Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w03 7/1 tsamba 8
  • Chikondi Chapamwamba Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi Chapamwamba Kwambiri
  • Nsanja ya Olonda—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumatsatira “Njira Yopambana” ya Chikondi?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • ‘Chachikulu cha Izi Ndicho Chikondi’
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chikondi (Agape)—Zimene Sichili ndi ZImene Chili
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Koposa Zonse Mukhale Nacho Chikondano Chenicheni”
    Dikirani!
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2003
w03 7/1 tsamba 8

Chikondi Chapamwamba Kwambiri

NTHAŴI zambiri m’Malemba Achigiriki Achikristu, kapena kuti Chipangano Chatsopano, pamene timapeza liwu loti “chikondi” alimasulira kuchokera ku liwu lachigiriki lakuti a·gaʹpe.

Pofotokoza tanthauzo la liwu limenelo, buku la Insight on the Scripturesa limati: “[Chikondi cha a·gaʹpe] sindicho kutengeka mtima, kumene munthu amakhala nako chifukwa cha kugwirizana kwake ndi munthu winayo, monga mmene anthu amaganizira nthaŵi zambiri, koma ndi chikondi cha makhalidwe abwino chimene munthu amakhala nacho pochivomereza monga mfundo yofunika, kuona kuti ndi udindo wake kutero, ndiponso kuti ndi khalidwe lofunika, kufunira zabwino munthu wina malinga ngati zili zoyenera. (Chikondi cha) a·gaʹpe chimachititsa munthu kusonyeza chikondi ngakhale pamene pali udani. Sichimalola udani kupangitsa munthu kulephera kutsatira mfundo zabwino zachikhalidwe mwa kubwezera choipa.”

Chikondi cha a·gaʹpe chingaphatikizeponso malingaliro amphamvu. Mtumwi Petro analangiza kuti: ‘Mukhale nacho chikondano [a·gaʹpe] chenicheni mwa inu nokha.’ (1 Petro 4:8) N’chifukwa chake, tinganene kuti chikondi cha a·gaʹpe chimakhudza mtima ndiponso maganizo. Bwanji osapenda malemba amene amasonyeza mphamvu ndi ukulu wa chikondi chapamwamba chimenechi? Malemba otsatirawa angakhale othandiza: Mateyu 5:43-47; Yohane 15:12, 13; Aroma 13:8-10; Aefeso 5:2, 25, 28; 1 Yohane 3:15-18; 4:16-21.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena