Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w15 11/1 tsamba 9
  • Kodi Mukudziwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yehova Sanamuiwale Yosefe
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • “Kodi Ine Ndatenga Malo a Mulungu?”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 11/1 tsamba 9

KODI MUKUDZIWA?

N’chifukwa chiyani Yosefe anayamba wameta asanakaonane ndi Farao?

Chithunzi chojambulidwa pakhoma chosonyeza munthu akumeta tsitsi

Chithunzi chojambulidwa pakhoma chosonyeza munthu akumeta tsitsi

Buku la Genesis limanena kuti Farao analamula zoti mkaidi wina wachiheberi amasulidwe mwamsanga. Ankafuna kuti mkaidiyo amasulire maloto ake omwe anali atamuzunguza mutu. Mkaidiyu anali Yosefe ndipo anali atakhala m’ndende kwa zaka zingapo. Ngakhale kuti Farao ankamufuna mwamsanga, Yosefe anayamba wameta kaye. (Genesis 39:20-23; 41:1, 14) Zimene anachitazi zikusonyeza kuti ankadziwa bwino chikhalidwe cha anthu a ku Iguputo.

Mitundu yambiri kuphatikizapo Aheberi, inkakonda kusunga ndevu. Koma mosiyana ndi zimenezi, buku lina limanena kuti, “ndi anthu a ku Iguputo okha omwe sankagwirizana ndi zoti munthu azisunga ndevu.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature.

Kodi anthu a ku Iguputo ankangometa ndevu zokha basi? Magazini inanso inanena kuti munthu akamapita kwa Farao ankafunika kudzikonza bwinobwino ngati kuti akupita kukachisi. (Biblical Archaeology Review) Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti Yosefe ankafunika kumeta tsitsi ndi ndevu zomwe.

Buku la Machitidwe limanena kuti bambo a Timoteyo anali Mgiriki. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti anali wochokera ku Girisi?

Yunike akuwerengera Timoteyo ndipo bambo ake ali kumbuyo

Ayi. Mtumwi Paulo analemba makalata ambiri mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. Pamene ankalemba makalatawa ankakonda kusiyanitsa Ayuda ndi Agiriki. Mwachitsanzo, ankatchula anthu onse amene sanali Ayuda kuti Agiriki kapena Ahelene. (Aroma 1:16; 10:12) N’kutheka kuti Paulo ankanena zimenezi chifukwa anthu ambiri a m’madera amene Paulo ankalalikira ankalankhula komanso kutsatira miyambo ya Agiriki.

Koma kodi anthu a nthawi imeneyo ankaona kuti Mgiriki ndi munthu wochokera ku Girisi yekha basi? M’zaka za m’ma 300 B.C.E., munthu wina wodziwa kulankhula pagulu wa ku Atene, dzina lake Isocrates, ananena kuti chikhalidwe cha Agiriki chinkafalikira ngati moto. Anati chifukwa cha zimenezi, “anthu amene anachita maphunziro a Agiriki ndi amene ankaonedwa kuti ndi Agiriki kuposa nzika zenizeni za dziko la Girisi.” Choncho, ngakhale kuti Paulo anatchula anthu ena komanso bambo a Timoteyo kuti anali Agiriki, n’kutheka kuti sanali ochokera ku Girisi, koma ankangotsatira miyambo ya Agirikiwo.​—Machitidwe 16:1

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena