Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 8/1 tsamba 9
  • Mboni Zifikira Anthu mu France

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni Zifikira Anthu mu France
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zotsatirapo Zabwino, Zamwamsanga
  • ‘Amakamba za Ubwino ndi Chikondi’
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Muzigwiritsa Ntchito Timapepala Pofalitsa Uthenga Wabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Tidzakhala ndi Ntchito Yapadera Yogawira Kapepala Kuyambira pa October 20 Mpaka pa November 16
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Mkupiti Wachipambano wa Uthenga wa Ufumu
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 8/1 tsamba 9

Olengeza Ufumu Akusimba

Mboni Zifikira Anthu mu France

KUYAMBIRA m’mawa wa Lachisanu pa January 29, 1999, ndi kupitirizabe kufikira kumathero a mlunguwo, Mboni za Yehova mu France zinagaŵira mofunitsitsa ndi mwachimwemwe, mathirakiti okwana 12 miliyoni okhala ndi mutu wakuti Anthu a mu France, Mukunyengedwa! Mathirakitiŵa anawagaŵira m’misewu ndipo pambuyo pake ku nyumba ndi nyumba. N’chifukwa chiyani anapanga ndawala imeneyo?

Pamsonkhano wa atolankhani umene unachitikira mumzinda wa Paris m’mawa wa tsiku limenelo, panaperekedwa chifukwa chake ndawala imeneyi inachitika. Woimira Mboni pamsonkhanowo analongosola kuti: “Chomwe ife tikufuna tsopano ndicho kudzidziŵikitsa ife eni ndi kuthetsa manong’onong’o oipitsa dzina lathu omwe akufalitsidwa. Tili ololera kutsutsidwa, koma sitidzalola kumvetsera mabodza ndi ndemanga zowononga mbiri yathu.”

Ngakhale kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova n’chachitatu pazipembedzo zazikulu zachikristu mu France, ana ambiri a Mboni akhala akuwachitira chipongwe ndi kuwavutitsa ku sukulu. Achikulire achotsedwa ntchito ndipo akhala akuopsezedwa chifukwa cha chipembedzo chawo. N’zodabwitsa kuti ngakhale pazopereka za mpingo zimene amalandira amazikhomera msonkho wa 60 peresenti. Kodi tsankho limeneli anathana nalo bwanji mwa ndawala yawoyo?

Thirakitilo linalengeza kuti: “Mboni za Yehova zokwana 250,000 ndi anzawo ogwirizana nawo okhala mu France AKUDZUDZULA mchitidwe wopanda chilungamo umene wachitidwa pa chipembedzo chawo cha Chikristu, chomwe chakhala mu France kuyambira mu 1900, wa kuwaphatikiza pamodzi ndi timagulu toopsa tampatuko kuyambira 1995. . . . KUDZUDZULA mtopola umene anthu ena apitiriza kuwachitira.” Mabodza amene Mboni zinanenezedwa mu France ndi njira zoipa zimene otsutsa anayesera kuipitsira nazo Mboni, zinaululidwa. Thirakitilo linamaliza ndi kuti: “Lerolino, Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni aŵiri ndi anzawo ogwirizana nawo akukhala mu Europe. Amalemekeza malamulo a dziko lomwe iwo akukhalamo monga nzika zake mwa kulimbikitsa makhalidwe abwino opezeka mu Uthenga Wabwino. Anthu a mu France, izitu ndizo zenizeni. Ndi udindo wathu kuzifotokoza monga m’mene zilili!”

Zotsatirapo Zabwino, Zamwamsanga

Mathirakiti ambirimbiri anagaŵiridwa tsiku loyambalo. Pofika masana, Mboni zoposa 7,000 zinali zitagaŵira anthu mathirakiti oposa 1.3 miliyoni, mu Paris mokha. Kuona Mboni zambirimbiri zikugaŵira mathirakiti m’misewu, chinali chinthu chachilendo kwa anthu. Oulutsa nkhani limodzinso ndi manyuzipepala ndi wailesi za kanema, zinalengeza bwino lomwe za ndawala imeneyi. Nyuzipepala ya Le Progrès de Lyon inati: “Njira imeneyi . . .yasonyeza poyera kusamvetsetsa tanthauzo la mawu ena. Zaka khumi zapitazo mawu akuti ‘kagulu kampatuko’  . . atanthauza kagulu kamakhalidwe oipa, koopsa, ndi kovulaza . . . Mboni za Yehova si anthu oopsa amene angasokoneze mtendere wa anthu.”

Awo amene akuzidziŵa bwino Mboni za Yehova amadziŵa kuti ndi anthu amtendere ndi olemekeza chikhalidwe ndi bata. Motero, anthu ambiri anasonyeza kuyamikira ndi kulimbikitsa Mboni zochuluka zimene zinatenga nawo mbali pandawala imeneyo. Posapita nthaŵi, matelefoni, mafakisi ndi makalata anayamba kufika kuchokera kwa anthu kuthokoza chifukwa chowapatsa mathirakitiwo. Chopambana zonse, onse okonda choonadi anapatsidwa mwayi wakumva zoona zenizeni ponena za Mboni, kusiyana ndi nkhani zopeka ndi zopanda tanthauzo. Ndipo aja amene chikhulupiro chawo chinasokeretsedwa analinso okhoza kusonyeza malingaliro awo pa zimene anaziona kukhala zofunika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena