Gileadi Itumiza Amishonale “Kufikira Malekezero Ake a Dziko”
KWA zaka zoposa theka la zana tsopano, Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower yakhala ikutumiza amishonale. Pa September 11, 1999, ophunzira m’kalasi la 107 la Gileadi anamaliza maphunziro awo. Linali ndi ophunzira 48 ochokera m’mayiko 11, ndipo anthu ameneŵa anatumizidwa kukatumikira m’mayiko 24. Iwoŵa akagwirizana ndi amishonale enanso, omwe achita mbali yofunika kwambiri pokwaniritsa mawu omaliza a Yesu amene anawanena asanakwere kumwamba. Ananeneratu kuti ophunzira ake adzakhala “Mboni [zake] . . . kufikira malekezero ake a dziko.”—Machitidwe 1:8.
Pologalamu yokondwerera kumaliza maphunziroyo, yomwe inachitikira ku Likulu la Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York, inalidi chochitika chachikulu pamalo okongola ameneŵa. Ophunzira omwe anamaliza maphunzirowo anali osangalala kwambiri kuona achibale, mabwenzi, ndi alendo omwe anadza kudzapenyerera chochitika chimenechi. Kuphatikiza onse amene anamvera pologalamuyi pawailesi ndi kuionera pavidiyo ku Brooklyn ndi ku Wallkill, anali okwanira 4,992.
Tumikirani Yehova ndi Mnansi Mokhulupirika
“Ndani ali Kumbali ya Yehova?” Umenewo unali mutu wa nkhani ya malonje ya Carey Barber, wa m’Bungwe Lolamulira yemwenso anali tcheyamani wa pologalamu yokondwerera kumaliza maphunziroyo. Anafotokoza kuti imeneyi inalinso nkhani yomwe Aisrayeli a m’tsiku la Mose anayang’anizana nayo. Ophunzira amene anamaliza maphunzirowo ndi awo amene anadza kudzapenyerera mwambowo anakumbutsidwa kuti Aisrayeli ena ambiri anafera m’chipululu chifukwa chakuti sanathe kukhalabe ku mbali ya Yehova mokhulupirika. Atatha kupembedza mafano, iwo “anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kuseŵera.” (Eksodo 32:1-29) Yesu anachenjeza Akristu za ngozi yofananayo kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.”—Luka 21:34-36.
Wokamba nkhani wachiŵiri, Gene Smalley, wa m’Dipartmenti Yolemba, anafunsa ophunzira amene anamaliza maphunzirowo kuti: “Kodi Mudzakhala Ochepetsa Ululu?” Anafotokoza kuti liwu la Chigiriki lakuti pa·re·go·riʹa (kuchepetsa ululu) linayamba kugwiritsidwa ntchito m’Chingelezi monga dzina la mankhwala amene amachepetsa ululu. Komabe, mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito liwu lachigiriki limeneli lokhala ndi tanthauzo pa Akolose 4:11 pofotokoza antchito anzake. Mu New world Translation, liwu limeneli latembenuzidwa kuti “chotonthoza.”
Mu utumiki wawo wa umishonale omaliza maphunziroŵa angakhale ochepetsa ululu a masiku ano m’njira yeniyeni mwakukhala otonthoza odzichepetsa kwa abale ndi alongo ndiponso mwakusonyeza mzimu wogwirizana ndi wachikondi kwa amishonale anzawo.
Kenako, Daniel Sydlik wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yamutu wakuti “Mfundo ya Chikhalidwe (Pulinsipulo) Yofunika Kuitsatira.” Anafotokoza kuti mfundo yapamwamba yachikhalidwe yomwe Yesu ananena pa Mateyu 7:12 yakuti, “zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero,” imaphatikizapo kuchitira ena zabwino, osati kupeŵa kuchita zoipa kokha.
Kuti tichite zimenezi bwino lomwe, pamafunika zinthu zitatu: diso lopenya bwino, mtima wachifundo, ndi kupereka chithandizo. Pofotokoza mwachidule iye anati: “Ngati tikufunitsitsadi kuthandiza, tiyenera kutero mofulumira. Tiyenera kuyesetsa kuchitira ena zinthu zimene tikufuna kuti iwo atichitire.” Zimenezi ziyenera kukhaladi choncho makamaka kwa amishonale opita m’mayiko ena kukathandiza anthu kutsata Chikristu choona.
Alangizi Apereka Zikumbutso Zogwira Mtima
Karl Adams, mlangizi wa Gileadi analimbikitsa amishonale omaliza maphunzirowo “Kupitirizabe Kukula.” M’mbali ziti? Yoyamba, m’chidziŵitso ndi m’nzeru yochigwiritsa ntchito moyenera. Ku Gileadi, ophunzirawo anaphunzira mmene angafufuzire kuti apeze chiyambi cha nkhani za m’Baibulo ndi mmene zinachitikira. Analimbikitsidwa kulingalira mmene nkhani iliyonse iyenera kukhudzira miyoyo yawo. Anapemphedwa kupitirizabe kuchita zimenezi.
“Yachiŵiri, kupitirizabe kukula m’chikondi. Chikondi ndi chinthu chinachake chomwe chimakula ngati chisamalidwa. Koma ngati chinyalanyazidwa, chingafe,” anatero Mbale Adams. (Afilipi 1:9) Tsono monga amishonale, adzafunikira kukula m’chikondi m’mikhalidwe yosiyanasiyana. Ndipo yachitatu: “Kulani m’chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu.” (2 Petro 3:18) Wokamba nkhaniyo anati “Ichi ndi chisomo chapadera chimene Yehova wasonyeza kupyolera mwa Mwana wake. Pamene tikulitsa kuyamikira chisomo chapadera chimenecho, chisangalalo chathu chimakula pochita chifuno cha Mulungu ndi zomwe watiuza kuchita.”
Mlangizi wina wa Gileadi, Mark Noumair, anakamba nkhani yakuti “Lolerani Mikhalidwe Yovutayo mwa Chikondi, Ndipo Mudzapirira.” Analimbikitsa kuti: “Phunzirani kulolera mikhalidwe yovuta pamoyo wa umishonale mwa chikondi, ndipo mudzapirira. Yehova amalanga okhawo amene amawakonda. Ngakhale mutaona kuti uphungu wina uli wosayenerera, wokondera, kapena wachinyengo, kukonda kwanu Yehova komanso unansi wanu ndi iye zidzakuthandizani kupirira.”
Mbale Noumair ananena kuti utumiki wa umishonale umaphatikizapo ntchito zinanso zambiri. “Koma ntchito yopanda nayo chikondi idzakupangitsani kukhala osasangalala. Popanda chikondi, ntchito zanu za panyumba monga kuphika, kugula zinthu, kutsuka zipatso, kuŵiritsa madzi, zingangokupangitsani kukhala wonyong’onyeka zedi. Muyenera kulingalira kaye ndi kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani ndikugwira ntchito zimenezi?’ Eya, mukayankha kuti, ‘Ntchito zangazi zikuchirikiza nawo thanzi ndi chimwemwe cha amishonale anzanga,’ ndiye kuti sikudzakhala kovuta kupirira.” Mwachidule, iye analimbikitsa ndi mawu akuti: “Kaya kukhale kulandira uphungu, kukwaniritsa maudindo anu aumishonale, kapena kusamalira mikangano, kuchita zimenezi mwa chikondi kudzakuthandizani kupirira m’ntchito yanu. ‘Chikondi sichitha nthaŵi zonse.’”—1 Akorinto 13:8.
Kenako mlangizi wa Gileadi Wallace Liverance, anatsogolera zitsanzo zabwino zingapo za zokumana nazo zosangalatsa zomwe zinakondweretsa ophunzirawo pamene anali kugwira ntchito limodzi ndi mipingo yakumeneko. Kuphatikiza pa kupita kunyumba ndi nyumba, anagwiritsa ntchito maphunziro awo aumishonalewo kufufuza anthu pamalo oimika galimoto zikuluzikulu, kumalo ochapira a anthu osiyanasiyana, poima sitima, ndi m’malo enanso.
Amishonale Ozoloŵera Ntchito Yawo Anapereka Chilimbikitso
Pamene amishonale atsopano apita kudziko lachilendo, kodi palinso chifukwa choti azidera nkhaŵa? Kodi angakumane ndi mavuto a kutumikira m’dziko lachilendo? Kodi maofesi anthambi amachitanji kuti athandize anthu achatsopano ameneŵa kukwaniritsa ntchito yawo? Poyankha mafunso ameneŵa ndi enanso, Steven Lett, wa m’Dipatimenti Yoyang’anira Utumiki, ndi David Splane, wa m’Dipatimenti Yolemba, anafunsa abale amene panthaŵiyo anali akuphunzira sukulu ya nthambi ku Likulu la Maphunziro a Watchtower. Abale amene anafunsidwa akutumikira m’makomiti anthambi ku Spain, Hong Kong, Liberia, Benin, Madagascar, Brazil, ndi Japan.
Atumiki a Yehova oidziŵa bwino ntchito ameneŵa, omwenso ambiri a iwo akhala akutumikira monga amishonale kwa zaka zambiri, anatsimikizira ophunzira omaliza maphunziroŵa komanso makolo ndi achibale awo omwe anadza kudzaonerera nawo mwambowu. Kuchokera pa zomwe iwo eniwo aziona komanso pa zomwe amishonale anzawo akumana nazo, anasonyeza kuti mavuto ndi nkhaŵa zitha kugonjetsedwa bwinobwino. Mwina vuto lomwe angakumane nalo lingakhale lalikulu, “koma lingathetsedwe, ndipo Sosaite imatithandiza,” anatero Raimo Kuokkanen, yemwe akuchita umishonale ku Madagascar. “Sitinasankhe ntchito imeneyi, tinachita kupatsidwa,” anatero Östen Gustavsson, yemwe tsopano akutumikira ku Brazil. “Choncho tinatsimikiza mtima kuchita zonse zimene tikanatha kuti tikhalebe muutumiki wathuwu.” James Linton, amene amatumikira ku Japan, ananena kuti chomwe chinam’thandiza chinali “kukhalapo kwa abale omwe anali atayamba kale utumiki wa umishonale.” Utumiki waumishonale ndi njira yosangalatsa ndi yokhutiritsa yotumikirira Yehova ndi kusamalira nkhosa zake.
Kupewa Mliri Womwe Umapha Mkhalidwe Wauzimu
Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira, amenenso anamaliza maphunziro a Gileadi m’kalasi lachisanu ndi chiŵiri m’chaka cha 1946, anapereka nkhani yomaliza, yamutu wakuti “Vuto la Kukhalabe Wamoyo Mwauzimu.” Atavomereza nkhanza zosaneneka zomwe zikuchitika m’mbali zosiyanasiyana padziko lapansi, iye ananena kuti masoka oopsa, kwenikweni akuchitikira mtundu wa anthu.
Ponena za Salmo 91, Mbale Jaracz anatchula “mlili” ndi “chiwonongeko” zimene zadwalitsa ndi kupha mwauzimu anthu miyandamiyanda kulikonse. Mdyerekezi ndi dongosolo lake loipali agwiritsa ntchito mabodza onga mliliwo, ozikidwa pa nzeru zadziko ndi kukonda chuma, pofuna kufoola ndi kupha mikhalidwe ya uzimu, koma Yehova akutitsimikizira kuti mlili umenewu sudzayandikira “Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba.”—Salmo 91:1-7.
“Vuto,” Mbale Jaracz anati “ndilo kukhala wathanzi m’chikhulupiriro, kukhalabe pamalo osungika. Sitingakhale ngati onyoza ‘osakhala naye mzimu.’ Lerolino limeneli n’lomwe lili vuto. N’lomwenso tonsefe m’gululi tayang’anizana nalo. Lingagwere inunso mu ntchito yanu ya umishonaleyo.” (Yuda 18, 19) Koma amishonale omaliza maphunzirowo anauzidwa kuti angakhoze bwino lomwe kukhalabe auzimu mu utumiki wawo. Mwachitsanzo, analimbikitsidwa kulingalira, momwe abale athu akupiririra ku Russia, Asia, ndi m’mayiko ena a mu Africa, mosasamala kanthu za ziletso, chitsutso champhamvu, chitonzo, mabodza osonyeza kusakhulupirira Mulungu, ndi milandu yopeka. Ndipo, nthaŵi zambiri, pamakhalanso mavuto akuthupi, obwera chifukwa cha nkhondo za mafuko ndi kuperewera kwa zinthu zofunika.
Pamene pali kufooka mwauzimu, “n’kofunika kuona kaye chomwe chayambitsa vutolo ndiyeno n’kugwirirapo ntchito, pogwiritsa ntchito uphungu wa m’Mawu a Mulungu.” Anapereka zitsanzo za m’Baibulo. Yoswa analimbikitsidwa kuŵerenga buku lake la Chilamulo ndi kulingaliramo tsiku ndi tsiku. (Yoswa 1:8) Buku la Chilamulo litapezeka m’tsiku la Yosiya, Yehova anadalitsa kugwira ntchito mokhulupirika kwa malangizo ake. (2 Mafumu 23:2, 3) Timoteo anadziŵa malembo oyera kuyambira ubwana wake. (2 Timoteo 3:14, 15) Abereya sanali kokha omvetsera mwatcheru; anaonedwanso kukhala “mfulu” chifukwa anasanthula Malemba tsiku ndi tsiku. (Machitidwe 17:10, 11) Ndipo Yesu Kristu ndi chitsanzo chapadera koposa cha munthu amene anadziŵa ndi kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu.—Mateyu 4:1-11.
Pomaliza, Mbale Jaracz mwachikondi anauza amishonale atsopanowo kuti: “Tsopano ndinu wokonzeka kuyamba utumiki wanu wa umishonale. Ndipo mupita m’mayiko ena, m’lingaliro lenileni, kumbali zosiyanasiyana za dziko lapansi. Ngati tipirira pa kukhalabe wamoyo mwauzimu, ndiye kuti sitidzalolanso china chilichonse kutidodometsa kuchita zimene tasankha kuzichita. Mudzalalikira mwachangu, kulimbikitsa ena kutsanzira chikhulupiriro chanu, ndipo ife tidzapemphera nanu limodzi kuti amene mukaphunzitsa, Yehova awapange kukhala amoyo monga mmene watipangira ifeyo. Ndipo potero ambiri adzapewa tsoka lauzimu limene tsopano likukula padziko lonse. Ambiri adzatsagana nafe limodzi m’kuchita chifuniro cha Yehova. Ndipotu pachifukwa chimenechi tikupempha Yehova kuti akudalitseni.”
Tcheyamani atatsiriza kuŵerenga moni wochokera m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse lapansi, inafika nthaŵi yoti apereke madipuloma kwa ophunzira omaliza maphunzirowo. Kenako anaŵerenga kalata yothokoza imene ophunzirawo analemba. Si mmenetu anathokozera Yehova ndi gulu lake chifukwa cha maphunziro apadera amene analandirawo ndi mautumiki awo osiyanasiyana monga amishonale kupita ku “malekezero ake a dziko”!—Machitidwe 1:8.
[Bokosi patsamba 29]
Ziŵerengero za kalasi
Chiŵerengero cha mayiko amene anachokera: 11
Chiŵerengero cha mayiko kumene anatumizidwa: 24
Chiŵerengero cha ophunzira: 48
Chiŵerengero cha mabanja: 24
Avareji ya zaka zakubadwa: 34
Avareji ya zaka m’choonadi: 17
Avareji ya zaka mu utumiki wanthaŵi zonse: 12
[Chithunzi patsamba 26]
Kalasi la 107 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo mayina andandalikidwa kuyambira kumanzere kumka kumanja mumzera uliwonse.
1. Peralta, C.; Hollenbeck, B.; Shaw, R.; Hassan, N.; Martin, D.; Hutchinson, A. 2. Edwards, L.; Vezer, T.; Ceruti, Q.; Entzminger, G.; D’Aloise, L.; Baglieri, L. 3. Knight, P.; Krause, A.; Kasuske, D.; Rose, M.; Friedl, K.; Nieto, R. 4. Rose, E.; Backus, T.; Talley, S.; Humbert, D.; Bernhardt, A.; Peralta, M. 5. D’Aloise, A.; Humbert, D.; Dunn, H.; Gatling, G.; Shaw, J.; Ceruti, M. 6. Baglieri, S.; Krause, J.; Hollenbeck, T.; Martin, M.; Bernhardt, J.; Hutchinson, M. 7. Backus, A.; Dunn, O.; Gatling, T.; Vezer, R.; Knight, P.; Hassan, O. 8. Nieto, C.; Talley, M.; Friedl, D.; Kasuske, A.; Edwards, J.; Entzminger, M.