Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 1 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?
  • Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?
  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira??
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chiyani Chimachitika pa Imfa?
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?
    Galamukani!—2007
  • Funso Lachiwiri: Kodi Chidzandichitikire N’chiyani Ndikadzamwalira?
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 1 tsamba 16
Duwa lili pachiliza

KODI BAIBULO LIMANENA ZOTANI?

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake ngati nyama kapena chinthu chinachake. Pamene ena amakhulupirira kuti munthu akafa, ndiye kuti zake zathera pomwepo. Nanga inuyo mumakhulupirira zotani?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Choncho munthu akamwalira, ndiye kuti kulibenso.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Adamu atamwalira anabwereranso kufumbi. (Genesis 2:7; 3:19) Masiku anonso anthu onse amene amamwalira, amabwerera kufumbi.—Mlaliki 3:19, 20.

  • Anthu amene amwalira amakhala kuti amasuka ku machimo awo. (Aroma 6:7) Umenewu ndi umboni wakuti munthu akamwalira, sapita kwinakwake kukalangidwa chifukwa cha machimo amene anachita.

Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?

KODI MUNGAYANKHE KUTI . . .

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Kudzakhala kuuka.”—Machitidwe 24:15.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Nthawi zambiri Baibulo limayerekezera imfa ndi tulo. (Yohane 11:11-14) Mulungu adzaukitsa akufa ngati mmene timadzutsira munthu akagona.—Yobu 14:13-15.

  • M’Baibulo muli nkhani za anthu ambiri amene anaukitsidwa. Zimenezi zimatitsimikizira kuti Mulungu adzaukitsadi akufa.—1 Mafumu 17:17-24; Luka 7:11-17; Yohane 11:39-44.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 6 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena