Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w02 12/15 tsamba 8-14
  • “Yandikirani kwa Mulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Yandikirani kwa Mulungu”
  • Nsanja ya Olonda—2002
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pitirizani ‘Kum’dziŵa’ Mulungu
  • Sonyezani Kukonda Kwanu Yehova
  • Khala Nayeni pa Ubwenzi wa Pamtima Kudzera M’pemphero
  • “Adzayandikira kwa Inu”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Yandikirani Mulungu Ndipo Iyenso Adzakuyandikirani”
    Yandikirani Yehova
  • Kodi Yehova Ndi Mnzanu Weniweni?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi N’zothekadi ‘Kuyandikira Mulungu’?
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2002
w02 12/15 tsamba 8-14

“Yandikirani kwa Mulungu”

“Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”​—YAKOBO 4:8.

1, 2. (a) Kodi nthaŵi zambiri anthu amati chiyani? (b) Kodi Yakobo anapereka langizo lotani, ndipo n’chifukwa chiyani linali lofunika?

“MULUNGU ali nafe.” Mawu ameneŵa akometsera mbendera za dziko ndiponso ngakhale mayunifolomu a asilikali. Mawu akuti, “Timakhulupirira Mulungu,” awalemba pa ndalama zambiri za koini ndiponso za pepala za masiku ano. Sizachilendo anthu kunena kuti ali paubwenzi wapamtima ndi Mulungu. Koma kodi simungavomereze kuti kukhaladi pa ubwenzi umenewo kumafuna zambiri kuposa kungonena pakamwa kapena kulemba penapake kuti ena aone?

2 Baibulo limasonyeza kuti n’zotheka kukhala paubwenzi ndi Mulungu. Komabe pamafunika khama. Ngakhalenso Akristu ena odzozedwa a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino anafunika kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova Mulungu. Yakobo, woyang’anira wachikristu, anawachenjeza ena pankhani ya zizoloŵezi zawo zathupi ndi kusakhala kwawo oyera mwauzimu. M’malangizo amene anawapatsawo anaphatikizamonso langizo lamphamvu lakuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:1-12) Kodi Yakobo anatanthauza chiyani ponena kuti, “yandikirani”?

3, 4. (a) Kodi ena mwa anthu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, amene anaŵerenga kalata ya Yakobo, ayenera kuti anakumbukira chiyani atamva mawu akuti “yandikirani kwa Mulungu”? (b) N’chifukwa chiyani tingatsimikize kuti n’zotheka kuyandikira kwa Mulungu?

3 Yakobo anagwiritsira ntchito mawu amene ambiri mwa anthu omwe anaŵerenga kalata yake ayenera kuti anali kuwadziŵa bwino. Chilamulo cha Mose chinapatsa ansembe malangizo osapita m’mbali ofotokoza mmene iwo, m’malo mwa anthu ake, angatsenderere kapena ‘kuyandikira’ kwa Yehova. (Eksodo 19:22) Motero, amene anaŵerenga kalata ya Yakobo ayenera kuti anawakumbutsa kuti kuyandikira kwa Yehova sayenera kukuona ngati nkhani yamaseŵera. Yehova ndiye wolemekezeka kwambiri m’chilengedwe chonse.

4 Komabe, monga mmene katswiri wina wa maphunziro a Baibulo ananenera, “langizo limeneli [la pa Yakobo 4:8] likusonyeza kuti n’kothekadi” kuyandikira kwa Mulungu. Yakobo anadziŵa kuti Yehova nthaŵi zonse wakhala akupempha mwachikondi anthu opanda ungwiro kuti ayandikire kwa Iye. (2 Mbiri 15:2) Nsembe ya Yesu inatsegula njira yom’fikira Yehova kotheratu. (Aefeso 3:11, 12) Masiku ano, njira yom’fikira Mulungu yatseguka kwa anthu miyandamiyanda. Koma kodi tingatani kuti tigwiritsire ntchito mwayi wamtengo wapatali umenewu? Tikambirana mwachidule njira zitatu zimene tingayandikirire kwa Yehova Mulungu.

Pitirizani ‘Kum’dziŵa’ Mulungu

5, 6. Kodi chitsanzo cha Samueli ali mwana chikusonyeza bwanji zimene zimafunika pa ‘kum’dziŵa’ Mulungu?

5 Malinga ndi Yohane 17:3, Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” Kodi Yesu anatanthauza chiyani pamene ananena za ‘kum’dziŵa’ Mulungu? Akatswiri angapo amati ganizo la liwu limene analigwiritsira ntchito poyambirira m’Chigiriki limasonyeza kuti kudziŵako kuyenera kupitiriza, zimene zingachititse munthu kum’dziŵa bwino kwambiri mnzake.

6 Kum’dziŵa bwino kwambiri Mulungu sinali mfundo yatsopano m’nthaŵi ya Yesu. Mwachitsanzo, m’Malemba Achihebri, timaŵerenga kuti pamene Samueli anali mwana, “sanadziŵe Yehova.” (1 Samueli 3:7) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Samueli ankadziŵa zochepa chabe zokhudza Mulungu wake? Ayi. Makolo ake ndi ansembe ayenera kuti anamuphunzitsa kwambiri. Koma malinga ndi mmene ananenera katswiri wina, liwu la Chihebri limene analigwiritsira ntchito m’vesi limeneli, “lingagwiritsidwe ntchito pofotokoza za ubwenzi wapamtima zedi.” Samueli anali asanamudziŵe bwino kwambiri Yehova, monga mmene anali kudzam’dziŵira pambuyo pake pamene anali kutumikira ngati wom’lankhulira Wake. Pamene Samueli anali kukula, anam’dziŵadi Yehova, kukhala naye paubwenzi wapamtima.​—1 Samueli 3:19, 20.

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchita mantha ndi ziphunzitso zakuya za m’Baibulo? (b) Kodi choonadi china chakuya cha m’Mawu a Mulungu chimene tiyenera kuphunzira n’chiti?

7 Kodi mukuphunzira za Yehova n’cholinga choti mum’dziŵe bwino kwambiri? Kuti muchite zimenezo, mufunika “kulakalaka” chakudya chauzimu chimene Mulungu amapereka. (1 Petro 2:2, NW) Musakhutire ndi ziphunzitso zazikulu zokha zoyambirira za m’Baibulo. Yesetsani kuphunzira ziphunzitso zina zakuya za m’Baibulo. (Ahebri 5:12-14) Kodi mumachita mantha ndi ziphunzitso zimenezo, kuganiza kuti n’zovuta kwambiri? Ngati ndi choncho, kumbukirani kuti Yehova ndiye “Mlangizi Wamkulu.” (Yesaya 30:20, NW) Iye amadziŵa mmene angaperekere choonadi chakuya kwa anthu opanda ungwiro. Ndipo angadalitse khama lanu lochokera pansi pamtima lofuna kumvetsa zimene akukuphunzitsani.​—Salmo 25:4.

8 Bwanji osadzipenda nokha pankhani ya zina mwa “zakuya za Mulungu”? (1 Akorinto 2:10) Zimenezi si nkhani zopanda pake monga zimene akatswiri a maphunziro azaumulungu ndi atsogoleri a zipembedzo amakanganapo. Izo ndi ziphunzitso zofunika kwambiri zimene zimatithandiza kudziŵa zinthu zosangalatsa zokhuza maganizo ndi mtima wa Atate wathu wachikondi. Mwachitsanzo, pali nkhani za dipo, “chinsinsi,” ndi mapangano osiyanasiyana amene Yehova wagwiritsira ntchito pofuna kupindulitsa anthu ake ndi kukwaniritsa zolinga zake. Nkhani zimenezi pamodzinso ndi nkhani zina zangati zimenezi, ndi mfundo zosangalatsa ndiponso zopindulitsa zimene munthu angafufuze ndi kuziphunzira.​—1 Akorinto 2:7.

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani kudzikuza n’koipa, ndipo n’chiyani chingatithandize kuti tikupeŵe? (b) Pankhani ya kudziŵa Yehova, n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa?

9 Pamene mukudziŵa zambiri za choonadi chakuya chauzimu, peŵani kudzikuza, vuto limene lingakhalepo chifukwa chodziŵa zambiri. (1 Akorinto 8:1) Kudzikuza n’koipa chifukwa kumapatutsa anthu kwa Mulungu. (Miyambo 16:5; Yakobo 4:6) Kumbukirani kuti palibe munthu amene ali ndi zifukwa zodzikuzira pa zimene akudziŵa. Mwachitsanzo, taonani mawu oyamba awa a buku limene limafotokoza zimene anthu atulukira posachedwapa pankhani za sayansi. Ilo limati: “Pamene tikupitiriza kudziŵa zambiri, m’pamenenso tikuzindikira kuti zimene tikudziŵa n’zochepa chabe. . . . Zonse zimene taphunzira n’zochepa kwambiri poyerekeza ndi zimene tifunikabe kuziphunzira.” Kudzichepetsa ngati kumeneku n’kosoŵa. Tsopano pankhani ya chidziŵitso chonse chofunika kwambiri cha Yehova Mulungu, tili ndi zifukwa zambiri zokhalira odzichepetsa nthaŵi zonse. Chifukwa chiyani?

10 Taonani mawu ena a m’Baibulo onena za Yehova. “Zolingalira zanu n’zozama ndithu.” (Salmo 92:5) “Nzeru yake [Yehova] njosatha.” (Salmo 147:5) “Nzeru zake [Yehova] sizisanthulika.” (Yesaya 40:28) “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu!” (Aroma 11:33) Inde, sitidzadziŵa zonse zofunika kuzidziŵa zokhudza Yehova. (Mlaliki 3:11) Iye watiphunzitsa zinthu zabwino zambiri, koma nthaŵi zonse tidzakhalabe ndi zinthu zambiri zoti tiphunzire. Kodi zimenezi sizikutisangalatsa ndiponso kutipangitsa kudzichepetsa? Ndiyetu pamene tikuphunzira, tiyeni nthaŵi zonse tigwiritsire ntchito zimene tadziŵazo kuyandikira kwa Yehova ndiponso kuthandiza nazo ena kuti nawonso achite chimodzimodzi, osati kudzikuza nazo pamaso pa ena.​—Mateyu 23:12; Luka 9:48.

Sonyezani Kukonda Kwanu Yehova

11, 12. (a) Kodi zimene timadziŵa za Yehova ziyenera kutikhudza bwanji? (b) N’chiyani chimatsimikizira ngati munthu amakondadi Mulungu?

11 Mtumwi Paulo moyenerera anagwirizanitsa chidziŵitso ndi chikondi. Analemba kuti: “Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezere, m’chidziŵitso, ndi kuzindikira konse.” (Afilipi 1:9) Choonadi cha mtengo wapatali chilichonse chimene timaphunzira chokhudza Yehova ndi zolinga zake chiyenera kuwonjezera kukonda kwathu Atate wathu wakumwamba osati kutichititsa kudzitukumula.

12 N’zoona kuti ambiri amene amati amakonda Mulungu samukonda. Angamve kuti amamukonda ndipo angasonyeze mmene amamvera. Zimenezo n’zabwino, ndipo n’zoyamikirika zikakhala kuti zikugwirizana ndi kudziŵa zolondola. Koma zimenezi pazokha sizitanthauza kuti munthuyo akukondadi Mulungu. Chifukwa chiyani tikutero? Taonani mmene Mawu a Mulungu amafotokozera kukondadi Mulungu. Amati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Motero, kukonda kwathu Yehova kungakhale kwenikweni ngati tisonyeza zimenezo mwa zochita zathu zoonetsa kuti timamumvera.

13. Kodi kuopa Yehova kudzatithandiza bwanji kusonyeza kum’konda kwathu?

13 Kuopa Yehova kudzatithandiza kumumvera. Mantha otereŵa pamodzi ndi kulemekeza kwambiri Yehova zimayambira pa kudziŵa za iye, kuphunzira za chiyero, ulemerero, mphamvu, chilungamo, nzeru, ndi chikondi chake chosatha. Mantha oterowo ndi ofunika kwambiri poyandikira kwa iye. Ndipotu, onani zimene Salmo 25:14 (NW) limanena. Limati: “Ubwenzi ndi Yehova ngwa iwo akuopa iye.” Motero, ngati timaopa kusasangalatsa Atate wathu wokondedwa wakumwamba, tingayandikire kwa iye. Kuopa Mulungu kudzatithandiza kumvera malangizo anzeru amene ali pa Miyambo 3:6 omwe amati: “Um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

14, 15. (a) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene timafunika kusankha tsiku ndi tsiku? (b) Kodi tingasankhe bwanji zochita m’njira yomwe ingasonyeze kuti timaopa Mulungu?

14 Mumafunika kusankha zochita tsiku lililonse, kaya ndi zochita zazikulu kapena zazing’ono. Mwachitsanzo, kodi mudzakambirana nkhani zotani ndi amene mukugwira nawo ntchito limodzi, amene mukuphunzira nawo kusukulu, ndi anthu amene mwayandikana nawo? (Luka 6:45) Kodi mudzagwira mwakhama ntchito imene mwapatsidwa, kapena mudzachita ukamberembere mwa kungogwira ntchitoyo patalipatali? (Akolose 3:23) Kodi mudzagwirizana kwambiri ndi anthu amene amakonda pang’ono kapena sakonda n’komwe Yehova, kapena mudzalimbitsa ubwenzi wanu ndi anthu okonda zauzimu? (Miyambo 13:20) Kodi mudzachita chiyani kuti mupititse patsogolo zinthu za Ufumu wa Mulungu ngakhale m’njira zochepa chabe? (Mateyu 6:33) Ngati mfundo za m’Malemba monga zimene tazifotokoza pano zingakutsogolereni posankha zochita zanu za tsiku ndi tsiku, ndiye kuti mukum’lemekezadi Yehova ‘m’njira zanu zonse.’

15 Kwenikweni, chilichonse chimene tingasankhe kuchita, tiyenera kusankha motsogoleredwa ndi mfundo yakuti: ‘Kodi Yehova angafune kuti ndichite chiyani pankhani imeneyi? Kodi ndi njira iti imene ingamusangalatse kwambiri?’ (Miyambo 27:11) Kusonyeza kuopa Mulungu mwa kuchita zimenezi ndiyo njira yabwino kwambiri yosonyezera kukonda Yehova. Kuopa Mulungu kudzatichititsanso kukhala oyera pa moyo wathu wauzimu, makhalidwe, ndiponso kukhala aukhondo. Kumbukirani kuti m’vesi limene Yakobo analimbikitsa Akristu kuti ‘ayandikire kwa Mulungu,’ analangizanso m’vesi lomwelo kuti: “Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iŵiri inu.”​—Yakobo 4:8.

16. Pamene tipereka kwa Yehova, kodi sitingakwaniritse chiyani, komabe kodi nthaŵi zonse tingathe kuchita chiyani?

16 Komabe, kusonyeza kukonda kwathu Yehova kumafuna zambiri osati kungopeŵa chabe zoipa. Chikondi chimatilimbikitsanso kuchita zabwino. Mwachitsanzo, kodi timachitapo chiyani pa kuoloŵa manja kosaneneka kwa Yehova? Yakobo analemba kuti: “Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko.” (Yakobo 1:17) Kunena zoona, tikamam’patsa chuma chathu Yehova, sitimamulemeretsa. Zinthu zonse n’zake kale. (Salmo 50:12) Ndipo tikamapereka nthaŵi ndi mphamvu zathu kwa Yehova, sikuti timakwaniritsa chinthu chimene iye sakanatha kuchikwaniritsa pakadapanda ife. Titati takana kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, iye akhoza kuchititsa miyala kufuula. Nangano n’chifukwa chiyani tifunika kupereka chuma chathu, nthaŵi yathu, ndi mphamvu zathu kwa Yehova? Chifukwa chachikulu n’chakuti mwa kuchita zimenezo timasonyeza kuti timamukonda ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, nzeru zathu zonse, ndi mphamvu zathu zonse.​—Marko 12:29, 30.

17. Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kupereka kwa Yehova mokondwera?

17 Tikamapereka kwa Yehova, tiyenera kuchita zimenezo mokondwera, “pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Mfundo imene ili pa Deuteronomo 16:17 ingatithandize kupereka mokondwera. Iyo imati: “Apereke yense monga mwa mphatso ya m’dzanja lake, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani.” Tikamaganizira mmene Yehova watipatsira zinthu mooloŵa dzanja, timafunitsitsa kum’patsa mokondwera. Kupatsa kumeneko kumasangalatsa mtima wake, monga mmene mphatso yaing’ono imene mwana wokondedwa wapereka kwa kholo lake imasangalatsira khololo. Kusonyeza chikondi chathu m’njira imeneyi kudzatithandiza kuyandikira kwa Yehova.

Khala Nayeni pa Ubwenzi wa Pamtima Kudzera M’pemphero

18. N’chifukwa chiyani n’kopindulitsa kuona mmene tingawongolere mapemphero athu?

18 Nthaŵi imene timapemphera patokha timakhala ndi mwayi waukulu wolankhula zakukhosi kwa Atate wathu wakumwamba. (Afilipi 4:6) Popeza pemphero ndi njira yofunika kwambiri yoyandikirira kwa Mulungu, n’kopindulitsa kuima kaye n’kuona kuti kodi mapemphero athu ndi otani. Sikuti afunika kukhala ambambande, osanjidwa mwa mtundu winawake ayi, koma zimene tikunenazo ziyenera kuchokera mumtima. Kodi tingawongolere bwanji mapemphero athu?

19, 20. N’chifukwa chiyani tifunika kusinkhasinkha tisanapemphere, ndipo ndi nkhani zina ziti zoyenerera zimene tingasinkhesinkhe?

19 Tingasinkhesinkhe tisanapemphere. Ngati tisinkhasinkha pasadakhale, tingachititse mapemphero athu kukhala olunjika ndiponso atanthauzo, motero tingapeŵe chizoloŵezi chongobwerezabwereza mawu ofanana amene savuta kuwakumbukira. (Miyambo 15:28, 29) Mwina kusinkhasinkha zina mwa mfundo zimene Yesu anatchula m’pemphero lake lachitsanzo ndiyeno n’kuona mmene mfundo zimenezi zikugwirizanira ndi mmene moyo wathu ulili zingathandize. (Mateyu 6:9-13) Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti ndi mbali yochepa iti imene tikufuna kuchita pa kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Yehova padziko lapansi pano. Kodi tingamuuze Yehova kuti tikufuna atigwiritsire ntchito mmene angathere ndi kum’pempha kuti atithandize pogwira ntchito iliyonse imene watipatsa? Kodi talema chifukwa chodera nkhaŵa zinthu zofunika pa moyo wathu? Kodi ndi machimo ati amene tikufuna kuti atikhululukire, ndipo kodi ndi anthu ati amene tikufunika kuwakhululukira kwambiri? Kodi ndi mayesero ati amene tikukumana nawo, ndipo kodi tikuzindikira kuti tikufunika mwamsanga chitetezo cha Yehova pankhani imeneyi?

20 Kuwonjezera pamenepo, tingaganizire anthu omwe tikuwadziŵa amene akufunika kwambiri thandizo la Yehova. (2 Akorinto 1:11) Komabe, sitifunika kuiwala kuthokoza. Ngati tiima kaye ndi kuganizira zimenezo, tingaone kuti tili ndi zifukwa zoyamikirira ndi kutamanda Yehova tsiku lililonse chifukwa cha zabwino zonse zimene amatichitira. (Deuteronomo 8:10; Luka 10:21) Kuchita zimenezo kulinso ndi phindu lina. Kungatithandize kuti tiuone bwino kwambiri moyo ndi kuuyamikira.

21. Kodi ndi kuphunzira zitsanzo za m’Malemba ziti kumene kungatithandize tikamapemphera kwa Yehova?

21 Kuphunzira kungawongolerenso mapemphero athu. M’Mawu a Mulungu muli mapemphero abwino kwambiri a amuna ndi akazi okhulupirika. Mwachitsanzo, ngati vuto lalikulu likutisoŵetsa mtendere, limene lingatichititse kukhala ndi nkhaŵa ngakhale kuchita mantha kuti moyo wathu kapena wa anthu amene timawakonda ukhala pa ngozi, tingaŵerenge pemphero la Yakobo lokhudza kukumana kwake ndi mkulu wake Esau amene anali wokwiya. (Genesis 32:9-12) Kapena tingaŵerenge pemphero la Mfumu Asa pamene ankhondo pafupifupi wani miliyoni a Akusi anaopseza anthu a Mulungu. (2 Mbiri 14:11, 12) Ngati tikuvutika mumtima chifukwa cha vuto limene linganyozetse mbiri yabwino ya Yehova, kungakhale kopindulitsa kuona pemphero limene Eliya anapemphera pamaso pa olambira Baala pa phiri la Karimeli. Kapenanso tingaone pemphero la Nehemiya lokhudza mzinda wopasuka wa Yerusalemu. (1 Mafumu 18:36, 37; Nehemiya 1:4-11) Kuŵerenga ndi kusinkhasinkha mapemphero amenewo kungalimbitse chikhulupiriro chathu ndiponso kutisonyeza mmene tingam’fikire bwino kwambiri Yehova ndi mavuto amene akutidetsa nkhaŵa.

22. Kodi lemba la chaka cha 2003 ndi liti, ndipo tingadzifunse chiyani nthaŵi ndi nthaŵi m’chaka chonsechi?

22 Inde, palibe chinthu kapena cholinga chabwino kwambiri choposa kumvera langizo la Yakobo lakuti: “Yandikirani kwa Mulungu.” (Yakobo 4:8) Tiyeni tichite zimenezo mwa kupitiriza kum’dziŵa Mulungu, kuyesetsa kusonyeza kum’konda kwathu, ndiponso kukhala naye pa ubwenzi wapamtima popemphera. M’chaka chonse cha 2003, pamene tikukumbukira Yakobo 4:8 monga lemba lachaka, tiyeni tipitirize kudzipenda kuti tione ngati tikuyandikiradi kwa Yehova. Nanga bwanji mbali yomaliza ya mawuwo? Kodi Yehova “adzayandikira kwa inu” motani, ndipo zingakupindulitseni chiyani? Nkhani yotsatirayi idzafotokoza mfundo imeneyo.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani kuyandikira kwa Yehova sitiyenera kukuona ngati nkhani yamaseŵera?

• Kodi tingaike zolinga zina zotani pankhani ya kum’dziŵa Yehova?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamukondadi Yehova?

• Kodi ndi njira ziti zimene tingakulitsire ubwenzi wathu ndi Yehova m’pemphero?

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Lemba la chaka cha 2003 lidzakhala lakuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”​—Yakobo 4:8.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Atakula, Samueli anadzam’dziŵa bwino kwambiri Yehova

[Chithunzi patsamba 12]

Pemphero la Eliya pa phiri la Karimeli ndi chitsanzo chabwino kwa ife

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena