Kodi Mumapanga Zolinga Zauzimu Monga Banja?
1 Monga anthu odzipatulira tili ndi cholinga chotumikira Yehova mokhulupirika. Ndiponso timayembekeza mwachidwi kulandira mphatso ya moyo wosatha. Ndithudi, sitimangofuna kuti tikhulupirike ndi kupulumuka tokha basi. Timafunanso kuthandiza ena kukhala ndi zolinga zomwezi, makamaka timafuna kuthandiza banja lathu.—Yoh. 1:40, 41; 1 Tim. 5:8.
2 Monga mmene amakwerera phiri mwapang’onopang’ono, ifenso tingapite patsogolo m’njira yathu yachikristu mwapang’onopang’ono. Pachifukwa chimenechi timakhala ndi zolinga zauzimu zathuzathu. Izi sizongofunika munthu aliyense payekha basi. Mabanjanso angakhale ndi zolinga zokhudza misonkhano, utumiki wakumunda, ndiponso phunziro la banja. Kodi pali pena pamene pakufunika kuwongolera? Kodi ena m’banjamo angathandizidwe kukhala ndi cholinga cha utumiki wanthaŵi zonse? Kukambirana kwa banja kungathandize kukwaniritsa zolinga zimene mukufunitsitsa. Pamene zimenezi zakwaniritsidwa, mungakhalenso ndi zolinga zina zateokalase. Choncho, pang’onopang’ono, mungapite patsogolo mwauzimu.
3 Misonkhano: Mabanja ena angafune kukhala ndi cholinga chofika pamisonkhano nthaŵi yabwino. Zimenezi zingakhale zovuta kwambiri kwa mabanja akuluakulu, kwa awo amene ali ndi ndandanda ya ntchito yothinana, kapena kumene kuli vuto la zoyendera. Zofunika ndi kugwirizana ndiponso kulinganiza zinthu bwino.
4 Cholinga china chabwino chimene banja liyenera kukhala nacho ndicho choyankha pamisonkhano. Ena a m’banjamo angasankhe kuŵerenga ndemanga zifupizifupi. Komabe, kukhala ndi ndemanga zachidule ndi zachindunji m’mawu athuathu kumasonyeza kupita patsogolo mwauzimu ndipo n’kopindulitsa. Anthu a m’banja angathandizane kukonzekera ndemanga zawo. Angathandizanenso kupita patsogolo mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Izi zingaphatikizepo kumvetsera ana an’gonoang’ono a m’banjamo akuyeserera nkhani zawo, kuwaphunzitsa mmene angagwiritsirire ntchito autilaini, kuwathandiza katchulidwe ka mawu, ndi zina zotero. Cholinga chokhala mphunzitsi wabwino kapena woŵerenga wabwino kwambiri kumaso kwa anthu chimafuna khama ndithu.—1 Tim. 4:13.
5 Utumiki Wakumunda: Mabanja ena amafuna kuloŵa mu utumiki wakumunda mokhazikika. Kodi banja lanu lonse limapita mu utumiki wakumunda pamodzi? Palinso cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba kapena kumachititsa mokhazikika kwambiri phunziro limene muli nalo kale.
6 Phunziro la Banja: M’mabanja ena kungakhale kovuta kwambiri kutsatira ndandanda ya phunziro la banja. Nthaŵi zina kungakhale koyenera kusintha nthaŵi ya phunzirolo. Koma izi ziyenera kukhala za kamodzikamodzi. Cholinga china chabwino kwambiri ndicho kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu mokhazikika, ngakhalenso kuchita zimenezi paphunziro la banja. Kwa anthu ambiri, kuŵerenga kwenikweni ndime za mlungu umenewo kumatha nthaŵi yokwanira mphindi 20-25 zokha basi. Kungathandize kuwonjezera chidziŵitso chathu cha m’Malemba ndipo kumapangitsa kapendedwe ka mfundo zazikulu za Baibulo kwa mlungu uliwonse kukhala kosangalatsa kwambiri.
7 Pali zolinga zina zambiri zedi zimene aliyense payekha ndiponso mabanja angakhale nazo. Mwachitsanzo, bwanji za khama la banja la kuchita upainiya wothandiza mwezi umodzi? Komanso, molinganiza zinthu bwino ndiponso kugwirizana, kodi banja lingathandize kuti mwina m’modzi m’banjamo akhale mpainiya wokhazikika? Palinso cholinga chokhala mtumiki wotumikira kapena mkulu? Abale achinyamata angakhale ndi cholinga chochita utumiki wa pa Beteli. Zolinga zimenezi n’zotheka, koma zimafuna khama ndi kugwira ntchito molimba. Pamene tikuyesetsa kukwaniritsa zolinga zathu ndiponso zabanja, utumiki wathu kwa Yehova udzasintha, zonse ku ulemu ndi ulemerero wake.—Sal. 96:7, 8.