Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Ulosi wa Baibulo
MFUMU PYRRHUS ya ku Epirus kumpoto chakumadzulo kwa Girisi inali pankhondo kwanthaŵi yaitali ndi Ufumu wa Roma. Pofunitsitsa kudziŵa za zotsatira zake, anapita ku kachisi wa ku Delphi. Koma yankho limene anamuuza linali lotheka kulimva mwa njira ziŵirizi: (1) “Ndikuuza iwe mwana wa Æacus udzagonjetsa Aroma. Udzapita, udzabwerako, sudzaphedwa konse kunkhondo.” (2) “Ndikuuza kuti Aroma angakugonjetse iwe mwana wa Æacus. Udzapita, sudzabwerako, udzafera kunkhondo.” Iye anasankha loyambalo ndipo anakamenya nkhondo ndi Roma. Pyrrhus anagonjetsedwa kotheratu.
Zochitika ngati zimenezi zinachititsa mayankho a alauli akale kukhala ndi mbiri yoipa chifukwa anali ovuta kuzindikira komanso okuluŵika. Koma bwanji za ulosi wa Baibulo? Otsutsa ena amanenabe kuti maulosi a m’Baibulo sasiyana konse ndi zonena za alauli akale. Otsutsa amenewa amanena kuti maulosi a Baibulo analoseredwa mwamachenjera chabe ndi anthu anzeru ndi luntha, makamaka apabanja la ansembe. Iwo amakhulupirira kuti chifukwa chabe cha nzeru zawo kapena anthu amene ankagwirizana nawo kwambiri, amuna amenewa analosera mmene zochitika zina zidzathera. Tikayerekeza mbali zosiyanasiyana za maulosi a Baibulo ndi zonena za alauli amenewo, tidzakhala okonzeka kufika pa mfundo zoyenera.
Kusiyana Kwake
Zonena za alauli zinkadziŵika kukhala zovuta kuzindikira. Mwachitsanzo, ku Delphi, mayankho ankaperekedwa m’mawu osatheka kuwamva. Zimenezi zinachititsa kuti ansembe aziwamasulira komanso kutchula mawu otheka kutanthauza zinazina. Chitsanzo chabwino ndi yankho lomwe Croesus, mfumu ya Lidiya, analandira. Pamene anapita kukafunsira ku kachisi, anauzidwa kuti: “Ngati Croesus adzawoloka mtsinje wa Halys, adzagonjetsa ufumu wamphamvu.” Komano, “ufumu wamphamvu” umene unagonjetsedwa unali wakewo! Pamene Croesus anawoloka mtsinje wa Halys kuti akalande Kapadokiya, anagonja kwa Koresi mfumu ya Perisiya.
Mosiyana ndi mayankho achikunja a alauli, maulosi a Baibulo amadziŵika bwino chifukwa cha kumveka ndi kulondola kwake. Mwachitsanzo, ulosi wonena za kugwa kwa Babulo, wolembedwa m’buku la Baibulo la Yesaya. Zaka 200 zimenezi zisanachitike, mneneri Yesaya analosera mwatsatanetsatane ndi mosaphonya zakuti Babulo akagonjetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi. Ulosiwo unanena kuti wopambanayo dzina lake lidzakhala Koresi, ndipo unaneneratunso za njira zomwe adzagwiritsira ntchito poloŵa mumzinda wamalingawo monga kuphwetsa mtsinje wozama wachitetezo wonga chemba ndi kutinso zipata zidzakhala zotseguka. Zonse zimenezi zinachitikadi. (Yesaya 44:27–45:2) Analoseranso molondola kuti anthu sadzakhalanso m’Babulo kunthaŵi yonse.—Yesaya 13:17–22.
Taganiziraninso za chenjezo losapita m’mbali la mneneri Yona lakuti: “Atsala masiku makumi anayi ndipo Nineve adzapasuka.” (Yona 3:4) Palibe chosamveka pamenepa! Uthengawo unali wochititsa nthumazi komaso wosapita m’mbali moti anthu a ku Nineve mwamsanga “anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli.” Chifukwa cha kulapa kwawo, Yehova sanabweretse chiwonongeko kwa Anineve panthaŵiyo.—Yona 3:5-10.
Zonena za alauli ankazigwiritsa ntchito monga chokopera anthu pandale. Olamulira ndi atsogoleri azankhondo kaŵirikaŵiri anali kugwira mawu yankho la mlauli limene linawakomera pofuna kulimbikitsa zolinga zawozawo, ndipo mwa kuchita zimenezo ankapereka chithunzi chakuti “anaikidwa ndi milungu.” Koma mauthenga aulosi a Mulungu anaperekedwa mosaganizira munthu.
Mwachitsanzo: Natani mneneri wa Yehova sanaleke kudzudzula Mfumu Davide yolakwayo. (2 Samueli 12:1-12) Panthaŵi ya ulamuliro wa Yerobiamu Wachiŵiri pa ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi, mneneri Hoseya ndi Amosi anadzudzula mwamphamvu mfumu yopandukayo ndi anthu ake chifukwa cha mpatuko ndi makhalidwe awo oipa osalemekeza Mulungu. (Hoseya 5:1-7; Amosi 2:6-8) Makamaka chenjezo la Yehova kwa mfumuyo mwa mawu a mneneri Amosi linali loŵaŵa zedi. Anati: “Ndidzaukira nyumba ya Yerobiamu ndi lupanga.” (Amosi 7:9) Ndipo nyumba ya Yerobiamu inasakazidwa.—1 Mafumu 15:25-30; 2 Mbiri 13:20.
Kaŵirikaŵiri, alauli popereka mauthenga awo anali kulipiritsa. Yemwe amapereka ndalama zambiri ndiye amalandira mayankho abwino. Omwe amapita kukafunsira ku kachisi ku Delphi amalipira ndalama zambiri pa mayankho opanda pake, akumasiya chuma chambiri kukachisi wa Apollo ndi nyumba zina. Kusiyana ndi zimenezo, maulosi ndi machenjezo a Baibulo anaperekedwa kwa onse mosalipiritsa ndiponso mopanda tsankho lililonse. Zinali choncho mosasamala kanthu za udindo kapena chuma chimene munthuyo anali nacho, pakuti mneneri woona sankalandira ziphuphu. Samueli mneneri komanso woweruza anafunsa modzichepetsa kuti: “Ndinalandira m’manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga?”—1 Samueli 12:3.
Popeza kuti mayankho a alauli ankapezeka kumalo akutiakuti, munthu wofuna mayankhowo anayenera kupanga ulendo wautali zedi. Kwa anthu wamba zinali zovuta kwambiri kukafika kumalo amenewo chifukwa anali malo monga Dodona pa Phiri la Tomarus ku Epirus ndi Delphi m’mapiri m’chigawo chapakati cha Girisi. Kaŵirikaŵiri, olemera ndi olamulira okha ndiwo amapita kukafunsira kwa milungu ku akachisi amenewo. Komanso, “chifuno cha milungu” chinali kuvumbulidwa kwa anthu pa masiku oŵerengeka pachaka. Mosiyana kwambiri, Yehova Mulungu anatumiza mauthenga ake aulosi mwachindunji kwa anthu kuti alalikire maulosiwo amene iwo anafunikira kumva. Mwachitsanzo, panthawi ya ukapolo wa Ayuda ku Babulo, Mulungu anali ndi aneneri osachepera atatu kwa anthu ake—Yeremiya ku Yerusalemu, Ezekieli kwa akapolo, komanso Danieli kulikulu la Ufumu wa Babulo.—Yeremiya 1:1, 2; Ezekieli 1:1; Danieli 2:48.
Alauli anali kupereka mayankho awo mtseri kuti iye wakuwalandira awagwiritse ntchito malinga ndi kufuna kwake kuti akwaniritse zolinga zake. Mosiyana ndi zimenezo, maulosi a Baibulo ankaperekedwa poyera kuti aliyense amve uthenga ndi kumvetsa tanthauzo lake. Mneneri Yeremiya nthaŵi zambiri anali kulankhula poyera ku Yerusalemu ngakhale anadziŵa kuti uthenga wake sakaulandira atsogoleri komanso anthu a mumzindawo.—Yeremiya 7:1, 2.
Lero, zonena za alauli zimaoneka kukhala mbiri yakale. Zilibe phindu kwa anthu m’masiku ovuta ano. Palibe ngakhale chimodzi mwa zonena zawozo zimene zimakhudza za m’tsiku lathu kapena tsogolo lathu. Mosiyana kwambiri ndi zimenezi, Maulosi a Baibulo ali mbali ya “mawu a Mulungu [amene] ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Maulosi a Baibulo amene anakwaniritsidwa kale amasonyeza ndondomeko ya mmene Yehova amachitira ndi anthu komanso amavumbula chifuno chake ndi umunthu wake. Kuwonjezera pamenepa, maulosi ena ofunika a Baibulo adzakwaniritsidwa posachedwapa m’tsogolo. Pofotokoza za m’tsogolo, mtumwi Petro analemba kuti: “Monga mwa lonjezano lake [la Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano [Ufumu wa Mesiya wakumwamba], ndi dziko latsopano [anthu olungama] m’menemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13.
Kuyerekeza kwachidule kumeneku ulosi wa Baibulo ndi zonena za alauli achipembedzo chonyenga kungakuthandizeni kugamulapo monga momwe buku lakuti The Great Ideas limanenera kuti: “Pankhani yokhudza kudziŵiratu zam’tsogolo kwa anthu okhoza kufa, aneneri achihebri anali apaderadera. Mosiyana ndi alauli achikunja, . . . iwo sanagwiritse ntchito matsenga kapena chenjerero kuti atulukire zinsinsi zaumulungu. . . . Mosiyana ndi zonena za alauli, maulosi awo ambiri ali omveka bwino. Zikuoneka kuti cholinga chake sichinali kubisa koma kuulula zolinga za Mulungu monga momwe Iye Mwini akufunira kuti anthu adziŵe mmene mphamvu yake imayendetsera zinthu.”
Kodi Mudzakhulupirira Ulosi wa Baibulo?
Mungathe kukhulupirira ulosi wa Baibulo. Ndiiko komwe Yehova angakhale wofunika kwambiri m’moyo wanu komanso kukwaniritsidwa kwa mawu ake aulosi. Ulosi wa Baibulo si mbiri ya zinthu zonenedweratu zotha ntchito zimene zinakwaniritsidwa kale. Maulosi ambiri opezeka m’Malemba akukwaniritsidwa tsopano kapena adzakwaniritsidwa posachedwa pompa. Malinga ndi zochitika mmbuyomu, tili ndi chikhulupiriro chakuti nawonso adzakwaniritsidwa. Popeza kuti maulosi amenewa amanena za m’nthaŵi yathu komanso za tsogolo lathu, tiyenera kuwaona kukhala ofunika.
Ndithudi mungakhulupirire ulosi wa Baibulo wa pa Yesaya 2:2, 3 wakuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, . . . Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, . . . ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” Lero, anthu miyandamiyanda akulandira ndi mtima wonse kulambira kokwezeka kwa Yehova ndipo akuphunzira kuyenda m’mayendedwe ake. Kodi inu mudzapeza nawo mwayi wakuphunzira mokwana za njira za Mulungu ndi kupeza chidziŵitso cholongosoka chonena za zifuno zake kuti muyende m’mayendedwe ake?—Yohane 17:3.
Kukwaniritsidwa kwa ulosi wina wa Baibulo kumafuna kuti tichite changu. Ponena za patsogolopa, wamasalmo anaimba nyimbo yolosera kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa . . . Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti.” (Salmo 37:9, 10) Kodi mukuganiza kuti chikufunika n’chiyani kuti tipewe chiwonongeko choyandikirachi cha anthu oipa, kuphatikizapo onse amene amanyozera maulosi a Baibulo? Wamasalmo yemweyo akuyankha kuti: “Iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 37:9) Kuyembekeza Yehova kumatanthauza kuika chidaliro chonse m’malonjezo ake ndi kugwirizanitsa moyo wathu ndi miyezo yake.—Miyambo 2:21, 22.
Kodi moyo udzakhala wotani pamene oyembekeza Yehova adzalandira dziko lapansi? Panonso, ulosi wa Baibulo umavumbula kuti anthu omvera ali ndi tsogolo labwino laulemerero. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.” (Yesaya 35:5, 6) Mtumwi Yohane analemba mawu otonthoza awa: “[Yehova] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati: . . . Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:4, 5.
Mboni za Yehova zikudziŵa kuti Baibulo ndi buku la maulosi odalirika. Ndipo zimavomereza langizo la mtumwi Petro lakuti: ‘Tili nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mitima yanu.’ (2 Petro 1:19) Chikhulupiriro chathu n’chakuti mudzalimbikitsidwa ndi chiyembekezo chodabwitsa cha m’tsogolo chimene maulosi a Baibulo amapereka!
[Bokosi/Zithunzi patsamba 6]
KACHISI WA KU DELPHI anali wotchuka kwambiri ku Girisi wakale.
Nthunzi yoledzeretsa inapangitsa wansembeyo kutengeka maganizo
[Zithunzi]
Wansembe wamkazi ankakhala pa mpando wamiyendo itatu ndi kunena maulosi ake
Mawu omwe amanena ankati ndi vumbulutso lochokera kwa mulungu Apollo
[Mawu a Chithunzi]
Mpando wamiyendo itatu: Kuchokera m’buku la Dictionary of Greek and Roman Antiquities; Apollo: The Complete Encyclopedia of Illustration/J.G. Heck
[Chithunzi patsamba 7]
Maulosi omwe amaperekedwa kukachisi wa ku Delphi anali osadalirika
[Mawu a Chithunzi]
Delphi, Girisi
[Zithunzi patsamba 8]
Mungathe kukhala ndi chidaliro cholimba m’maulosi a Baibulo onena za dziko latsopano