Gaŵirani Magazini Abwino Koposa m’Dziko
1 Chifuno cha Nsanja ya Olonda chofotokozedwa ndicho “kulemekeza Yehova Mulungu monga Mfumu Ambuye wa chilengedwe chonse.” Galamukani! ili “kaamba ka kupereka chidziŵitso ku banja lonse. . . . Magazini ino imalimbikitsa chidaliro mu lonjezo la Mlengi la dziko latsopano lamtendere ndi losungika.” Mawu ogwidwa ameneŵa achokera m’magazini enieniwo. Kulondola zonulirapo zimenezi kwawachititsa kukhala magwero a chitonthozo kwa oŵerenga mamiliyoni.
2 Tidzakhala tikugaŵira magazini ameneŵa muutumiki wathu mu April ndi May. Kuti tikhale ogwira mtima, tifunikira kuzoloŵerana bwino ndi zamkati mwake. Ŵerengani kope lililonse, mukumatenga mfundo zimene mungakhoze kugwiritsira ntchito powagaŵira. Lingalirani za zimene zikudetsa nkhaŵa anthu. Kodi ndi nkhani zotani zamayanjano, banja, kapena malingaliro zimene zili m’maganizo mwa anansi anu ambiri? Yesani kulingalira za chinachake chimene munganene chimene chidzakhudza mitima yawo ndi kusonkhezera chikhumbo cha kuphunzira zowonjezereka.
3 Kusonyeza Nsanja ya Olonda ya April 1: Anthu ambiri amalakalaka dziko labwinopo, lopanda mavuto ambiri amene nthaŵi zambiri amawalanda chimwemwe chawo tsopano.
Pambuyo podzidziŵikitsa, munganene kuti:
◼ “Ndingakonde kukusonyezani ndemanga yosangalatsa imene yapangidwa m’nkhani ino yokhala ndi mutu wakuti ‘Dziko Labwinopo—Kodi Ndiloto Chabe?’ Ikuti: ‘Dzikoli, dziko lathuli, siliri konse malo abwino koposa. . . . Ndandanda ya mavuto atsopano ikuonekera kukhala yosatha.’ Mkhalidwe umenewu umakuchititsa kukhala kovuta kulingalira zabwino ponena za mtsogolo, kodi sichoncho? Komabe, ndiloleni ndikusonyezeni zimene Salmo 37:11 limanena ponena za mtsogolo.” Mutaŵerenga vesilo, funsani mwininyumba mmene akulingalirira ponena za lonjezo limeneli. Pambuyo pa ndemanga yake, mungatembenukire ku nkhani yakuti “Dziko Labwinopo—Layandikira!,” patsamba 4, ndi kunena kuti: “Malemba angapo atchulidwa pano, kuphatikizapo limene tangoŵerenga mu Salmo 37:11. Ndikhulupirira kuti mungakonde kuŵerenga nkhani zimenezi ndi kuyang’ana malembawo m’Baibulo lanu. Ndingakonde kukusiyirani iwo.” Ndiyeno tchulani chopereka cha nthaŵi zonse.
4 Kusonyeza Nsanja ya Olonda ya April 15: Nkhani ya patsamba 4 ili ndi funso lakuti: “Kodi Nkuti Kumene Mungapeze Chitsogozo Chodalirika?”
Pambuyo podzidziŵikitsa, munganene kuti:
◼ “Pali mavuto ochuluka kwambiri m’dziko lerolino, monga ngati [tchulani chinthu chimene panopo chikudetsa nkhaŵa anthu kapena mutu wankhani]. Zimatipangitsa kudabwa ngati munthu wina aliyense angapeze njira yothetsera mavuto ameneŵa. Mosangalatsa, lemba la 2 Timoteo 3:16, 17 limatitsimikizira kuti Baibulo ndilo chitsogozo ku njira ya moyo wachimwemwe ndi wachisungiko.” Mutaŵerenga mavesi ameneŵa, sonyezani mmene Nsanja ya Olonda imatithandizira kumvetsetsa chifukwa chake Baibulo lili chitsogozo chodalirika.
5 Ngati mungakonde kugaŵira Galamukani!, mungagwiritsire ntchito kope la May 8 ndi nkhani yakuti “Kodi Pali Chiyembekezo Chenicheni kwa Ana?” Mosakayikira mudzapeza kuti makolo amakhudzidwa ndi zosoŵa za ana ndi kufuna kudziŵa zimene angachite kuti awathandize.
6 Ngati tili otenthedwa maganizo ndi magazini athu, magazini abwino koposa m’dziko, tidzakhala odera nkhaŵa ndi kugaŵira masabusikripishoni kwa ena kotero kuti nawonso akhale ndi chiyembekezo cha Ufumu ndi kukhala ndi phande m’kulemekeza Yehova monga Mfumu Ambuye wa chilengedwe chonse.—Sal. 83:18.