Bokosi la Mafunso
◼ Ndi liti pamene munthu angayenere kulandira buku lakelake la Olinganizidwa Kukwaniritsa Utumiki Wathu, ndipo kodi akulu angalinganize motani ndiponso liti kupenda mafunso ndi anthu ofuna kubatizidwa?
Nkhani yokhudza zimenezi ili m’buku la Utumiki Wathu pa masamba 173-5, pamutu wakuti “Mawu kwa Akulu a Mpingo.” Pamenepo pamafotokoza kuti munthu akagwirizanitsa moyo wake ndi miyezo yolungama ya Yehova ndipo amafika pamisonkhano mokhazikika, angakumane ndi akulu aŵiri kuti am’pende ngati akuyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Ngati akuyenera, m’pamene angakhale ndi buku la Olinganizidwa Kukwaniritsa Utumiki Wathu.—Onaninso masamba 97-100 za “wofalitsa wosabatizidwa.”
Akapeza bukuli, wofalitsa wosabatizidwa ayenera kuyamba kuphunzira mafunso a ubatizo kuyambira patsamba 175. Ayenera kuyesetsa kuzindikira tanthauzo la malemba amene agwidwa mawu ndi ongosonyezedwa osagwidwa mawu. Akamaliza kuphunzira zimenezo, akulu ena adzapenda naye mafunso ndi mayankho. Woyang’anira wotsogolera ndi amene amalinganiza zimenezi.
Kukonzekera ubatizo sikuyenera kuchitika mothamanga. Choncho, munthu ayenera kuuza akulu nthaŵi ikadalipo pamene akufuna kudzabatizidwa. Akulu sayenera kudikira kuti msonkhano ulengezedwe kuti ayambe kupenda anthu okonzekera ubatizo. Ochititsa maphunziro a Baibulowo ayenera kukhala tcheru kuona mmene ophunzira awo akupitira patsogolo mwauzimu, kuzindikira pamene akuyandikira kudzipatulira, ndi kuwauza mmene angakonzekere ubatizo.
Akulu openda munthu wofuna kubatizidwa angaone kuti munthuyo akufunikabe kupita patsogolo mwauzimu asanatenge sitepe lofunika limeneli. Mwina afunika kuwonjezera chidziŵitso kapena kukhala waluso kwambiri pofotokozera ena chikhulupiriro chake. (1 Pet. 3:15) Zikhoza kukhala kuti akufunika kuzoloŵerabe utumiki wakumunda. Kapena iwo angaone kuti sakuyenera kubatizidwa. (Onani Machitidwe 8:36.) M’mbali zonsezi, akulu ayenera kunena zimene munthuyo akufunika kulimbikira kuti apitebe patsogolo, ndipo ngati n’kofunika, apange makonzedwe alionse ofunika kum’thandiza kuti nthaŵi ina adzayenerere ubatizo.