Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/02 tsamba 1
  • Makolo—Kodi Ana Anu Akukula Mwauzimu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo—Kodi Ana Anu Akukula Mwauzimu?
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Makolo ndi Ana Ayenera Kulankhulana Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 4/02 tsamba 1

Makolo—Kodi Ana Anu Akukula Mwauzimu?

1 Kukhala ndi ana okonda kutumikira Yehova kumasangalatsa kwambiri. Zimenezi zimakondweretsa kwambiri makolo odzipereka. Mtumwi Yohane anasangalala moteromo ndi ana ake auzimu, pamene analemba kuti, “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti ali kuyenda m’choonadi.”—3 Yoh. 4.

2 Makolo ambiri amafunsa kuti “Kodi ungatani kuti ana ako azikonda zinthu zauzimu?” Limeneli ndi funso labwino kwambiri tikaona mavuto amene Satana akubweretsa pa ana masiku ano. Zimene anena makolo amene alera bwino ana awo, zingathandize kwambiri. Bambo wina anati: “Chofunika kwambiri n’chakuti muziyamba ndinu kukonda zinthu zauzimu.” Mbale ameneyu ali ndi ana anayi ofuna kuwasamala ndipo ndi mkulu wotanganidwa koma amapeza nthaŵi yocheza ndi ana akewo. Iwo amakonda zinthu za Ufumu. M’banja lawo amakambirana zinthu zauzimu. Popita ku tchuti, amapita banja lonse ndipo bambo amaonetsetsa kuti kumene apitako azikapezeka pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu.

3 Chofunikanso ndi kuonetsetsa kuti utumiki wa kumunda ukusangalatsa. Mayi wina ananena kuti anayamba kupita ndi ana ake mu utumiki wa kumunda kuyambira anawo ali makanda. Iwo akamapita mu utumiki, sichikhala chifukwa chakuti alibe chochita koma chifukwa chakuti amaukonda.

4 Masukani Polankhulana: Kodi mungadziŵe bwanji kuti ana anu akukula mwauzimu ngati simumasuka polankhulana? Kunena zoona, simungadziŵe. N’chifukwa chake makolo ambiri amene alera bwino ana awo aona kuti kukhala omasuka polankhulana ndi ana awo n’kwanzeru. Amachezera limodzi. M’malo mopita okha kukacheza ndi akuluakulu anzawo, amaona kuti ndi bwino kutenganso ana awo. Choncho sipakhala kucheza kosankhana misinkhu. Makolo anzeru amakhalanso achidwi kwambiri ndi zimene ana awo amachita kusukulu kapena kwina kulikonse. Ngati makolo asonyeza chidwi chotere kwa ana, anawo amamasuka kuuza makolo awo mavuto amene apeza, ndipo amakhulupirira kuti makolo awo amvetsa ngakhale kuti anawo alakwa.—Miy. 15:14.

5 Makolo ena aona kuti ndi kwanzeru kumvetsera mwatcheru zimene ana awo akunena. Amafufuza zimene ana awo akuphunzira panyumba ndiponso kwina, ndiyeno amachotsa maganizo onse olakwika asanakhazikike m’mitima mwa ana awo. Makolo anzeru saganiza kuti zimene ana awo akunena n’zosafunika, koma amayesetsa kuwalimbikitsa kuti asasiye kumenya nkhondo kuti akhalebe olimba mwauzimu m’dziko lino lokonda chuma. (Aef. 6:10-13) Chikondi choterechi chimathandiza makolo ndi ana kukhala ogwirizana.—Miy. 24:5.

6 Kuphunzira Mawu a Mulungu Pamodzi: Phunziro la Baibulo lokhazikika n’lofunikanso kuti ana akule mwauzimu. Ana akaona kuti makolo awo amakonda kwambiri kuphunzira Baibulo ndipo mlungu uliwonse amapatula nthaŵi yophunzira, nawonso amaphunzira kuchita zomwezo. Kuwonjezera pa nthaŵi imene amakambirana nkhani zina za m’mabuku kapena magazini mlungu uliwonse, makolo ozindikira amalangiza kapena kulimbikitsa ana awo zilizonse zimene zingawathandize pakali pano. Zochitika kusukulu kapena kuderalo zingafune kuti aphunzire nkhani ina yake kuti anawo athane ndi vuto limenelo kapena ndi nkhani inayake. Kukula mwauzimu kumafuna zimenezi.

7 Kuwapatsa Chuma Chauzimu: Makolo ena amaganiza molakwika kuti ngati pali zabwino zimene angachitire ana awo ndi kuwapatsa chuma chakuthupi. Zochitika zikusonyeza kuti makolo akakhala okondetsetsa chuma, amafooka mwauzimu ndiponso amasiya kuphunzitsa ana awo zauzimu. (Marko 8:36) Ngakhale kuti akhoza kukhala ndi moyo wapamwamba, kodi ndi bwino kuwononga moyo wauzimu chifukwa cha zimenezi? Mabanja ena asankha kuchepetsa zofunika pamoyo wawo kuti asaiŵale cholinga chawo chenicheni. (Yoh. 6:27) Aphunzira kukhutira ndi chuma chochepa, koma apindula mwauzimu ndipo zimenezi zawathandiza iwo ndi ana awo.

8 Kodi mumadera nkhaŵa kwambiri moyo wauzimu wa banja lanu? Ngati mumatero, bwanji osayesetsa kukundikira pamodzi chuma chauzimu chenicheni? (Mat. 6:19-21) Thandizani ana anu kukula mwauzimu ndipo inunso mudzasangalala kuti ‘ana anu ali kuyenda m’choonadi.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena