Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp19 No. 1 tsamba 3
  • Kodi Mulungu Ndi Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Ndi Ndani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kudziwa Bwino Mulungu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mumawadziwa Atate Wanu wa Kumwamba?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Mukudziwa Zotani Zokhudza Mulungu?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
wp19 No. 1 tsamba 3
Munthu akuchita chidwi ndi malo okongola

Kodi Mulungu Ndi Ndani?

Anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira Mulungu. Koma mukawafunsa kuti Mulungu ndi ndani, amayankha zosiyanasiyana. Ena amaona kuti Mulungu ndi woweruza wankhanza amene amangoganizira zopereka chilango kwa anthu olakwa. Pomwe ena amaona kuti Mulungu amakonda komanso kukhululukira anthu nthawi zonse, kaya anthuwo achita zotani. Ndiye palinso ena amene amaona kuti Mulungu ali kutali kwambiri ndipo alibe nafe chidwi. Chifukwa choti pali maganizo osiyanasiyana chonchi onena za Mulungu, anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka kudziwa kuti zoona ndi ziti.

Kodi kudziwa zolondola kuli ndi phindu lililonse? Inde. Kudziwa zolondola zokhudza Mulungu kungakuthandizeni kwambiri. (Machitidwe 17:26-28) Mukamayesetsa kumuyandikira kwambiri, m’pamenenso iye amakuthandizani komanso kukukondani kwambiri. (Yakobo 4:8) Chofunikanso kwambiri n’chakuti, kudziwa Mulungu molondola kungakuthandizeni kuti mudzakhale ndi moyo wosatha.​—Yohane 17:3.

Kodi mungatani kuti mumudziwe Mulungu? Taganizirani za munthu amene mumamudziwa bwino, mnzanu wapamtima. Kodi zinayamba bwanji kuti munthuyo afike pokhala mnzanu? Muyenera kuti poyamba munadziwa dzina lake, makhalidwe ake, zimene amakonda, zimene amadana nazo, zimene wachita, zimene amafuna kudzachita ndi zina zambiri. Choncho tingati munaphunzira zokhudza munthuyo ndipo zimenezi ndi zimene zinachititsa kuti muyambe kumukonda.

N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Kudziwa mayankho a mafunso otsatirawa kungatithandize kuti timudziwe bwino:

  • KODI DZINA LA MULUNGU NDI NDANI?

  • KODI ALI NDI MAKHALIDWE OTANI?

  • KODI MULUNGU WACHITA ZINTHU ZITI?

  • KODI M’TSOGOLO ADZACHITA CHIYANI?

  • KODI KUDZIWA MULUNGU KUNGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Magaziniyi yakonzedwa n’cholinga choti itithandize kupeza mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa. Nkhani zimene zili m’magaziniyi zikuthandizani kudziwa zolondola zokhudza Mulungu. Zikuthandizaninso kudziwa mmene kukhala naye pa ubwenzi wolimba kungakuthandizireni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena