Kodi Muli ndi Mngelo Wokuyang’anirani?
KODI mumakhulupirira kuti muli ndi mngelo amene amakuyang’anirani? Anthu ambiri amakhulupirira kuti ali naye. Mwachitsanzo, mkazi wina kumadzulo kwa Canada akuti ali ndi mphatso yapadera yolankhula ndi angelo. Iye amati mutamuuza maina anu onse ndi kumpatsa $200, angakuthandizeni kulankhula ndi mngelo wanu wokuyang’anirani. Choyamba, amayang’ana dwii laŵi la kandulo. Kenako, amaona masomphenya a mngelo wanu amene amampatsira uthenga wanu. Kungokuthandizani, mkaziyo amakujambulirani maonekedwe a mngelo wanu.
Kwa ena, zimenezi zangofanana ndi nthano yonena za Mfumu Louis IX ya ku France. Nthanoyo imati iye anagula nthenga zamtengo wapatali kwambiri zimene amati zinagwa kuchokera kumapiko a Mngelo Wamkulu Mikayeli. Pamene kuli kwakuti nthanoyo amaikayikira, ambiri samakayikira mpang’ono pomwe zonena za mkazi wa ku Canada ameneyo.
Kuchita Chidwi ndi Angelo
M’zaka zino, anthu ambiri achita chidwi ndi angelo. Pawailesi yakanema ndi m’mafilimu, m’mabuku, m’magazini, m’manyuzipepala, timamva za angelo amene amatonthoza odwala matenda akayakaya, kutonthoza ofedwa, kupereka nzeru, ndi kupulumutsa anthu ku imfa. Ku United States, anthu ngati 20 miliyoni amaonerera pologalamu ina ya mlungu ndi mlungu pawailesi yakanema imene imasonyeza zochita za angelo pamoyo wa anthu. Sitolo ina yamabuku ili ndi mabuku oposa 400 onena za angelo basi.
Buku lina laposachedwapa likusimba mmene angelo oyang’anira anapulumutsira miyoyo ya asilikali m’nkhondo. Timapepala tomatidwa pagalimoto timanena kuti woyendetsa galimotoyo akutetezedwa ndi mngelo woyang’anira. Mabungwe, misonkhano, ndi maseminale amalimbikitsa anthu kuti aziphunzira za angelo ndipo akuti maguluwo amathandiza anthu kulankhula ndi angelowo.
Eileen Freeman walemba mabuku atatu onena za angelo ndipo ndi wofalitsa wa magazini ina yongonena za angelo. Iye akuti: “Ndikhulupirira kuti mngelo aliyense wa kumwamba ali ndi mngelo mnzake woyang’anira Padziko Lapansi, amene ntchito yake sindiyo kutamanda Mulungu kwenikweniko kumwamba koma kusamalira anthu ndi zamoyo zina mwachindunji Padziko Lapansi. Mngelo woyang’anira amagaŵiridwa kwa aliyense wa ife mayi wathu akangokhala ndi pathupi pathu ndipo amatiyang’anira tikumakula m’mimbamo, pamene tikubadwa, pamoyo wathu wonse m’dziko lapansili, mpaka mngeloyo amatitsogolera kuchoka m’dzikoli kukaloŵa mu ulemerero wakumwamba.” Mawuwa akufotokoza bwino zimene anthu ambiri amaganiza ponena za angelo oyang’anira.
M’nthaŵi zovutazi, nkotonthoza kukhulupirira kuti tili ndi mngelo wathu wotiyang’anira, amene ntchito yake ndiyo kutiteteza. Kodi Mawu a Mulungu, Baibulo, amatipo bwanji pankhaniyi? Kodi tiziyesa kulankhula ndi angelo? Kodi amasamala za makhalidwe athu ndi zikhulupiriro zathu zachipembedzo? Kodi tingayembekeze thandizo lotani kwa iwo? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.