Msonkhano wa Pachaka October 2, 1999
MSONKHANO WA PACHAKA wa mamembala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitika pa October 2, 1999, pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, pa 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, ku New Jersey. Kukumana koyambirira kwa mamembala okhaokha kudzakhalako pa 9:15 a.m., motsatiridwa ndi msonkhano wa onse wa pachaka pa 10:00 a.m.
Mamembala a Bungweli ayenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano lino za kusintha kulikonse kwa makeyala awo a makalata mkati mwa chaka chapita kotero kuti iwo adzathe kulandira makalata odziŵitsa anthaŵi zonse ndi mapepala a voti m’July.
Mapepala a voti, amene adzatumizidwa kwa mamembalawo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pachaka, ziyenera kubwezedwa kotero kuti zidzafike ku Ofesi ya Mlembi wa Sosaite pasanafike pa August 1. Membala aliyense ayenera kudzaza ndi kutumiza pepala lake la voti mofulumira, akumafotokoza kuti kaya adzapezeka pamsonkhanowo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa pepala la voti lililonse chiyenera kukhala chotsimikizirika pamfundoyi, popeza kuti chidzakhala chodziŵira amene adzapezekapo.
Kukuyembekezeredwa kuti pologalamu yonse, kuphatikizapo msonkhano wa kayendetsedwe ka zinthu ndi malipoti, zidzamalizidwa pa 1:00 p.m. kapena kupitirira pang’ono pamenepo. Sipadzakhala pologalamu yamasana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, okhala ndi matikiti okha ndiwo amene adzaloledwa kuloŵa. Sipadzapangidwa makonzedwe akugwirizanitsa matelefoni ndi nyumba zina zosonkhanira pamsonkhano wa pachakawo.