Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini a Chowonadi
1 Kope la Nsanja ya Olonda la January 1, 1994, tsamba 22, linatikumbutsa kuti magazini athu amafalitsa “nkhani za panthaŵi yake zimene zafotokoza zosoŵa zenizeni za anthu.” Tikufuna kufalitsa mofala magazini ameneŵa. Mkati mwa miyezi ya April ndi May, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndiwo zogaŵira. Khalani makamaka ndi chonulirapo cha kupeza masabusikripishoni a Nsanja ya Olonda.
2 Ntchito ya kunyumba ndi nyumba imatipatsa mpata wabwino kopambana wa kugaŵira magazini ameneŵa. Kulalikira kwa mwamwaŵi kogwira mtima ndipo maulendo obwereza zimachititsanso kugaŵiridwa kwa magazini kwanthaŵi zonse. Kuchita ntchito ya m’khwalala ndi kufikira malo a mabizinesi m’dera lathu kulinso njira zobala zipatso zowonjezera kugaŵiridwako.
3 Mitu Yokambitsirana: Kope la Nsanja ya Olonda la April 1 lili ndi mitu yakuti “Dziko Labwinopo—Kodi Ndiloto Chabe?” ndi “Dziko Labwinopo—Layandikira!” Ndithudi imeneyi njogwirizana ndi cholinga cha magazini cha kulengeza Ufumu wa Mulungu. Nkhani yachiŵiri ikumalizidwa mwa kusonyeza mmene paradaiso wosatha adzakhalira weniweni pansi pa ulamuliro wa Kristu Yesu.—Luka 23:43.
4 “Kodi Nkuti Kumene Mungapeze Chitsogozo Chodalirika?” ndilo funso limene likuyankhidwa m’kope la April 15. Makope a May adzafotokoza mosamalitsa mutu umenewu m’nkhani zakuti “Kodi Chipembedzo Chikukhutiritsa Zosoŵa Zanu?” ndi “Nkuŵerengeranji Baibulo?” Tiyenera kukhala okhoza kuyambitsa makambitsirano mosavuta ndi anthu amene amalingalira kuti moyo wawo ulibe tanthauzo ndi chifuno.
5 Kuwonjezera Zogaŵira: Nsanja ya Olonda ya January 1 inapereka malingaliro anayi a mmene tingawonjezere zogaŵira. Tinalimbikitsidwa (1) kukhala ozindikira kufunika kwa magazini. Pamene tiwaŵerenga, tiyenera kulingalira za nkhani zimene zingakhale zokopa kwambiri anthu a m’gawo lathu. Ndiponso, ngati timayenda ndi makope nthaŵi zonse, tingakhale okhoza kuwagaŵira kwa antchito anzathu, anansi, aphunzitsi, anzathu akusukulu, kapena anthu ogula zinthu.
6 Tinakumbutsidwa (2) kuchititsa maulaliki athu kukhala osavuta. Sankhani mfundo imodzi yokondweretsa, ndipo ineneni m’mawu ochepa. Ngati mungachititse magaziniwo kutengedwa ndi mwininyumbayo, iwo akhoza “kulankhula” kwa munthu amene mwaonana nayeyo kapena kwa ena a m’banjamo.
7 Chofunika china ndicho (3) kukhala wokhoza kusintha. Kuli bwino kukhala ndi nkhani zosiyanasiyana m’maganizo zokambitsirana—imodzi ya achichepere, ina ya amuna, ndi kanthu kena konena za akazi.
8 Potsirizira, tifunikira (4) kuika chonulirapo cha munthu mwini cha zogaŵira. Pamene kuli kwakuti mpingo sungathe kuika chiŵerengero choyenera cha kugaŵiridwa kwa magazini, ife aliyense payekha tikhoza kudziikira chonulirapo. Zimenezi zingatipatse chisonkhezero cha kukhala otenthedwa maganizo mowonjezereka pogaŵira magazini. Ngati tilembetsa chiŵerengero chakutichakuti cha oda ya magazini, tingakhale osonkhezereka kuchita zowonjezereka.
9 Tikufuna kuti ena adziŵe za Ufumu wa Mulungu. Tiyeni tigwiritsire ntchito mwaŵi wonse wa chithandizo chabwino kwambiri chimene magazini amapereka m’kufalitsa uthenga wa Ufumu.—Mat. 10:7.