Oyamikira Chifukwa cha Zimene Tili Nazo
1 “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Tonsefe tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga chifukwa cha kudzimana kwakukulu kumene kunachitidwa ndi Yehova Mulungu ndi Mwana wake yemwe kaamba ka ife! Mwa mwazi wokhetsedwa wa Kristu, tapatsidwa mwaŵi wa moyo wosatha, kanthu kena kamene palibe munthu amene angatipatse.
2 Kodi tingasonyeze motani chiyamikiro chathu? Pali anthu ambiri amene akumva ludzu la chidziŵitso choona, chimene chingapezeke m’Mawu Opatulika a Mulungu mokha. Chifuniro cha Yehova nchakuti iwo adziŵe choonadi. (1 Tim. 2:4) Timasonyeza kuyamikira kwathu choonadi mwa ‘kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.’ (Luka 4:43) Kukhala ndi phande ndi mtima wonse mu ntchito imeneyi kumasonyeza kuti timayamikira kuti Kristu anatifera ndi kuti tikufuna kumtsanzira mwa kumvera mokhulupirika lamulo lake la kupanga ena kukhala ophunzira.—Mat. 28:19, 20.
3 Kodi nziti zimene zili njira zina za kulalikira zotseguka kwa ife? Kodi nkotheka kwa ife kulembetsa monga apainiya othandiza panthaŵi ndi nthaŵi? Ena angakhale okhoza kuchita utumiki waupainiya wokhazikika ataŵerengera mtengo wake. Mwa kugwiritsira ntchito mipata yabwino kwambiri imeneyi, tingawonjezere nthaŵi imene timathera pa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Mwina kalelo inu munalingalirapo za kulembetsa, koma panali zopinga. Mwina mwake mikhalidwe yanu yasintha. Ngati ndi choncho, kodi mwalingalirapo mwamphamvu za kuloŵa mu utumiki wa upainiya kapena mwa kutumikira monga mpainiya wothandiza?
4 Kuyamikira kwathu kumakhala kwakukulu pamene tiyang’ana zimene zikuchitika motizinga. Pali chiwawa chomawonjezereka, kudana, ndi nkhondo padziko lonse. Paulo anafotokoza bwino lomwe nthaŵi yathuyi kukhala “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Tim. 3:1) Pakati pa mikhalidwe yosautsa imeneyi, ife tili ndi uthenga wabwino wochuluka woti tiuze ena. Tili ndi magazini aŵiri abwino kwambiri, Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Magazini ameneŵa angadzetse chitsitsimulo chenicheni kwa awo amene amawaŵerenga. Mwezi uno tikugaŵira sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. Kuyamikira zimene tili nazo kuyenera kutisonkhezera kukhala omasuka kugaŵana ndi ena.—Aheb. 13:16.
5 Tikuthokoza Yehova chifukwa cha kutipatsa apainiya ogwira ntchito zolimba. M’mipingo ina mungakhale apainiya amene amafola magawo awo nthaŵi zambiri. Oterowo angalingalire za kukatumikira kudera lina m’dziko muno kumene kuli kofunikiradi thandizo, malinga ndi mmene mikhalidwe ingalolere. Woyang’anira dera wanu angakhale ndi malingaliro ena othandiza ponena za nkhaniyi.
6 Pali zifukwa zambiri za kukhala oyamikira chifukwa cha zimene tili nazo, ndithudi zinthu zabwino zochuluka. Kuyamikira kwathu Yehova kungasonyezedwe bwino koposa mwa kudziŵikitsa dzina lake ndi zifuno zake kwa ena.—Yes. 12:4, 5.