Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini a Nthaŵi Zathu Zofulumira!
1 Zochitika zogwedeza dziko zimene zikuchitika zikukwaniritsa ulosi wa Baibulo! Pamene tikusinkhasinkha zimene zikuchitika m’dziko limene tikukhalamo ndiponso m’gulu la teokrase, tingamvetsetse chifukwa chake tiyenera kufulumira kulalikira “uthenga wabwino” wa Ufumu. (Marko 13:10) Zimenezi zikutipatsa chifukwa chochitira utumiki wathu mwachangu m’mwezi wa April.
2 Kufunika kwake kwa uthenga wathu kukugogomezeredwa ndi ntchito yapadera imene tidzachita mwezi uno. Tikuyembekezera mwachidwi kutulutsidwa kwa Uthenga wa Ufumu umene tidzagaŵira m’April ndi May. Kuti akulitse chikondwerero chathu m’ntchitoyi limodzinso ndi chidwi mwa anthu a m’gawo lathu, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! adzakhala ndi nkhani za panthaŵi yake zimene zikugogomezera tanthauzo la ulosi la zochitika za dziko zovutitsa maganizo. Kodi tingakonzekere motani ulaliki umene udzachititsa anthu kufuna magaziniwo ndipo mwina sabusikripishoni?
3 Mosakayikira mungakhoze kukhala ndi ulaliki wogwira mtima mwa kugwiritsira ntchito njira zoyambirira zotsatirazi: (1) Sankhani nkhani ina m’magazini imodzi imene mukuganiza kuti idzakopa anthu akwanuko. (2) Sankhani mawu kapena lemba logwidwa mawu m’nkhani imeneyi imene mukukhulupirira kuti idzachititsa chidwi mwininyumba. (3) Konzani ulaliki wachidule wophatikizapo moni waubwenzi, funso kapena mawu osonyeza mfundo ina yosangalatsa ya Malemba, ndi mmene mudzawapemphera moona mtima kuti alandire magaziniwo. Monga momwe mukuonera, zimenezi nzapafupi ndipo nzosavuta. Mwinamwake mungakhale ndi wofalitsa wina amene mumagwira naye ntchito mu utumiki kuti mukonzekere naye ulalikiwo.
4 Popeza kuti “Galamukani!” wa May 8 ali ndi funso lakuti, “Kodi Ano Ndiwo Masiku Otsiriza?,” mungapende mfundo zili pakamutu kakuti “Masiku Otsiriza” patsamba 11 m’buku la “Kukambitsirana.” Mwina mungayambe mwa kunena kuti:
◼ “Tadza kudzakambitsirana nanu tanthauzo la zochitika zosautsa zimene zikuchitika m’dziko. Taonani zimene nkhaniyi ikunena . . . ”
5 “Nsanja ya Olonda” ya April 1 ili ndi funso lakuti: “Chipembedzo—Kodi ndi Nkhani Yosayenera Kukambitsirana?” Pogaŵira magaziniwo, munganene kuti:
◼ “Kaŵirikaŵiri anthu amanena kuti chipembedzo ndi nkhani imene ili yosayenera kukambitsirana chifukwa ili nkhani yobutsa mkangano kwambiri. Muganiza bwanji?” Ndiyeno sonyezani mawu ali m’nkhaniyo.
6 Mwina mungakhale mukugwiritsira ntchito “Nsanja ya Olonda” ya April 15 imene ili ndi nkhani yakuti “Kodi Choonadi cha Chipembedzo Chingapezeke?” Mwina munthu angamvetsere mutayamba ndi mawu otsatirawa:
◼ “Popeza pali zipembedzo zambiri lerolino, anthu ena amakayikira ngati choonadi cha chipembedzo chingapezeke. Nkhaniyi ikusonyeza mmene inu ndi ine tingapezere yankho lokhutiritsa pa funso limeneli. . . . ”
7 Musanayambe ntchitoyo, bwanji osayeseza ulaliki wanu ndi wofalitsa wina kuti muuzoloŵere? Mosakayikira mudzapatsana malingaliro amene adzakuchititsani kukhala ogwira mtima kwambiri ndi kukupatsani chidaliro chokulirapo.
8 Pamene mapeto a dongosolo ili akuyandikira, tiyenitu tiwonjezere kuyesayesa kwathu kothandiza oona mtima kuchoka m’Babulo Wamkulu. (Chiv. 18:4) Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amachita zazikulu m’ntchito imene sidzabwerezedwa konse imeneyi. Tikuthokoza Yehova potipatsa ziŵiya zabwino kwambiri zimenezi zoti tizigwiritsire ntchito! Yesayesani kupeza sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda mwezi uno.