Kodi Tingakhale ndi Moyo Kwautali Wotani?
Anthu mochulukirachulukira akukhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali, zomwe zikupangitsa ambiri kudabwa kuti, ‘Kodi tingakhale ndi moyo kwautali wotani?’
MALINGA ndi kunena kwa The New Encyclopædia Britannica (1995), kale anthu anali kukhulupirira kuti Pierre Joubert ndiye amene anakhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali kwambiri. Mu 1814 iye anafa ali ndi zaka 113. Zoona, alipo ena amene amanenedwa kuti anakhala ndi moyo kuposera pamenepo, koma zaka zawo sizinalembedwe bwino koti ndi kuzikhulupirira. Komabe, zolembedwa zolongosoka zatsimikizira kuti anthu ambiri anakhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali kuposa Pierre Joubert.
Jeanne Louise Calment anabadwira ku Arles, kummwera chakummaŵa kwa France, pa February 21, 1875. Imfa yake pa August 4, 1997—zaka zoposa 122 pambuyo pake—inafalitsidwa kwambiri. Mu 1986, Shigechiyo Izumi wa ku Japan anamwalira ali ndi zaka 120. Guinness Book of Records 1999 likutchula Sarah Knauss wazaka 118 kukhala munthu wakale kwambiri panthaŵi imene bukulo linali kulembedwa. Iye anabadwa pa September 24, 1880 ku Pennsylvania, U.S.A. Pamene Marie-Louise Febronie Meilleur wa ku Quebec, Canada, anamwalira mu 1998 ali ndi zaka 118, anali wamkulu kwa Sarah ndi masiku 26.
Ndithudi, chiŵerengero cha anthu okalamba kwambiri chakwera zedi. Chiŵerengero cha anthu okwanitsa zaka zana ali ndi moyo chikuyerekezeredwa kuti chidzawonjezeka kufika pa 2.2 miliyoni mkati mwa theka loyamba la zaka za zana lotsatirali! Mofananamo, chiŵerengero cha anthu azaka 80 ndi kuposerapo chinawonjezeka kuchoka pa 26.7 miliyoni mu 1970 kufika pa 66 miliyoni mu 1998. Chimenecho ndi chiwonjezeko cha 147 peresenti, pochiyerekezera ndi chiwonjezeko cha 60 peresenti cha anthu onse padziko lapansi.
Ndipo sichabe kuti anthu akukhala ndi moyo zaka zambiri. Ambiri akuchitanso zinthu zimene achinyamata ambiri azaka 20 sangathe kuchita. Mu 1990, John Kelley wazaka 82 anathamanga liŵiro lamtondo wadooka—mtunda wa makilomita 42.195—mu maola asanu ndi mphindi zisanu. Mu 1991, gogo wamkazi Mavis Lindgren wazaka 84, anathamanga mtunda umenewo mu maola asanu ndi aŵiri ndi mphindi zisanu ndi zinayi. Ndipo posachedwa kwambiri, mwamuna wina wazaka 91 anamaliza mtunda wa mpikisano wa New York City Marathon!
Zimenezi sizikutanthauza kuti kalelo anthu okalamba sanachite zinthu zodabwitsa. Abrahamu, kholo la m’Baibulo, pamene anali ndi zaka 99 ‘anathamanga kukakomana’ ndi alendo ake. Ali ndi zaka 85, Kalebe anati: “Monga mphamvu yanga pamene paja [zaka 45 m’mbuyomo], momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kutuluka ndi kuloŵa.” Ndipo Baibulo limati Mose pamene anali ndi zaka 120, “diso lake silinachita mdima, ndi mphamvu yake siidaleka.”—Genesis 18:2; Yoswa 14:10, 11; Deuteronomo 34:7.
Yesu Kristu anatchula za munthu woyambayo, Adamu, ndiponso munthu amene anapanga chingalawa Nowa kuti anali anthu osaiŵalika. (Mateyu 19:4-6; 24:37-39) Buku la Genesis limati Adamu anakhala ndi moyo zaka 930, ndipo Nowa zaka 950. (Genesis 5:5; 9:29) Kodi anthu anakhaladi ndi moyo kwautali woterowo? Kodi ife tingakhale ndi moyo kuposera pamenepo, mwinamwake kosatha? Chonde fufuzani umboni wa zimenezi m’nkhani yotsatirayi.