Yehova ndi Mulungu Wokoma Mtima Mwachikondi kwa Ine
YOSIMBIDWA NDI JOHN ANDRONIKOS
Chakacho chinali 1956. Patangopita masiku asanu ndi anayi pambuyo pa ukwati wanga, ndinaima pamaso pa khothi la apilo ku Komotiní, kumpoto kwa Greece. Chiyembekezo changa chinali chakuti chilango cha miyezi 12 chimene ndinapatsidwa chifukwa cha kulalikira za Ufumu wa Mulungu chidzachotsedwapo. Chigamulo cha khothi la apilo miyezi isanu ndi umodzi m’ndende, chinaswa chiyembekezo chimenecho ndipo chinangokhala chiyambi chabe kwa ziyeso zochuluka. Komabe, m’nthaŵi yonseyo, Yehova anasonyeza kukhala Mulungu wokoma mtima mwachikondi kwa ine.
PAMENE ndinabadwa pa October 1, 1931, banja lathu n’kuti likukhala mumzinda wa Kaválla, mzinda wa Neapoli wa ku Macedonia umene mtumwi Paulo anauchezera paulendo wake wachiŵiri waumishonale. Amayi anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova pamene ndinali ndi zaka zisanu zakubadwa, ndipo ngakhale kuti anali osadziŵa kwenikweni kuŵerenga, anayesetsa kukhomereza m’maganizo mwanga kukonda Mulungu ndi kumuopa. Bambo wanga anali munthu wokonda kusunga mwambo kwambiri amene anaumirira kwambiri ku mwambo wa Greek Orthodox. Analibe chidwi ndi choonadi cha Baibulo ndipo ankatsutsa amayi, nthaŵi zambiri kuwachitira nkhanza.
Motero, ndinakulira m’banja logaŵanika, mmene Bambo ankamenya ndi kuzunza Amayi, ndiponso analeka kutisamala. Kuyambira pamene ndinali wamng’ono kwambiri, Amayi amatitenga ine ndi mlongo wanga wamng’ono kupita nafe kumisonkhano yachikristu. Komabe, pamene ndinakwanitsa zaka 15, zilakolako zaunyamata ndi malingaliro a kudziimira pandekha zinanditalikitsa kwambiri ndi Mboni za Yehova. Komabe, amayi wanga wokhulupirikawo anayesetsa, ndipo anali kundililira kwambiri poyesayesa kundithandiza.
Chifukwa cha umphaŵi ndi makhalidwe anga oipa, ndinadwala mwa kayakaya ndipo ndinakhala chogona kwa miyezi yoposa itatu. Inali nthaŵi imeneyo pamene mbale wina wodzichepetsa kwambiri, amene anathandiza amayi wanga kuphunzira choonadi, anazindikira kuti ndimam’kondadi Mulungu. Iye anaona kuti ndingathandizidwe kuchira mwauzimu. Ena amamuuza kuti: “Mukutaya nthaŵi yanu pachabe kuyesa kuthandiza John; amene uja sadzakhalanso ndi chidwi.” Koma kuleza mtima kwa mbale ameneyu ndi kulimbikira kwake kundithandiza kunabala zipatso. Pa August 15, 1952, pausinkhu wazaka 21, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa kubatizidwa m’madzi.
Wongokwatira Kumene ndi Kuikidwa M’ndende
Zaka zitatu pambuyo pake ndinadziŵana ndi Martha, mlongo wamalingaliro auzimu ndi wamakhalidwe abwino kwambiri, ndipo posapita nthaŵi yaitali tinatomerana. Tsiku lina ndinadabwa pamene Martha anandiuza kuti: “Lero ndikuganiza zokalalikira khomo ndi khomo. Kodi ukufuna kutsagana nane?” Kufikira nthaŵi imeneyo ndinali ndisanachitepo mbali imeneyi ya ntchitoyi, poti kaŵirikaŵiri ndimachita ulaliki wamwamwayi. Nthaŵi imeneyo ntchito yolalikira mu Greece inali yoletsedwa, ndipo timayenera kuchita ntchito yathu yolalikira mwam’mtseri. Ambiri anamangidwa, kuzengedwa milandu, ndi zilango zikuluzikulu zokhala m’ndende. Komabe, sindinakane kuperekeza bwenzi langa!
Martha anakhala mkazi wanga mu 1956. Inali nthaŵi imeneyo, masiku asanu ndi anayi pambuyo pa ukwati wathu, pamene ndinalandira chilango cha kukhala m’ndende miyezi isanu ndi umodzi kuchokera ku bwalo la apilo limenelo mu Komotiní. Zimenezi zinandikumbutsa funso limene nthaŵi inayake kumbuyoko ndinafunsa mlongo wina wachikristu, mnzawo wa amayi lakuti: “Kodi ndi motani mmene ndingasonyezere kuti ndine Mboni yoona ya Yehova? Sindinakhalepo ndi mwayi wosonyeza chikhulupiriro changa.” Pamene mlongo ameneyu anabwera kudzandiona kundende, iye anandikumbutsa za funso limenelo n’kunena kuti: “Tsopano ungasonyeze kwa Yehova mmene umam’kondera. Imeneyi ndi ntchito yako.”
Pamene ndinamva kuti loya wanga amafunafuna ndalama zoti andilipilire monga chikole chonditulutsira m’ndendemo, ndinamuuza kuti ndikadakonda kumaliza chilango changacho. Ndinasangalala zedi kuona kuti pomaliza miyezi isanu ndi umodzi yokhala m’ndendeyi aŵiri mwa akaidi anzanga analandira choonadi! M’zaka zotsatira, ndinapezeka m’milandu yambiri kukhothi chifukwa cha uthenga wabwino.
Zosankha Zimene Sitinadandaulepo Nazo
Mu 1959, zaka zingapo pambuyo pa kutulutsidwa m’ndende, ndinali kutumikira monga mtumiki wa mpingo, kapena kuti woyang’anira wotsogoza, ndipo ndinaitanidwa kukachita nawo Sukulu ya Utumiki wa Ufumu maphunziro a akulu a mumpingo. Komabe, nthaŵi yomweyonso ndinapatsidwa ntchito yokhazikika pa chipatala china chaboma, ntchito imene ikanapatsa ine ndi banja langa chuma chokwanira kutithandiza m’moyo. Kodi ndisankhe chiyani? Ndinali nditagwirako kale ntchito pachipatalacho moyembekezera kwa miyezi itatu, ndipo mkulu wa pachipatalapo anali wosangalatsidwa kwambiri ndi magwiridwe anga a ntchito, koma pamene chiitano chopita kusukulu chinafika, sanandilole ngakhale kutenga tchuthi chosalipidwa. Pambuyo posinkhasinkha vutolo mwapemphero, ndinaganiza zoika zinthu za Ufumu pamalo oyamba ndi kukana mwayi wa ntchitowo.—Mateyu 6:33.
Panthaŵi yomweyonso, woyang’anira chigawo ndi woyang’anira dera anabwera kudzatumikira mumpingo wathu. Timayenera kuchita misonkhano yathu mwamtseri m’nyumba zathu chifukwa cha chitsutso chachikulu cha atsogoleri achipembedzo cha Greek Orthodox ndi akuluakulu a boma. Pambuyo pa umodzi wa misonkhanoyo, woyanga’anira chigawo anandifikira ndi kundifunsa ngati ndinaganizapo zochita utumiki wa nthaŵi zonse. Malingaliro ake anandigwira mtima kwambiri chifukwa zimenezi ndi zimene ndinakhala ndikuganiza kuchokera pamene ndinabatizidwa. Ndinayankha kuti: “Ndimafuna kwambirinso.” Komabe, ndinali kale ndi udindo wowonjezereka wa kusamalira mwana wathu wamkazi. Mbaleyo anandiuza kuti: “Khulupirira Yehova, ndipo iye adzakuthandiza kuzindikira zolingalira zako.” Choncho, mosanyalanyaza maudindo athu a m’banja, ine ndi mkazi wanga tinatha kusintha mikhalidwe yathu motero kuti mu December 1960, ndinayamba kutumikira kummaŵa kwa Macedonia monga mpainiya wapadera—mmodzi mwa apainiya apadera asanu okha m’dzikoli.
Nditagwira ntchito monga mpainiya wapadera kwa chaka chimodzi, ofesi yanthambi ku Athens inandiitana kukatumikira monga woyang’anira woyendayenda. Pamene ndinabwerera kumudzi kuchoka ku maphunziro a mwezi umodzi a utumiki umenewu, ndipo ndikufotokozera Martha za zokumana nazo zanga, mkulu wa mgodi wina waukulu wa miyala ya manganese anadzandichezera ndi kundiitana kuti ndikakhale woyang’anira chigawo choyenga miyala, akumandipatsa mwayi wapangano la zaka zisanu, nyumba yabwino, ndi galimoto. Anandipatsa masiku aŵiri kuti ndiyankhe. Kachiŵirinso, mosaopa ngakhale pang’ono, ndinapemphera kwa Yehova kuti: “Ndine pano, munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Mkazi wanga anandivomereza kotheratu. Pokhulupirira Mulungu, tinayamba ntchito yoyendayenda, ndipo Yehova m’kukoma mtima kwake kwachikondi sanatigwiritse fuwa lamoto.
Kutumikira Movutika Kwambiri
Ngakhale kuti panali mavuto a zachuma, tinapitabe patsogolo ndipo Yehova anatipatsa zinthu zofunika. Poyambirira, ndinali kumakachezera mipingo pogwiritsa ntchito njinga yaing’ono yamoto, kuyenda mtunda wokwana makilomita 500. Nthaŵi zambiri ndinali kukumana ndi zopinga, ndiponso panali ngozi zingapo. Pobwerera kuchoka kumpingo winawake m’dzinja linalake, injini ya njinga inazima pamene ndimaoloka kamtsinje kena kodzaza kwambiri, ndipo ndinanyoŵa mpaka m’maondo. Kenako njingayo inaphwa. Wopita ndi njira wina amene anali ndi pompi anandithandiza, potero ndinatha kufika pa mudzi wina wapafupi pamene ndinakonza tayalalo. Ndinafika kumudzi nthaŵi ya fili koloko m’bandakucha, nditazizidwa ndiponso ndili wotopa.
Nthaŵi ina, pamene ndinachoka ku mpingo wina kupita ku mpingo wina, njinga yamoto inatelereka, ndinagwa ndipo inandigwera pabondo. Choncho, buluku langa linang’ambika ndi kupakika magazi. Ndinalibe buluku lina, motero madzulo a tsiku limeneli ndinakamba nkhani nditavala buluku la mbale wina, limene linandikulira kwambiri. Komabe, panalibe chopinga chimene chikanafooketsa chifuno changa cha kutumikira Yehova ndi abale okondedwa.
Pangozi ina, ndinavulala kwambiri, kuthyoka mkono ndi kuguluka mano apamphumi. Inali nthaŵi imeneyi pamene mlongo wanga, amene si Mboni, yemwe amakhala ku United States anadzandichezera. Ndinasangalala kwambiri pamene anandithandiza kugula galimoto! Abale a panthambi ya Athens atamva za ngozi yanga, ananditumizira kalata yolimbikitsa, ndipo mwa zimene analemba m’kalatamo panali mawu opezeka pa Aroma 8:28, pamene ena mwa mawu ake amati: “Amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino.” Nthaŵi ndi nthaŵi, chitsimikizo chimenechi chakhaladi choona m’moyo wanga!
Zodabwitsa Zosangalatsa
Mu 1963, ndinali kugwira ntchito ndi mpainiya wina wapadera m’mudzi wina umene anthu ake anali osalabadira. Tinaganiza zogaŵana, wina kukhala mbali ina ya msewu ndi winanso mbali ina. Panyumba ina, nditangogogoda mayi wina anandikokera m’nyumbamo mwamphamvu ndi kundikhomera. Ndinali wosokonezeka maganizo, kudabwa zimene zinali kuchitika. Nthaŵi yochepa pambuyo pake, mayiyo mofulumira anaitaniranso mpainiya winayo m’nyumbamo. Kenako mkaziyo anatiuza kuti: “Chete! Musagwedezeke ngakhale pang’ono!” Patapita kanthaŵi, tinamva mawu okalipa kunja kwa nyumbayo. Anthu amatifunafuna. Zinthu zitakhala bata, mayiyo anatiuza kuti: “Ndachita izi kuti ndikutetezeni. Ndimakulemekezani chifukwa ndimakhulupirira kuti ndinu Akristu oona.” Tinamuthokoza ndi kunyamuka, titamusiyira mabuku ambiri.
Zaka 14 pambuyo pake, pamene ndinali pamsonkhano wachigawo mu Greece, mayi wina anandifikira n’kunena kuti: “Mbale, mwandikumbukira? Ndine uja amene anakubisani kwa otsutsa pamene munabwera kumudzi wakwathu kudzachita umboni.” Anali atasamukira ku Germany, anaphunzira Baibulo, ndipo anagwirizana ndi anthu a Yehova. Tsopano, banja lake lonse linali m’choonadi.
Inde, pazaka zonsezi, tadalitsidwa ndi ‘makalata a chivomerezo’ ambiri. (2 Akorinto 3:1) Ambiri mwa anthu amene tinali ndi mwayi wowathandiza kupeza choonadi cha Baibulo akutumikira monga akulu, atumiki otumikira, ndi apainiya tsopano. Zimasangalatsa kwambiri kuona ofalitsa ochepa a m’madera amene ndinatumikirako kalero kumayambiriro a 1960 akuwonjezeka kufika pa anthu oposa 10,000 olambira Yehova! Chiyamiko chonse chimapita kwa Mulungu wokoma mtima mwachikondi, amene amatigwiritsira ntchito m’njira yake.
“Pakama Wodwalira”
M’zaka zathu za m’ntchito yoyendayenda, Martha anasonyeza kukhala bwenzi lothandiza ndi labwino, wa mtima wachimwemwe nthaŵi zonse. Komabe, mu October 1976, anadwala mwakayakaya ndipo anamuchita opaleshoni yopweteka kwambiri. Anafa ziŵalo kuchokera m’chuuno mpaka kumiyendo yonse iŵiri nayamba kuyenda panjinga yothandizira kuyenda. Kodi tikanapirira bwanji zimene tinawononga ndiponso kupsinjika maganizo? Pokhulupiriranso mwa Yehova, tinaona chikondi chake ndi kuoloŵa kwa manja ake. Pamene ndinapita kukatumikira ku Macedonia, Martha anakhala panyumba ya mbale wina ku Athens kaamba kakuti azilandira mankhwala kuchipatala. Amandiyankhula pa foni ndi mawu olimbikitsa akuti: “Ine ndilibwino. Pitirizani, ndipo pamene ndidzayambanso kuyenda, ndizidzakuperekezani panjinga yothandizira kuyenda.” Ndipo ndi zimene anachitadi. Abale athu okondedwa a ku Beteli anatitumizira makalata ambiri olimbikitsa. Martha analimbikitsidwa kaŵirikaŵiri ndi mawu a pa Salmo 41:3 amene amati: “Yehova adzam’gwiriziza pakama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake.”
Chifukwa cha mavuto aakulu athanzi ameneŵa, mu 1986 kunalingaliridwa kuti kungandikhalire bwino kukatumikira monga mpainiya wapadera mu Kaválla, kumene ndikukhala pafupi ndi banja la mwana wathu wokondedwa wamkazi. M’March wapitayu mkazi wanga wokondedwa Martha anamwalira, ali wokhulupirika mpaka mapeto. Asanamwalire, pamene abale amam’funsa kuti: “Mulibwanji?” kaŵirikaŵiri ankayankha kuti: “Pokhala woyandikira kwa Yehova, ndili bwino kwambiri!” Pamene timakonzekera misonkhano kapena kulandira mapempho okopa mtima kuti tikatumikire kumadera kumene kuli zotuta zambiri, Martha ankanenabe kuti: “John, tiyeni tikatumikire kumene kusoŵa kuli kwakukulu.” Sanataye mzimu wake wachangu.
Zaka zingapo zapitazo, inenso ndinakumana ndi vuto lalikulu la thanzi. Mu March 1994, ndinapezeka ndi nthenda ya mtima yomwe inaika moyo wanga pangozi, ndipo ndinafunikira opaleshoni. Apanso, ndinamva dzanja la Yehova likundichirikiza m’nthaŵi yovuta imeneyi. Sindidzaiŵala pemphero limene woyang’anira dera anapereka ali pambali pa kama wanga pamene ndinatuluka m’chipinda cha odwala mwakayakaya, komanso phwando la Chikumbutso limene ndinachititsa m’chipinda mwanga kuchipatala komweko pamodzi ndi odwala ena anayi amene amasangalatsidwa ndi choonadi.
Yehova Wakhala Mthandizi Wathu
Nthaŵi ikuthamanga, ndipo matupi athu akufooka, koma mzimu wathu umapangidwanso kukhala watsopano kudzera m’phunziro ndi utumiki. (2 Akorinto 4:16) Papita zaka 37 tsopano kuchokera pamene ndinanena kuti, “Ndine pano; munditumize ine.” Moyo wanga wakhala weniweni, wosangalatsa, ndi wofupa. Inde, nthaŵi zina ndimadzimva kuti “ndine wozunzika ndi waumphaŵi,” komabe ndi chidaliro ndinganene kwa Yehova kuti: “Inu ndinu mthandizi wanga, ndi mpulumutsi wanga.” (Salmo 40:17) Iye wakhaladi Mulungu wokoma mtima mwachikondi kwa ine.
[Chithunzi patsamba 25]
Ndi Martha mu 1956
[Chithunzi patsamba 26]
Doko la ku Kaválla
[Chithunzi patsamba 26]
Ndi Martha mu 1997