Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/96 tsamba 1
  • Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Malonjezo a Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Chikhulupiriro Chimatipatsa Mphamvu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Sonyezani Chikhulupiriro Chozikidwa pa Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 6/96 tsamba 1

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

1 Mtumwi Paulo anamasulira chikhulupiriro kukhala “chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.” Anawonjezera kuti “wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Mulungu].” (Aheb. 11:1, 6) Paulo anatisonkhezera kusonyeza chikhulupiriro, kuchichulukitsa, ndi kuchitsata.—2 Akor. 4:13; Akol. 2:7; 2 Tim. 2:22.

2 Pali zitsanzo zambiri za chikhulupiriro zotchulidwa m’Baibulo. Mu Ahebri chaputala 11, Paulo akupereka mndandanda wautali wa mboni zimene zinasonyeza chikhulupiriro chosasweka. Pamndandandawo pali Abele, amene anali woyamba kuphedwa kaamba ka chikhulupiriro chake. Nowa anaikidwa pa mndandandawo chifukwa mwa chikhulupiriro chake anasonyeza mantha aumulungu omwe anali ofunikira kupulumutsa banja lake. Abrahamu akuthokozedwa kaamba ka chikhulupiriro chake ndi kumvera kwake. Mose akutamandidwa chifukwa chakuti mwa chikhulupiriro chake anapitiriza kuchirimika monga amene anaona Uyo wosaoneka. Mndandanda wa zitsanzo unali wautali kwakuti Paulo anati nthaŵi siikanamulola kupitiriza kusimba onse. Tili oyamikira chotani nanga kuti tingathe kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa kupenda ‘mayendedwe awo opatulika ndi chipembedzo’!—2 Pet. 3:11.

3 M’zaka za zana loyamba, Yesu anafunsa funso lakuti: “Mwana wa munthu pakudza iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?” (Luka 18:8) Pamenepo, kodi tili nazo zitsanzo za chikhulupiriro pakati pathu lerolino? Kodi tikuona amuna ndi akazi, achichepere ndi achikulire omwe, amene akusonyeza chikhulupiriro chosagwedera mwa Yehova monga momwe anachitira anthu a Mulungu m’nthaŵi za Baibulo?

4 Zitsanzo za Chikhulupiriro Zamakono: Zitsanzo zapadera za chikhulupiriro zilipo zochuluka pakati pathu! Chikhulupiriro cha oyang’anira amene amatitsogolera nchofunika kuchitsanzira. (Aheb. 13:7) Koma ameneŵa sindiwo okha opereka chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro. Palinso okhulupirika omwe akuyanjana ndi mpingo uliwonse amene ali ndi mbiri yaitali ya utumiki wokhulupirika kwa Yehova, kaŵirikaŵiri wochitidwa mkati mwa mikhalidwe yovuta kwambiri.

5 Tiyenera kusirira alongo athu okhulupirika, amene kwa zaka zambiri, apirira chitsutso cha amuna awo. Makolo opanda mnzawo wa muukwati akumana ndi vuto la kulera okha ana. Palinso akazi amasiye okalamba pakati pathu amene samaphonya konse ntchito za pampingo ngakhale kuti alibe banja lowathandiza. (Yerekezerani ndi Luka 2:37.) Timachita chidwi ndi chikhulupiriro cha aja omwe amapirira matenda osatha. Ambiri akupitiriza kutumikira mokhulupirika ngakhale kuti ali ndi zowalepheretsa kulandira mwaŵi wowonjezereka wa utumiki. Palinso Mboni zachichepere zimene molimba mtima zasonyeza chikhulupiriro mosasamala kanthu za chitsutso pasukulu. Kudzipereka kwathu kwaumulungu kumalimbirapo nthaŵi zonse pamene tiona apainiya okhulupirika omwe akupirira chaka ndi chaka poyang’anizana ndi mavuto osaneneka. Mofanana ndi Paulo, nthaŵi singatilole kusimba zokumana nazo zonse za muutumiki wa Ufumu ndi ntchito za chikhulupiriro zochitidwa ndi abale ndi alongo ameneŵa!

6 Zitsanzo za anthu okhulupirika zimenezi zimatitonthoza ndi kutilimbikitsa. (1 Ates. 3:7, 8) Tingachite bwino kutsanzira chikhulupiriro chawo chifukwa chakuti “ochita [mokhulupirika, NW] amsekeretsa [Yehova].”—Miy. 12:22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena