Mawu Woyamba
Kodi M’tsogolomu Muli Zotani?
Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti tsogolo lanu komanso la banja lanu lidzakhala lotani? Baibulo limati:
“Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
Nsanja ya Olonda iyi ikuthandizani kudziwa cholinga cha Mulungu kwa anthu komanso dzikoli. Ikufotokozanso zimene mungachite kuti mudzasangalale cholingachi chikadzakwaniritsidwa.