Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 9/1 tsamba 7
  • N’chifukwa Chiyani Timalalikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Timalalikira?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?
    Kodi Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo Tingawapeze Kuti?
  • Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Yesetsani Kudziwa Bwino Webusaiti Yathu ya JW.ORG
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Webusaiti Yathu Yovomerezeka Yakonzedwa Kuti Izithandiza Ifeyo Komanso Anthu Ena
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 9/1 tsamba 7
A Mboni za Yehova awiri akulalikira kunyumba za anthu

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI A MBONI ZA YEHOVA NDI ANTHU OTANI?

N’chifukwa Chiyani Timalalikira?

Anthu ambiri amatidziwa bwino chifukwa cha ntchito yolalikira, yomwe timagwira padziko lonse. Timalalikira kunyumba ndi nyumba, m’malo opezeka anthu ambiri komanso kulikonse komwe timapeza anthu. Koma kodi n’chifukwa chiyani timalalikira?

Timalalikira pofuna kulemekeza Mulungu komanso kuthandiza anthu ena kudziwa dzina lake. (Aheberi 13:15) Timachitanso zimenezi pomvera zimene Yesu ananena. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mateyu 28:19, 20.

Timalalikiranso chifukwa choti timakonda anthu ena. (Mateyu 22:39) Timadziwa kuti anthu omwe timawalalikira ali ndi zipembedzo zawo komanso kuti si onse amene amasangalala ndi uthenga wathu. Komabe, timachita zimenezi chifukwa timadziwa kuti uthenga wa m’Baibulo udzathandiza kuti anthu adzapulumuke. N’chifukwa chake ‘timapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.’—Machitidwe 5:41, 42.

Nyuzipepala ina ya ku Venezuela inanena zimene katswiri wina wophunzira za chikhalidwe cha anthu, dzina lake Antonio Cova Maduro, analemba zokhudza a Mboni za Yehova. Inati: “A Mboni za Yehova amagwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri ndiponso amalolera kuzunzidwa . . . n’cholinga choti uthenga wawo womwe ndi wofunika kwambiri ufike padziko lonse.”—El Universal.

Anthu ambiri amene amawerenga mabuku athu, si a Mboni. Ndiponso anthu ambiri omwe timaphunzira nawo Baibulo, ali ndi zipembedzo zawo. Komabe anthuwa amasangalala kwambiri tikafika kunyumba zawo.

Tikudziwa kuti pali zambiri zomwe mungafune kudziwa zokhudza a Mboni za Yehova. Choncho, pali njira zingapo zomwe zingakuthandizeni kudziwa zambiri.

  • Mungafunse wa Mboni za Yehova aliyense.

  • Mungapite pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny.

  • Mukhozanso kufika pa misonkhano yathu. Misonkhanoyi imachitika kwaulere ndipo aliyense ndi wolandiridwa.

Yesu akutumiza ophunzira ake awiri kukalalikira
Phiri lokhala ndi chipale chofewa pamwamba pake

Kuti mudziwe zambiri zokhudza Mboni za Yehova, onerani vidiyo yamutu wakuti, Mboni za Yehova—Gulu Limene Likulalikira Uthenga Wabwino, pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny. (Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MAVIDIYO)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena