Mawu Oyamba
Kodi Mukuganiza Bwanji?
M’dzikoli timakumana ndi mavuto ambiri. Kodi pali amene angatithandize komanso kutilimbikitsa?
Baibulo limati: “Tate wachifundo chachikulu [yemwe] ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
Nsanja ya Olonda imeneyi ikufotokoza zimene Mulungu amachita potilimbikitsa.