Mafunso Ophunzirira Brosha ya Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
Mmalo ena m’maphunziro ameneŵa, zilozero zapangidwa ku zawonjezeredwa, masamba 27-31. Ndemanga pa ndime zosonyezedwazo zingaphatikizidwe m’phunzirolo, ndime za zowonjezeredwa zingawerengedwe ngati nthaŵi ilola.
MLUNGU WOYAMBA
Tsamba 2
1-4. Kodi nchifukwa ninji kukambitsirana mmene mwazi ungapulumutsire miyoyo kuli kwapanthawi yake? (Onani tsamba 27, ndime 1-3.)
Tsamba 3
1, 2. Kodi nchifukwa ninji kuli kwachibadwa kulingalira moyo kukhala wogwirizanitsidwa ndi mwazi, ndipo ndimotani mmene Mulungu akuloŵetsedweramo mu nkhanlyi?
3, 4. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala okondweretsedwa ndi zimene Mulungu amanena ponena za mwazi?
5. Kodi pali chifukwa chotani chimene tiyenera kuperekera chisamaliro ku Genesis 9:3-6, ndipo kodi ndime imeneyo ili ndi tanthauzo lotani?
6. Kodi Aisrayeli anali pansi pa mathayo otani pankhani ya mwazi?
Tsamba 4
1, 2. Kodi malamulo a Mulungu anawapindulitsa motani Aisrayeli akale, koma kodi nchiyani chimene chinali chifukwa chachikulu chimene Aisrayeli anapeŵera mwazi?
3. Kodi lamulo la mwazi linayenera kuwonedwa motani panthaŵi yangozi?
Tsamba 5
1, 2. Kodi Yesu anakhazikitsa chitsanzo chotani ponena za lamulo la mwazi?
3, 4. (a) Kodi bungwe la atumwi linanenanji ponena za Akristu ndi mwazi? (b) Kodi timadziŵa motani ngaff lamulo la kusala mwazi linali la pakanthaŵi kochepa kokha?
5. Mogwirizana ndi atumwi a Yesu, kodi kupeŵa mwazi kunali kofunika motani?
6, 7. Kodi ndi umboni wowonjezereka wotani umene umasonyeza kuti lamulo la mwazi linali chofunika chachikhalire?
Tsamba 6
1, 2. Kodi mwazi unagwiritsiridwa ntchito motani m’zamankhwala nthaŵi za Chikristu chisanakhale?
3. Kodi Akristu oyambirira anavomereza motani ku kugwiritsira ntchito mwazi, ngakhale m’zamankhwala, m’nthaŵi za Aroma?
4-6. (a) Kodi kuthiriridwa mwazi kunayamba motani? (b) Polingalira za lamulo la Mulungu, kodi nchifukwa ninji kuthirira mwazi m’mitsempha kukakhala kolakwa?
7. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimakana kuthiriridwa mwazi? (Onani tsamba 27, ndime 4-6, ndi tsamba 28, ndime 1.)
Tsamba 7
1. Ngakhale kuti chifukwa choyamba chimene Akristu amakanira kuthiriridwa mwazi nchachipembedzo, kodi nchifukwa ninji tiyenera kusanthula mbali ya zamankhwala ya kuchiritsa kwamwazi?
MLUNGU WACHIŴIRI
Tsamba 7
2, 3. Kodi kuthiriridwa mwazi kuli ndi mbali yotani m’zamankhwala zamakono?
4, 5. Kodi nchifakwa ninji kuli kwanzeru kulingalira ngati kuthiriridwa mwazi kuli kwaupandu?
Tsamba 8
1. Mwanzeru timafunsa chiyani ponena za kuthiriridwa mwazi?
2, 3. Kodi nchifukwa ninji kuikidwa kwa mwazi m’mitundumitundu ndi kuyerekeza mwazi kuli kofunika koposa koma sikuli kokwanira kwenikweni?
4, 5. Kodi kuthiriridwa mwazi kungapangitse motani mavuto a kudzitetezera kwathupi?
6, 7. Kodi ndi chivulazo chotani chimene kuthiriridwa mwazi kungachite pambuyo pa opaleshoni ya kensa?
Tsamba 9
1. Kodi umboni wonena za kuthiriridwa mwazi ndi opaleshoni ya kensa uli wofunika motani?
2, 3. Kodi kuthiriridwa mwazi kungapangitse chivulazo china chotani cha kudzitetezera kwathupi?
4, 5. Kodi nchifukwa ninji anthu amafunikira kudziŵa za upandu wakugwidwa ndi nthenda kuchokera ku kuthiriridwa mwazi?
Tsamba 10 (Bokosi)
1, 2. Kodi upandu wa kutupa chiwindi kwa m’mwazi ngowopsa motani?
3. Kodi nchifukwa ninji panthaŵi ina kunawonekera ngati kuti upandu wa kugwidwa ndi kutupa chiwindi kwa m’mwazi unali pafupi kuthetsedwa?
4, 5. Kodi ndi zochitika zotani zimene zinatsimikizira kuti upandu wakugwidwa ndi kutupa chiwindi kwa m’mwazi sunafunikire kunyalanyazidwabe?
6-8. Kodi nchifukwa ninji kudera nkhaŵa ndi kugwidwa ndi kutupa chiwindi sikuli nkhani yakale?
Tsamba 11
1. Kodi nchiyani chimene chingasonyeze kuti maupandu a matenda ochokera ku mwazi saali pafupi kutha?
2-4. Kodi mwazi ungayambukiritse motani munthu ku matenda amene saali ofala m’dera lake? (Onaninso bokosi, tsamba 11.)
5-7. Kodi ndimotani mmene mliri wa AIDS wasonyezera kuti matenda atsopano, akupha angakhale ogwirizanitsidwa ndi mwazi?
Tsamba 12
1, 2. Kodi nchifukwa ninji kugwiritsira ntchito njira zopendera zizindikiro za m’thupi kupezera kachirombo kwa AIDS kudakali kopanda chitsimikizo kuti mwazi ulibe upandu?
3-5. Kodi nchifukwa ninji chiwopsezo cha kachirombo ka AIDS sichiri mapeto a nkhaniyo?
6, 7. Kodi ndi nkhaŵa zoyenerera zotani zimene akatswiri ali nazo ponena za tizirombo ta m’mwazi?
MLUNGU WACHITATU
Tsamba 13
1, 2. Kodi ndani amafuna chisamaliro chabwino chamankhwala, ndipo kodi zimenezo zimaphatikizapo chiyani?
3-5. Kodi mungachitire chitsanzo motani kuti pali zoloŵa m’malo za kuthiriridwa mwazi?
6-8. Kodi ndiliti pamene kaŵirikaŵiri mwazi unathiriridwa, koma kodi nchifukwa ninji kachitidwe kameneka kanali kopanda maziko enieni?
Tsamba 14
1. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti mlingo wotsika kuposa wanthaŵi zonse wa hemoglobin ungalandiridwe?
2, 3. Ngati pali kutaika kwa mwazi kofulumira, kodi nchiyani chimafunikira, ndipo kodi vutdo lingathetsedwe motani?
4. Kodi nchifukwa ninji zoloŵa m’malo za madzi zosakhala ndi mwazi zimagwira ntchito?
5. Kodi madokotala angathandize motani wodwala kuchita ndi kutaikiridwa kwa maselo ofiira?
Tsamba 15
1. Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kufulumiza kupangidwa kwa maselo ofiira?
2-4. Mkati mwa opaleshoni, kodi kutaika kwa mwazi kungachepetsedwe motani?
Tsamba 16
1-3. Kodi ndi umboni wotani umene umasonyeza kuti nkotheka kuchita opaleshoni yaikulu popanda kuthiriridwa mwazi?
4-6. Kodi ndi maopaleshoni ambiri otani amene angatheke popanda kugwiritsira ntchito mwazi? (Onani tsamba 28, ndime 2-4.)
Tsamba 17
1. Kodi ndi zotulukapo zabwino zotani zimene zapezedwa ndi opaleshoni ya mtima kumene mwazi sunagwiritsiridwe ntchito?
2-4. Kodi odwala omwe ndi Mboni athandizira motani iwo eni ku zotulukapo zabwino koposa zimene kaŵirikaŵiri zimakhalapo pa opaleshoni yopanda mwazi?
MLUNGU WACHINAYI
Tsamba 17
5, 6. Kodi kupendedwa kwa upandu/phindu nchiyani, ndipo kodi kumagwiritsiridwa ntchito motani?
Tsamba 19
1, 2. Kodi wodwala amachita mbali yotani m’kupendedwa kwa upandu/phindu?
3-5. Kodi nchifukwa ninji kuchiritsa kwa mwazi moyenerera kwaphatikizidwa m’kupenda maupandu ndi mapindu? (Onani tsamba 31, ndime 1, 2.)
6. Kodi ndi lamulo lamakhalidwe abwino lalamulo lotani limene limasonyeza kuyenera kwanu kwakusankha kuchiritsa kwa mankhwala? (Onani tsamba 30, ndime 1-8.)
Tsamba 18 (Bokosi)
1-4. Kodi nchiyani chimene odwala omwe ndi Mboni amachita kuchotsa mantha a ogwira ntchito yazamankhwala? (Onani tsamba 28, ndime 5.)
5-7. Polingalira zimene Mboni zidzachita kuthetsa mantha a lamulo, kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kuti madokotala ndi zipatala zigwirizane nazo?
Tsamba 20
1-3. Kodi ndimotani mmene ogwira ntchito zamankhwala ena avomerezera ku kaimidwe kamene Mboni zimatenga?
4, 5. Kodi zatheka motani kuti mabwalo amilandu aloŵetsedwa m’nkhani zina za odwala omwe ndi Mboni?
Tsamba 21
1, 2. Kodi nchifukwa ninji kupita ku mabwalo amilandu sikuli njira yabwino koposa yothetsera nkhani zokhudza Mboni ndi mwazi?
3, 4. Kodi mpazifukwa zotani pamene kuliri kosayenerera kupita ku mabwalo amilandu ngakhale ngati wodwalayo ndi mwana?
5, 6. Kodi ndi kuyenera kwa kholo kotani kumene kumagwira ntchito posankha kuchiritsa kwa ana? (Onani tsamba 28, ndime 6, ndi tsamba 29, ndime 1.)
7–tsamba 22, ndime 1-3. Kodi pali zisonyezero zina zalamulo zotani zakuti makolo ali autulu kupanga zosankha zamankhwala za ana awo?
4. Kodi nchifukwa ninji makolo omwe ndi Mboni ndi ogwira ntchito zamankhwala ayenera kugwirfra ntchito pamodzi?
MLUNGU WACHISANU
Tsamba 22
5, 6. Kodi ndi mfundo zazikulu zotani zimene muyenera kukumbukira ponena za mwazi ndi pempho la Mboni la chisamaliro chamankhwala chopanda mwazi?
Tsamba 23
1-3. Ngakhale ngati ena anafa chifukwa chokana mwazi, kodi nchiyani chimene sitiyenera kunyalanyaza? (Onani tsamba 29, ndime 2-5, ndi tsamba 31, ndime 3-5.)
4, 5. Kodi nkati komwe kali kawonedwe kotsimikizirika ponena za imfa ndi mwazi?
Tsamba 24
1, 2. Kodi nchiyani chingatithandize kumvetsetsa mmene mwazi ungapulumutsiredi moyo?
3–tsamba 25, ndime 1. M’nthaŵi za Chikristu chisanakhale, kodi lingaliro la Mulungu lonena za mwazi linali lotani, ndipo nchifukwa ninji?
Tsamba 25
2. Kodi mwazi unaloŵetsedwamo motani pa Tsiku Lotetezera, ndipo kodi nchifukwa ninji tiyenera kudera nkhaŵa?
3, 4. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa Tsiku Lotetezera ndi mbali ya Yesu?
5. (a) Kodi nchifukwa chachikulu chiti chimene Akristu amasalira mwazi? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kugogomezera mopambanitsa pa maupandu a kuthiriridwa mwazi?
6, 7. (a) Kodi mwazi ngwogwirizanitsidwa motani ndi kaimidwe kathu ndi Mulungu? (b) Kodi ndi chiphunzitso chotani chimene tiyenera kumvetsetsa monga maziko a lingaliro lathu la mwazi?
8. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kaimidwe ka Mboni pa mwazi kamasonyeza ulemu kaamba ka moyo?
Tsamba 26
1, 2. Kodi mwazi umaloŵetsedwamo motani m’mtsogolo mwathu mosatha?
CN Mal & Zam 4/98