Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp17 No. 2 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi tili ‘m’masiku otsiriza’?
  • Kodi zinthu zidzakhala bwanji m’tsogolo?
  • Kodi Dzikoli Lithadi Posachedwa?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi “ya Mapeto” N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
wp17 No. 2 tsamba 16
Ana ndiponso akuluakulu akusangalala m’dziko latsopano

Anthu amene adzapulumuke adzakhala m’dziko lokongola kwambiri

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi tili ‘m’masiku otsiriza’?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Ulosi wa m’Baibulo komanso zimene zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Linaneneratu kuti m’masiku otsiriza padzakhala nkhondo, njala, zivomerezi ndiponso matenda oopsa.—Mateyu 24:3, 7; Luka 21:11.

  • Linaneneratunso kuti m’masiku otsiriza anthu ambiri adzakhala ndi makhalidwe oipa komanso sadzakonda Mulungu.—2 Timoteyo 3:2-5.

Kodi zinthu zidzakhala bwanji m’tsogolo?

Anthu ena amakhulupirira kuti . . . pa mapeto pa masiku otsiriza, dziko ndiponso anthu onse adzawonongedwa, pomwe ena amakhulupirira kuti zinthu zidzayamba kuyenda bwino. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Pa mapeto pa masiku otsiriza anthu onse oipa adzawonongedwa.—1 Yohane 2:17.

  • Dziko lidzasinthidwa kuti likhale lokongola kwambiri.—Yesaya 35:1, 6.

Kuti mudziwe zambiri zokhudza “masiku otsiriza,” werengani mutu 9 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena