Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 12/1 tsamba 24-25
  • Yeremiya Sanasiye Kutumikira Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yeremiya Sanasiye Kutumikira Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tsiku Lililonse Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Yeremiya Sanasiye Kulankhula za Yehova
    Phunzitsani Ana Anu
  • Khalani Wolimba Mtima Ngati Yeremiya
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Yehova Anauza Yeremiya Kuti Azilalikira
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2009
w09 12/1 tsamba 24-25

Phunzitsani Ana Anu

Yeremiya Sanasiye Kutumikira Mulungu

KODI nthawi ina unakhumudwapo n’kuganiza zongosiya kutumikira Mulungu?​—a Ambiri anayamba aganizapo choncho ndipo Yeremiya ali mnyamata anaganizaponso choncho. Komabe, sanalole zonena kapena zochita za anthu ena kumusiyitsa kutumikira Mulungu. Tiye tikambirane zimene zinachititsa Yeremiya kuti azikondedwa kwambiri ndi Mulungu, ngakhale kuti nthawi ina ankafuna kusiya kumutumikira.

Yeremiya asanabadwe, Mulungu woona, Yehova, anamusankha kuti akhale mneneri n’cholinga choti akachenjeze anthu omwe ankachita zinthu zimene Mulungu samasangalala nazo. Kodi ukudziwa zimene Yeremiya anauza Yehova patapita zaka zingapo?​— Iye anati: “Sindithai kunena pakuti ndili mwana.”

Kodi ukuganiza kuti Yehova anamuyankha chiyani Yeremiya?​— Yehova anamuyankha mosapita m’mbali koma mwachikondi kuti: “Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza. Usaope.” Kodi Mulungu anamuuza kuti asaope chifukwa chiyani? Yehova anati: “Chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe.”​—Yeremiya 1:4-8.

Komabe monga mmene taonera, nthawi ina Yeremiya anakhumudwa chifukwa ankanyozedwa potumikira Mulungu. Iye anati: “Ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.” Choncho anaganiza zongosiya kutumikira Mulungu. Ndipo anati: “Sindidzam’tchula [Yehova], sindidzanenanso m’dzina lake.” Koma kodi Yeremiya anasiyadi kutumikira Mulungu?

Yeremiya anati: ‘Mu mtima mwanga mawu a Yehova ali ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira.’ (Yeremiya 20:7-9) Ngakhale kuti Yeremiya nthawi zina ankaopa, sanasiye kutumikira Yehova chifukwa chomukonda. Tiye tione mmene Yeremiya anatetezedwera chifukwa chosasiya kutumikira Mulungu.

Yehova anamuuza Yeremiya kuchenjeza anthu kuti Yerusalemu awonongedwa ngati anthuwo sasiya kuchita zoipa. Yeremiya atawachenjeza, anthuwo anakwiya n’kumati: “Munthu uyu ayenera kufa.” Koma Yeremiya, anawachonderera kuti ‘amvere mawu a Yehova.’ Ndiyeno anawauza kuti: ‘Mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, pakuti Yehova wandituma kwa inu.’ Kodi ukudziwa chimene chinachitika kenako?​—

Baibulo limanena kuti: “Akulu ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa; pakuti watinenera ife m’dzina la Yehova Mulungu wathu.” Choncho, Yehova anamuteteza Yeremiya chifukwa choti sanasiye kumutumikira chifukwa cha mantha. Tsopano tiye tione zimene zinachitikira Uriya, mneneri winanso wa Yehova, amene anachita zinthu mosiyana ndi Yeremiya.

Baibulo limanena kuti: ‘Uriya ananenera Yerusalemu monga mwa mawu onse a Yeremiya.’ Kodi ukudziwa zimene Uriya anachita mfumu Yehoyakimu itamukwiyira?​— Anachita mantha n’kusiya kutumikira Mulungu ndipo anathawira ku Iguputo. Choncho mfumu inatuma anthu kukamutengako. Kodi ukudziwa zimene mfumu yoipayi inachita anthuwa atabwera naye?​— Inapha Uriya ndi lupanga.​—Yeremiya 26:8-24.

Kodi ungati n’chifukwa chiyani Yehova anateteza Yeremiya, osati Uriya?​— Yeremiya ayenera kuti anali ndi mantha mofanana ndi Uriya, koma sanasiye kutumikira Yehova ndipo sanathawe. Iye sanasiye kutumikira Mulungu. Kodi ukuona kuti tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yeremiya?​— Tikuphunzira kuti nthawi zina zimakhala zovuta kuchita zimene Mulungu watiuza, koma tiyenera kumukhulupirira ndi kumumvera nthawi zonse.

a Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, mukapeza pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.

Mafunso:

  • Kodi Mulungu anapatsa Yeremiya ntchito yotani?

  • N’chifukwa chiyani Yeremiya ankafuna kusiya kutumikira Mulungu?

  • N’chifukwa chiyani Yeremiya anatetezedwa koma Uriya ayi?

  • Kodi waphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yeremiya?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena