Kodi Zaka za Chikwi Chachitatu Zidzayamba Liti?
KODI munamvapo ena akunena kuti zaka za chikwi chachitatu sizidzayamba mu chaka cha 2000 koma mu 2001? Zimenezo ndi zoona pamlingo wina wake. Tikanena kuti Yesu Kristu anabadwa m’chaka chomwe tsopano chikudziŵika kuti 1 B.C.E., monga ena analingalirira, ndiye kuti December 31, 2000 (osati 1999), adzakhaladi mapeto a zaka za chikwi chachiŵiri, ndipo January 1, 2001, chiyambi cha zaka za chikwi chachitatu.a Komabe, pafupifupi akatswiri onse a zamaphunziro amavomereza kuti Yesu Kristu sanabadwe mu 1 B.C.E. Chabwino, nanga kodi anabadwa liti?
Kodi Yesu Anabadwa Liti?
Baibulo silinena deti lenileni limene Yesu anabadwa. Komabe, ilo limati anabadwa “m’masiku a Herode mfumu.” (Mateyu 2:1) Akatswiri ambiri a Baibulo amakhulupirira kuti Herode anamwalira m’chaka cha 4 B.C.E. ndi kuti m’nthaŵi imeneyo n’kuti Yesu atabadwa kale, mwinamwake cha m’ma 5 kapena 6 B.C.E. Zomwe ananena zokhudza imfa ya Herodeyo anatengera m’zomwe wolemba mbiri wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba, Flavius Josephus anafotokoza.b
Malinga n’kunena kwa Josephus, nthaŵi itangotsala pang’ono kuti Mfumu Herode amwalire, mwezi unada pang’ono. Akatswiri a Baibulo amanena za kuda kwa mwezi kumene kunachitika pa March 11, 4 B.C.E., kukhala umboni wakuti Herode anamwaliradi m’chaka chimenecho. Komabe, pa January 8 m’chaka cha 1 B.C.E., mwezi unada kwambiri, ndipo pa December 27 unadanso pang’ono. Palibe anganene kuda kwa mwezi kumene Josephus ankatanthauza pakati pa kumene kunachitika mu 1 B.C.E. ndi kumene kunachitika mu 4 B.C.E. Choncho, sitingagwiritse ntchito mawu a Josephus ponena za chaka chenicheni chimene Herode anamwalira. Ngakhale titagwiritsa ntchito, koma popanda umboni wowonjezeka sitingadziŵebe tsiku limene Yesu anabadwa.
Umboni wamphamvu womwe tili nawo wonena za deti limene Yesu anabadwa n’ngochokera m’Baibulo. Mawu ouziridwa amati msuwani wake wa Yesu, Yohane Mbatizi anayamba ntchito yake monga mneneri m’chaka cha khumi ndi chisanu cha ulamuliro wa Mfumu ya Roma, Tiberiyo Kaisara. (Luka 3:1, 2) Mbiri imatsimikizira kuti Tiberiyo anavekedwa ufumu pa September 15, 14 B.C.E., choncho pomafika kumapeto a chaka cha 28 C.E. kapena 29 C.E anali atalamulira kwa zaka 15. Yohane anayamba utumiki wake m’nthaŵi imeneyo, ndipo mwachionekere Yesu anayamba utumiki wake patatha miyezi isanu ndi umodzi. (Luka 1:24-31) Zimenezi pamodzi ndi umboni wina, zimasonyeza kuti Yesu anayamba utumiki wake kumapeto a chaka cha 29 C.E.c Baibulo limati Yesu anali “monga wa zaka makumi atatu” pamene anayamba utumiki wake. (Luka 3:23) Ngati anali wa zaka 30 kumapeto a chaka cha 29 C.E., ndiyeno ayenera kuti anabadwa cha kumapeto a chaka cha 2 B.C.E. Tsono ngati tiŵerenga mopita m’tsogolo zaka 2000 kuchokera kumapeto a chaka cha 2 B.C.E. (tikumbukire kuti panalibe chaka cha zilo; choncho, kuchokera mu 2 B.C.E. kukafika mu 1 C.E. ndi zaka ziŵiri), tidzaona kuti zaka za chikwi chachiŵiri zinatha ndipo zaka za chikwi chachitatu zinayamba kale cha kumapeto kwa chaka cha 1999!
Kodi zimenezo zili n’kanthu? Mwachitsanzo, kodi chiyambi cha zaka za chikwi chachitatu chikutanthauza kuyambika kwa Ulamuliro wa Yesu Kristu wa Zaka Chikwi, wonenedwa m’buku la Chivumbulutso? Ayi. Baibulo silisonyeza pena paliponse kugwirizana kwa zaka za chikwi chachitatu ndi Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi.
Yesu anachenjeza otsatira ake kuti sayenera kuŵerengera masiku. Anauza ophunzira ake kuti: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa iye yekha.” (Machitidwe 1:7) Poyamba, Yesu ananena kuti ngakhale iyeyo panthaŵi imeneyo sankadziŵa nthaŵi imene Mulungu adzaweruze dongosolo la zinthu loipali, kulambula njira ya Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi. Iye anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.”—Mateyu 24:36.
Kodi n’kwanzeru kuyembekezera kuti Kristu adzabweranso patapita zaka 2,000 zenizeni kuchokera deti limene anabadwa monga munthu? Ayi, si kwanzeru. Yesu ayenera kuti ankadziŵa tsiku limene anabadwa. Ndipo mwachionekere ankadziŵanso kuŵerengera zaka 2,000 kuchokera tsiku limenelo. Koma, sanadziŵe tsiku ndi nthaŵi ya kudza kwake. N’zachionekere, kuti sikungakhale kwapafupi kutchula tsiku la kubweranso kwake! ‘Nthaŵi kapena nyengo’ zili mu ulamuliro wa Atate. Ndandanda ya nthaŵi ya zochita zake akuidziŵa yekha.
Komanso, Yesu sanalamule om’tsatira kuti adzamudikirire pa malo ena ake. Iye sanawauze kuti adzasonkhane ndi kumamudikirira, koma anawauza kuti amwazikane “kufikira kumalekezero ake a dziko” ndi kuphunzitsa anthu a mitundu yonse. Lamulo limenelo sanalichotse.—Machitidwe 1:8; Mateyu 28:19, 20.
Kodi Ziyembekezo Zawo pa Zaka Chikwi Sizidzakwaniritsidwa?
Komabe, anthu ena oumirira miyambo ya chipembedzo akuyembekezera mwa chidwi chaka cha 2000. Amakhulupirira kuti mkati mwa miyezi yoŵerengeka ikubwerayi, zigawo zina za buku la Chivumbulutso zikwaniritsidwa ndendende. Ndithudi, amaona ngati iwowo akutenga nawo mbali m’kukwanitsidwa kumeneko. Mwachitsanzo, amanena za ulosi wolembedwa pa Chivumbulutso 11:3, 7, 8, umene umanena za mboni ziŵiri zomwe zidzalosere ‘m’mudzi waukulu, umene utchedwa, ponena za chizimu, Sodoma ndi Aigupto, pameneponso Ambuye wawo anapachikidwa.’ Pamene amaliza kuchitira umboni, mboni ziŵirizo zikuphedwa ndi chilombo chochititsa mantha chotuluka kuphompho.
Malinga ndi lipoti la mu magazini ina yotchedwa The New York Times ya December 27, 1998, m’tsogoleri wa gulu lina la chipembedzo “anauza otsatira ake kuti iyeyo ndi mmodzi wa mboni ziŵiri zomwe mwa chikonzero cha Mulungu zinaikidwa kuti zilengeze za chiwonongeko cha dziko lapansi ndi kubwera kwa Ambuye, ndipo pambuyo pake zidzaphedwa ndi Satana mu misewu ya ku Yerusalemu.” Akuluakulu a boma la Israyeli ali ndi mantha zedi. Akuopa kuti mwina anthu ena ochita zinthu mopambanitsa angayesere ‘kukwaniritsa’ ulosiwo mwa iwo okha, ngakhale kuti zimenezo zingabutse ziwawa zowomberana! Komabe, Mulungu safuna “thandizo” la munthu kuti chifuno chake chikwaniritsidwe. Maulosi onse a m’Baibulo adzakwaniritsidwa m’nthaŵi yomwe Mulunguyo akuidziŵa yekha, ndipo Mulungu adzakwaniritsa maulosiwo m’njira yakeyake.
Buku la Chivumbulutso linalembedwa ‘m’zizindikiro.’ Malinga ndi Chivumbulutso 1:1, Yesu anafuna kuvumbulira “akapolo ake” (osati dziko lonse) zomwe zikachitika. Kuti amvetse buku la Chivumbulutso, akapolo a Kristu, kapena om’tsatira, amafuna mzimu woyera wa Mulungu, umene Yehova amapereka kwa omwe amam’sangalatsa. Ngati buku la Chivumbulutso likanakhala losavuta kumva, ndiye kuti ngakhale anthu osakhulupirira akanaliŵerenga ndi kulimvetsetsa. Ndiyeno sipakanakhala chifukwa chakuti Akristu azipempherera mzimu woyera kuti uwathandize kumvetsetsa.—Mateyu 13:10-15.
Malinga ndi umboni wa m’Baibulo, taona kuti zaka za chikwi chachitatu, kuchokera pamene Yesu anabadwa, ziyamba kumapeto a chaka cha 1999 ndi kuti kaya deti limenelo, kapena January 1, 2000, ngakhalenso January 1, 2001 si zofunika mwapadera. Koma pali zaka chikwi zomwe zikuchititsa chidwi Akristu ambiri. Ngati si zaka za chikwi chachitatu, tsono ndi ziti? Nkhani yotsiriza m’nkhani zotsatirazi zidzayankha funso limeneli.
[Mawu a M’munsi]
a Onani bokosi patsamba 5 lomwe lili ndi mutu wakuti “2000 Kapena 2001?”.
b Malinga ndi kuŵerengera nthaŵi kwa akatswiri a zamaphunziro ameneŵa, zaka za chikwi chachitatu zikanayamba mu 1995 kapena mu 1996.
c Kuti mumve zochuluka, chonde onani Insight on the Sciptures, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., Voliyumu 1, masamba 1094-5.
[Bokosi patsamba 5]
2000 Kapena 2001?
Kuti timvetse chifukwa chake ena amanena kuti zaka za chikwi chachitatu, kuchokera pamene Yesu anabadwa, zidzayamba pa January 1, 2001, lingalirani fanizo ili. Yerekezani kuti mukuŵerenga buku la masamba 200. Pamene mufika pamwamba pa tsamba 200, ndiye kuti mwamaliza kuŵerenga masamba 199, ndipo kwatsala tsamba limodzi loti muŵerenge. Simunganene kuti mwamaliza kuŵerenga bukulo pokhapokha mutafika kumapeto kwa tsamba 200. Mofananamo, zaka 999 za m’zaka chikwi zamakono zino, monga mmene ambiri amanenera, zikhala zitatha pa December 31, 1999, ndipo kutsala chaka chimodzi kuti zaka chikwi zithe. Malinga n’kaŵerengedwe kameneko, zaka za zana lachitatu, zidzayamba pa January 1, 2001. Komabe, zimenezo sizikutanthauza kuti podzafika tsiku limenelo, ndiye kuti zaka 2,000 ndendende zidzakhala zitatha kuchokera pa tsiku limene Yesu anabadwa, monga mmene nkhani ino yasonyezera.
[Bokosi patsamba 6]
Mmene Kuŵerengera Masiku Pogwiritsa Ntchito B.C.-A.D. Kunayambira
Kumayambiriro kwa zaka za zana lachisanu ndi chimodzi C.E., Papa Yohane woyamba, analamula mmonke wotchedwa Dionysius Exiguus kuti ayambitse njira ya kaŵerengedwe komwe kadzathandize matchalitchi kukhazikitsa tsiku la Isitala.
Dionysius anayamba ntchitoyo. Anaŵerengera masiku mobwerera ku nthaŵi za mmbuyo, kupyola nthaŵi ya imfa ya Yesu, ndi kukafika ku nthaŵi imene iye ankayilingalira kuti ndi imene Yesu anabadwa; ndiyeno anaŵerenga chaka chilichonse mopita m’tsogolo kuchokera pamenepo. Dionysius anatcha nyengo yochokera pa kubadwa kwa Yesu “A.D.” (kuimira Anno Domini—“m’chaka cha Ambuye wathu.”) Pamene anali kukhazikitsa njira yoyenerera yoŵerengera Isitala chaka chilichonse, Dionysius mosadziŵa anayambitsa lingaliro loŵerengera zaka kuyambira nthaŵi ya kubadwa kwa Kristu, kupita m’tsogolo.
Ngakhale kuti akatswiri ambiri amaphunziro avomereza kuti Yesu sanabadwe m’chaka chimene Dionysius anagwiritsa ntchito ngati maziko a kuŵerengetsa kwakeko, njira yake yoŵerengera nthaŵi, imatithandiza kudziŵa zomwe zinachitika kalelo m’kupita kwa nthaŵi ndi kuona mmene zikugwirizanira.