Kodi Ndani Ali Woyeneretsedwa Kulalikira?
1 Ponena za utumiki, kodi munamvapo monga Mose? Iye anati: “Mverani, [Yehova, NW], ine ndine munthu wosoŵa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire inu ndi kapolo wanu.” (Eks. 4:10) Ngati mumamva mofananamo, mungamafune kupewa kulalikira. Komabe, Yesu “anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni.” (Mac. 10:42) Choncho kodi timakhala motani alaliki oyeneretsedwa a uthenga wabwino?
2 Si maphunziro apamwamba akudziko amene amatiyeneretsa kuchita utumiki. Paulo ananena kuti “sa[na]itanidwa ambiri a nzeru [zakuthupi, NW]” ndi kuti “nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu.” (1 Akor. 1:26; 3:19) Yesu anasankha atumwi ake pakati pa anthu ogwira ntchito—anayi a iwo antchito ya usodzi. Atsogoleri achipembedzo onyadawo anali kuwaona mosuliza monga “anthu osaphunzira ndi opulukira.” Malinga ndi miyezo yakudziko, atumwi sanali oyeneretsedwa kulalikira. Komabe, nkhani yokhudza mtima ya Petro imene anapereka pa tsiku la Pentekoste inasonkhezera anthu 3,000 kubatizidwa!—Mac. 2:14, 37-41; 4:13.
3 Yehova Amatiyeneretsa Kulalikira: Paulo analengeza kuti: “Kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu.” (2 Akor. 3:5) Yehova, Magwero a nzeru, waphunzitsa mamiliyoni kulalikira choonadi cha Ufumu kwa ena. (Yes. 54:13) Kugwira mtima ndi kubala zipatso kwa ntchito imeneyi kungaonedwe mwa 338,491 amene anabatizidwa chaka chatha monga ‘makalata ovomerezetsa’ amoyo. (2 Akor. 3:1-3) Tili ndi zifukwa zabwino zolalikirira molimba mtima ndipo motsimikizira ponena za zinthu zimene taphunzira kwa Yehova.
4 Gulu la Mulungu lakhazikitsa programu yophunzitsa atumiki yapadziko lonse. Mwa Malemba ndi zothandizira kuphunzira Baibulo zambiri zosiyanasiyana, timasonkhanitsidwa ndi kuphunzitsidwa kukhala ‘oyenerera, okonzeka’ kulalikira. (2 Tim. 3:16, 17) Ambiri achita chidwi ndi maphunziro amene amapezeka m’zofalitsa za Sosaite. Mwachitsanzo, magazini ena a ku Sweden anati: “Chikhulupiriro chimene Mboni za Yehova zimalalikira chimachirikizidwa ndi sayansi ya Baibulo yapamwamba kwambiri yophunzitsidwa padziko lonse.”
5 Ndi malangizo operekedwa m’misonkhano yathu isanu ya pamlungu, programu yathu ya kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, kupereka uphungu mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki, chithandizo chaumwini choperekedwa ndi ena amene ali atumiki achidziŵitso, ndipo koposa zonse, chichirikizo cha mzimu woyera wa Yehova, tili otsimikiza kuti Yehova amationa kukhala oyeneretsedwa mokwanira kulalikira. Inde, “monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.”—2 Akor. 2:17.
6 Ngati tigwiritsira ntchito bwino mwaŵi wa maphunziro a teokrase operekedwa ndi Mulungu kudzera mwa gulu lake, tilibe chifukwa chopeŵera kulalikira kapena chochitira mantha. Tingalalikire kwa ena mwachimwemwe, tikumakhala ndi chidaliro chakuti Yehova adzadalitsa zoyesayesa zathu.—1 Akor. 3:6.