwaniritsidwa kwa maulosi ake. Programu yammaŵayo idzamaliza ndi seŵero la nthaŵi zakale lonena za kukhulupirika kwa anyamata atatu achihebri. Nkhani yaikulu yamsonkhanowo masana idzakhala nkhani yapoyera yakuti, “Njira Yokha ya Moyo Wosatha.”
Ndithudi, mudzapindula mwauzimu mutadzapezekapo masiku onse atatuwo. Mudzalandiridwa mwachimwemwe paprogramu yonse yamsonkhanowo, imene mudzangomvetsera kwaulere. Kuti mudziŵe malo a msonkhano a pafupi ndi kwanuko, kafunseni ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yapafupi ndi kwanuko kapena lemberani ofalitsa magazini ino.