Anachita Chifuniro cha Yehova
Paulo Achitira Umboni Molimba Mtima Pamaso pa Zinduna
AMUNA aŵiriwo anali osiyana kotheratu. Wina anavala chisoti chachifumu pamene winayo anali mu unyolo. Wina anali mfumu; winayo, wandende. Atakhala m’ndende kwa zaka ziŵiri, mtumwi Paulo anakaonekera pamaso pa mtsogoleri wa Ayuda, Herode Agripa II. Mfumuyo ndi mkazi wake, Bernike, anafika ‘ndi chifumu chachikulu, ndipo analoŵa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao aakulu, ndi amuna omveka a mudziwo.’ (Machitidwe 25:23) Buku lina limati: “Payenera kuti panafika anthu mazana angapo.”
Kazembe wongoikidwa kumeneyo, Festo, ndiye anaitanitsa msonkhanowo. Kazembe amene anamtulira udindowo, Felike, anali wokhutira kuti Paulo azingovutika m’ndendemo. Koma Festo anakayikira zifukwa zoikira Paulo m’ndende. Inde, Paulo iyemwini anali kulimbikira kunena kuti sanalakwe ndipo anapempha kuti akaonekere pamaso pa Kaisara! Mlandu wa Paulo unachititsa chidwi Mfumu Agripa. “Ndifuna nanenso ndimve munthuyo,” iye anatero. Mosataya nthaŵi, Festo anayamba kukonzekera za kukumanaku, mwina akumafunitsitsa kuti akamve zimene mfumuyo ikanene kwa wandende wodabwitsayu.—Machitidwe 24:27–25:22.
Tsiku lotsatira, Paulo anaonekera pamaso pa akuluakulu ambiri a boma. “Ndidziyesera wamwayi . . . popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu,” iye anatero kwa Agripa, “makamaka popeza mudziŵitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.”—Machitidwe 26:2, 3.
Paulo Adzikanira Molimba Mtima
Choyamba, Paulo anauza Agripa kuti kale ankazunza Akristu. ‘Ndinawakakamiza anene zamwano,’ iye anatero. “Ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.” Kenaka Paulo ananenanso za mmene anaonera masomphenya ochititsa chidwi pamene Yesu woukitsidwayo anamfunsa kuti: “Undilondalonderanji ine? Nkukuvuta kutsalima pachothwikira.”a—Machitidwe 26:4-14.
Kenaka Yesu anatuma Saulo kuti akhale mboni kumitundu yonse “ya izi wandionamo ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe.” Paulo anafotokoza kuti anali kuyesetsa kukwaniritsa ntchito yakeyo. Komatu “chifukwa cha izi Ayuda anandigwira m’Kachisi, nayesa kundipha,” iye anauza Agripa motero. Pogwiritsira ntchito chidwi cha Agripa ndi Chiyuda, Paulo anagogomezera kuti paumboni wake ‘sananene kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika’ zokhudza imfa ndi kuukitsidwa kwa Mesiya.—Machitidwe 26:15-23.
Festo anamdula mawu nafuula kuti: “Kuŵerengetsa kwako kwakuchititsa misala”! Paulo anayankha kuti: “Ndilibe misala, Festo womvekatu; koma nditulutsa mawu a choonadi ndi odziletsa.” Kenaka Paulo anati ponena za Agripa: “Mfumuyo idziŵa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziŵadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitika m’tseri.”—Machitidwe 26:24-26.
Kenaka Paulo analankhula mwachindunji kwa Agripa. “Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi?” Mosakayika funsoli linamzunguza Agripa. Vuto linali lakuti, anafuna kudzisungira dzina lake, chotero, kuvomerezana ndi Paulo kukanakhala ngati nayenso ‘ngwamisala’ malinga nzimene Festo ananena. Mwinamwake ataona kuti Agripa akuzengereza, Paulo anadziyankhira funso lake. ‘Ndidziŵa kuti muwakhulupirira,’ iye anatero. Kenaka Agripa analankhulapo, koma anayesetsa kulankhula mosasonyeza kuti akugwirizana naye. “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu,” iye anatero kwa Paulo.—Machitidwe 26:27, 28.
Pofotokoza mfundo yofunika, Paulo anagwiritsira ntchito mwaluso mawu a Agripa ofuna kuzemba. Iye anati: “Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang’ono, kapena ndi kukopa kwambiri, siinu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.”—Machitidwe 26:29.
Agripa ndi Festo anaona kuti Paulo analibe chifukwa chomuphera kapena kumuikira m’ndende. Komabe, iwo sanafune kunyalanyaza pempho lake lakuti akaonekere pamaso pa Kaisara. Nchifukwa chake Agripa anati kwa Festo: “Tikadakhoza kumasula munthuyu, akadapanda kunena, Ndikatulukira kwa Kaisara.”—Machitidwe 26:30-32.
Phunziro kwa Ife
Umboni wa Paulo pamaso pa akuluakulu a boma uli chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife. Polankhula kwa Mfumu Agripa, Paulo anali kulankhula mwanzeru. Mosakayika iye anadziŵa bwino vuto limene linalipo pakati pa Agripa ndi Bernike. Iwo anakwatirana pachibale, popeza kuti kwenikweni Bernike anali mlongo wake wa Agripa. Koma panthaŵiyi Paulo sanafune kulankhula za makhalidwe abwino. M’malo mwake, iye anagogomezera nkhani zimene iye ndi Agripa anali kuzidziŵa. Ndiponso, ngakhale kuti Paulo anaphunzitsidwa ndi Mfarisi wophunzira bwino Gamaliyeli, iye anavomereza kuti Agripa anali katswiri wa mwambo wachiyuda. (Machitidwe 22:3) Mosasamala kanthu za makhalidwe a Agripa, Paulo analankhula naye mwaulemu chifukwa chakuti Agripa anali wolamulira.—Aroma 13:7.
Tikamachitira umboni molimba mtima za zikhulupiriro zathu, sitiyenera kuvumbula kapena kutsutsa makhalidwe oipa a omvetsera athu. M’malo mwake, pofuna kuti iwo alandire choonadi mosavuta, tiyenera kugogomezera za mbali zolimbikitsa za uthenga wabwino, tikumafotokoza bwino za ziyembekezo zimene ifeyo ndi iwowo timazidziŵa. Tikamalankhula ndi anthu achikulire kapena anthu olemekezeka, tiyenera kulemekeza udindo wawo. (Levitiko 19:32) Tikatero, tidzatsanzira Paulo, amene anati: “Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.”—1 Akorinto 9:22.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu akuti “kutsalima pachothwikira” akufotokoza za mmene ng’ombe yamagoli imadzivulazira ngati itsalimira patsatsa loŵaŵa. Mofananamo, pamene anali kuzunza Akristu, Saulo akanangodzipweteka, popeza kuti anali kumenyana ndi anthu omwe anali kuchirikizidwa ndi Mulungu.