Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/95 tsamba 1
  • “Khalani Odikira”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Khalani Odikira”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kukhalabe Maso’?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • “Khalanibe Oganiza Bwino Ndipo Khalani Maso”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • “Dikirani” Chifukwa Nthawi ya Chiweruzo Yafika
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Tsanzirani Yesu pa Nkhani Yokhala Maso
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 7/95 tsamba 1

“Khalani Odikira”

1 Pamene Yesu ananena mawuwo olembedwa pa Mateyu 26:38-41 (NW), anali kuyandikira nthaŵi yovuta kwambiri m’moyo wake waumunthu. Imeneyo inali kudzakhala nthaŵi yofunika koposa m’mbiri yonse ya anthu. Chipulumutso cha anthu onse chinali pachiswe. Ophunzira a Yesu anafunikira ‘kukhala odikira.’

2 Lerolino taima pa mphembenu pa kufika kwa Yesu kudzachita ntchito ya mbali ziŵiri, ya wolanditsa ndi ya wakupha. Monga Akristu odikira ozindikira kufulumira kwa nthaŵi, sitimangokhala manja lende tikumayembekezera chilanditso. Tikudziŵa kuti tiyenera kukhala okonzeka nthaŵi zonse. Tifunikira kupitiriza ‘kugwiritsa ntchito ndi kuyesetsa’ mu utumiki wathu kwa Yehova. (1 Tim. 4:10) Bwanji nanga za ife monga munthu payekha? Kodi tikukhala odikira?

3 Kudzipenda Ife Eni: Yesu anachenjezanso kuti: “Mudziyang’anire nokha.” (Luka 21:34, 35) Tiyenera kudzipenda ife eni, tikumatsimikizira kuti tili “osalakwa ndi oona . . . pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka.” (Afil. 2:15) Kodi tikukhala monga Akristu tsiku ndi tsiku, tikumatsanzira Yesu ndi kuyenda monga mwa malamulo osonyezedwa m’Mawu a Mulungu? Tiyenera kupeŵa khalidwe losakhala Lachikristu losonyezedwa ndi dziko limene “ligona mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19; Aroma 13:11-14) Pamene tidzipenda tokha mwa Malemba, kodi tikudikiradi monga momwe Yesu analangizira?

4 Akulu ayenera kukhala atcheru ndi akhama posamalira mathayo awo mumpingo, akumazindikira kuti adzaŵerengeredwa mlandu wa mmene amasamalirira gulu la nkhosa. (Aheb. 13:17) Mitu ya mabanja ili ndi thayo lapadera la kutsogolera mabanja awo m’njira za Yehova. (Gen. 18:19; Yos. 24:15; yerekezerani ndi 1 Timoteo 3:4, 5.) Ndiponso, nkofunika kwambiri chotani nanga kwa ife tonse kukwaniritsa lamulo la Malemba la kukondana wina ndi mnzake! Ndiko chizindikiro cha Chikristu choona.—Yoh. 13:35.

5 Khalani Atcheru Kuchenjeza Ena: Kukhala odikira sikumangokhudza kudziyang’anira tokha. Tili ndi ntchito ya kupanga ena kukhala ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Chikondi cha mnansi chiyenera kutisonkhezera kuchenjeza ena kuti iwo akapulumuke chiwonongeko chimene dzikoli likuyang’anizana nacho. Thayo limeneli lili pa Akristu onse. Ili mbali yofunika kwambiri pa kulambira kwathu. (Aroma 10:9, 10; 1 Akor. 9:16) Kaŵirikaŵiri timakumana ndi mphwayi ndi chitsutso chachikulu pantchito yopulumutsa moyo imeneyi. Tili ndi thayo la kulimbikira, ngakhale ngati ochuluka anyalanyaza chenjezo lathu. (Ezek. 33:8, 9) Chikondi chenicheni pa Mulungu ndi mnansi chidzatisonkhezera kuchita khama.

6 Ino si nthaŵi ya kuganiza kuti zonse zili bwino. Sitiyenera kulola zosamalira za moyo wa tsiku ndi tsiku kuticheutsa, kapena kuloŵerera kwambiri m’zokondweretsa za dongosolo lino kwakuti zikhala msampha. (Luka 21:34, 35) Tsopano, kuposa ndi kalelonse, pali kufunika kwa kuona kufulumira kwa nthaŵi. Nthaŵi yakuti Yesu Kristu apereke chiweruzo pa dongosolo loipa ili ikuyandikira mofulumira. Amene ali ogalamuka, atcheru, ndi odikira ndiwo okha adzapulumuka. Ngati tamvera malangizo a Yesu ndi ‘kulimbika kupulumuka zonse zimene zidzachitika,’ tidzakhala othokoza chotani nanga!—Luka 21:36.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena