Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 2/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Uthenga Wabwino ndi Wochokeradi kwa Mulungu?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Baibulo Nlochokeradi kwa Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?
    Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 2/1 tsamba 16
Mpukutu wakale wa Baibulo

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Baibulo ndi Mawudi a Mulungu?

Timayembekezera kuti buku lochokera kwa Mulungu liyenera kukhala lapadera kwambiri. Baibulo ndi buku lotero. Pali Mabaibulo ambirimbiri amene asindikizidwa ndipo ali m’zinenero zambiri. Malangizo amene amapezeka m’Baibulo, amathandiza anthu kusintha n’kukhala abwino.—Werengani 1 Atesalonika 2:13; 2 Timoteyo 3:16.

Tikudziwa kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu chifukwa limalosera molondola za m’tsogolo. Palibe munthu amene angathe kuneneratu zam’tsogolo, pokhapokha atatsogoleredwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo taganizirani za buku la Yesaya. Mpukutu wa bukuli womwe unalembedwa zaka 100 Yesu asanabadwe, unapezeka kuphanga lina pafupi ndi Nyanja Yakufa. Mpukutuwu unanena kuti mzinda wa Babulo udzakhala bwinja. Mawu amenewa anakwaniritsidwa patapita zaka zambiri kuchokera pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi.—Werengani Yesaya 13:19, 20; 2 Petulo 1:20, 21.

Kodi Baibulo linalembedwa bwanji?

Baibulo linalembedwa kwa zaka zoposa 1,600. Anthu 40 amene analemba Baibulo analemba zinthu zogwirizana, pa mutu wankhani umodzi. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Zinatheka chifukwa choti Mulungu ndi amene ankawatsogolera.—Werengani 2 Samueli 23:2.

Nthawi zina Mulungu ankalankhula ndi anthu amene analemba Baibulo kudzera mwa angelo, masomphenya kapena maloto. Nthawi zambiri, Mulungu ankaika m’maganizo a wolembayo mfundo zimene akufuna kuti zilembedwe, ndipo ankalola munthuyo kusankha yekha mawu amene akufuna kugwiritsa ntchito polemba mfundozo.—Werengani Chivumbulutso 1:1; 21:3-5.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 2 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Mungapange dawunilodi bukuli pa www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena