Khalani Ofunitsitsa Kugaŵira sabusikripishoni Mu October
1 Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! zili ndi uthenga wotonthoza ndi wolimbikitsa wa mbiri yabwino yosatha. Kukhala wofunitsitsa kugaŵira sabusikripishoni kumaloŵetsamo kupatula nthaŵi ya kuŵerenga magaziniwo mosamalitsa ndi kulingalira mmene nkhanizo zingakopere anthu m’gawo lathu.
2 Choyamba, dziŵani nkhani zosonyezedwa pa chikuto. Kaŵirikaŵiri zithunzi za pa chikuto zenizenizo zidzachititsa munthu kutenga magaziniwo. Sankhani nkhani zimene mukulingalira kuti zingakhale zokopa kwa anthu a m’gawo lanu. Kodi makamaka anthuwo ngachipembedzo chimodzi? Kodi nkhaŵa zawo zazikulu nzotani? Polingalira zimenezi, mukhoza kukonzekera ulaliki wogwira mtima. Taonani maulaliki amene aikidwa pansipa.
3 Ngati mukugaŵira “Nsanja ya Olonda” ya October 1, mungasonyeze nkhani yakuti “Baibulo—Kodi Phindu Lake Lenileni Nlotani?” Munganene kuti:
◼ “Mungapeze Baibulo pafupifupi m’nyumba iliyonse m’chitaganya chathu chino. Ambiri amene ali nalo amalingalira kuti ilo lili ndi kanthu kena kopindulitsa kwambiri.” Ndiyeno mungafunse funso lachindunji, longa lakuti: “Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chimapangitsa Baibulo kukhala lapadera?” kapena, “Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chingathandize anthu ambiri kupindula ndi Baibulo?” Mwininyumba atayankha, mungakhoze kupitiriza kunena mawu oyenerera, onga akuti: “Pali umboni wambirimbiri wosonyeza kuti Baibulo nlouziridwa ndi Mulungu ndipo ndilo chitsogozo chathu chodalirika. Lili ndi chidziŵitso chimene chingatitsogolere ku moyo wosatha. [Ŵerengani Yohane 17:3.] Anthu ambiri amalilemekeza komano samadziŵa mmene angaligwiritsirire ntchito. Nkhani iyi mu Nsanja ya Olonda ikulongosola mmene inu mwininu mungagwiritsirire ntchito Baibulo kupezera mayankho a mafunso anu onena za mtsogolo. Ndifuna kukusiyirani kope limeneli.” Ndiyeno ŵerengani chiganizo chimodzi kapena ziŵiri zosankhidwa pasadakhale ndi kupitiriza kufotokoza chogaŵira cha sabusikripishoni.
4 Pogwiritsira ntchito “Nsanja ya Olonda” ya October 15, mwina mungakonde mafikidwe osavuta onga awa:
◼ “Pafupifupi munthu aliyense watayikiridwa ndi wokondedwa mu imfa. Nkhani iyi ikudzutsa mafunso akuti, ‘Kodi Mkhalidwe wa Akufa Ngwotani?’ Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chimachitika pamene munthu afa? [Yembekezerani yankho.] Ngati mungafune kudziŵa mmene Baibulo limayankhira funso limenelo, ndingakonde kukusiyirani kope ili la magazini. Ngati mungafune kuti magazini ameneŵa azitumizidwa kwa inu kaŵiri pa mwezi kwa chaka chonse, mungathe kulembetsa sabusikripishoni pa K25.00 chabe.”
5 “Galamukani!” wa November 8 akufotokoza umodzi wa maumboni ambiri osonyeza kulephera kwa chipembedzo chonyenga. Pogwiritsira ntchito nkhani zakuti “Pamene Chipembedzo Chichirikiza Mbali Ina mu Nkhondo,” mungafunse funso ili:
◼ “Ngati Yesu akanakhala pano, kodi muganiza kuti akanalingalira motani ponena za chiwawa chonsechi chimene chilipo? [Yembekezerani yankho.] Yesu anatiphunzitsa kukonda aliyense, ngakhale adani athu. Komabe, zipembedzo zambiri zimene zimanena kuti ndi Zachikristu zimachirikiza mbali ina m’mikangano ya ndale. Kodi muganiza kuti zimenezo zimayambukira motani anthu amene amafuna kukhala mogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa? [Yembekezerani yankho.] Kope ili la Galamukani! likunena za funso limenelo ndi kulongosola mmene Ufumu wa Mulungu udzaperekera yankho.”
6 Kuwonjezera pa kugaŵira magazini pa khomo lililonse, tsimikizirani kugaŵiranso masabusikripishoni. Chopereka chake ndicho K25.00 pa chaka.