Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/97 tsamba 3-4
  • Tiyenera Kukhalanso Aphunzitsi, Osati Alaliki Chabe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tiyenera Kukhalanso Aphunzitsi, Osati Alaliki Chabe
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Tingapangire ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Kuona Mmene Ntchito Yamwamsanga Yopanga Ophunzira Ikupitira Patsogolo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Yang’anirani ‘Luso Lanu la Kuphunzitsa’
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Maphunziro a Baibulo Enanso Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 12/97 tsamba 3-4

Tiyenera Kukhalanso Aphunzitsi, Osati Alaliki Chabe

1 Kwaoneka kuti “Mboni za Yehova zazunguliradi dziko lonseli pochitira umboni.” Kodi zakhoza bwanji zimenezo? Osati mwa mphamvu kapena nyonga ya anthu, koma mwa mzimu wa Mulungu umene ukusonkhezera atumiki ake kugwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana kuti akwaniritse ntchito yawo yolalikira ndi yophunzitsa.—Zek. 4:6; Mac. 1:8.

2 Masamba olembedwa ndiwo njira yogwira mtima yochitira ntchito yathu yolalikira. Pazaka zambiri zapitazo, Mboni za Yehova zasindikiza ndi kugaŵira mabuku ochulukitsitsa monga othandizira kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu. Mu 1997 Yearbook muli malipoti osonyeza kuti chiŵerengero cha mabuku amene anafalitsidwa nchachikulu zedi. Kufikira lero, makope a New World Translation oposa 91 miliyoni afalitsidwa. Pachaka chimodzi, chiŵerengero cha magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! osindikizidwa ku United States chinakwera ndi 7.1 peresenti. Ku Germany, chiŵerengero cha magazini osindikizidwa chinakwera ndi 35 peresenti. Pamagazini onse amene amasindikizidwa kumeneko, chigawo chimodzi mwa atatu anali a munda wa Russia.

3 Kodi nchifukwa ninji mabuku ambiri motero akufunika? Padziko lonse, unyinji wa anthu alabadira pamene talimbikitsidwa kuti tizichitira umboni kulikonse kumene tingapeze anthu. Ambirife tikamafutukula ntchito yathu yochitira umboni—pamakwalala, pamsewu, ndi m’gawo la m’malo amalonda—timagaŵira mabuku ambiri ndithu kwa anthu amene amachita nawo chidwi. Mwa onsewo, ambiri sanapezepo mpata woti nkumva uthenga wa Ufumu. Ndiye mipingo imakhala ndi zofalitsa zosiyanasiyana kuti azigaŵira m’mbali zonse za utumiki, kuti akwaniritse chosoŵa chimenechi.

4 Kodi Cholinga Chathu Nchiyani Pogaŵira Mabuku? Cholinga chathu si kungogaŵira mabuku chabe. Ntchito yopanga ophunzira njambali ziŵiri—kulalikira ndi kuphunzitsa. Choyamba, tili ndi mwaŵi wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu, kuti anthu adziŵe kuti uwo ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu. (Mat. 10:7; 24:14) Kupita kwa nthaŵi kwasonyeza kuti mabuku athu onena za Baibulo ngothandiza kwambiri ndipo ndiwo njira yogwira mtima yodzutsira chidwi ndi kupereka kwa ena chidziŵitso cha Ufumu.

5 Chachiŵiri, ngati tikufuna kupanga ophunzira, tiyenera kuwaphunzitsa zinthu zonse zimene Yesu analamula. (Mat. 11:1; 28:19, 20) Ndiponso, mabuku amachita mbali yofunika pakukhomereza choonadi m’mitima ya anthu, kuwathandiza kukhala ophunzira.

6 Amene amalandira mabuku angakhale ‘akumva mawu,’ koma nkosatheka kuti adzakhala akuwachita mawuwo ngati tidzangowasiya okha. (Yak. 1:22-25) Ndi oŵerengeka okha omwe angakhale ophunzira popanda wina wowatsogolera. (Mac. 8:30, 31) Afunikira mphunzitsi wowathandiza kuzindikira choonadi cha m’Malemba. (Mac. 17:2, 3) Cholinga chathu nchowathandiza kupita patsogolo mpaka adzipatulire ndipo abatizidwe, ndi kuwaphunzitsa kukhala okhoza bwino kuphunzitsa enanso.—2 Tim. 2:2.

7 Aphunzitsi Ochuluka Akufunika Kwambiri: Pamene tikulalikira, timalengeza uthenga wabwino poyera. Komabe, kuphunzitsa kumaphatikizapo kulangiza munthu pang’onopang’ono. Kulalikira kumapangitsa ena kumva uthenga wa Ufumu, pomwe kuphunzitsa kumathandiza anthu kukhulupirira uthenga wabwino ndi kuchitapo kanthu. (Luka 8:15) Mphunzitsi samangolengeza iyayi; amafotokoza, namakambitsirana ndi munthu mogwiritsira ntchito zitsanzo zabwino, amapereka maumboni, ndipo amasonkhezera.

8 Ambiri mwa ife tiyenera kukhalanso aphunzitsi, osati alaliki chabe. (Aheb. 5:12a) Kugaŵira mabuku nkofunika pantchito yathu, koma cholinga chachiŵiri cha utumiki wathu chimadalira kotheratu pa zimene timachita monga aphunzitsi. Indedi timakondwa tikagaŵira mabuku, koma kuti tikwaniritse utumiki wathu ndithu, tisamaganize kuti cholinga chathu nchokhacho chogaŵira mabuku basi. (2 Tim. 4:5) Kugaŵira mabuku ndiyo njira yabwino yotsegulira mipata yophunzitsira ena choonadi.

9 Pangani Maulendo Obwereza Kuti Muyambe Maphunziro a Baibulo: Ambirife tingakhale titagaŵira mabuku, mabrosha, ndi magazini angapo ndithu, moti mwina tili ndi kampambo ka maulendo obwereza. Tizipeza nthaŵi yokwanira yomabwererako kuti tikakulitse chidwi. Cholinga chathu chachikulu pobwererako si chokasiya mabuku ena koma chokalimbikitsa anthu kuŵerenga kuti apindule ndi zimene ali nazo kale. Kodi ife enife tikanapita bwanji patsogolo mwauzimu pakanapanda kukhala wina yemwe ankabwerabwera kudzatithandiza kupeza chidziŵitso cholongosoka?—Yoh. 17:3.

10 Bwererani kwa onse amene anachita chidwi ncholinga chokayamba phunziro la Baibulo mwina ndi brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Zofalitsa ziŵiri zimenezi zimalongosola uthenga wa Ufumu mwanjira yosavuta kuumvetsetsa. Brosha lakuti Mulungu Amafunanji lili ndi kosi yokwana bwino, yokhudza ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Buku la Chidziŵitso limathandiza munthu kuphunzitsa choonadi mwatsatanetsatane, komanso mosavuta, momveketsa bwino, ndi mwachidule.

11 Programu yophunzitsa mosavuta yofotokozedwa m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, imathandiza mphunzitsi kulangiza mosavuta ndi kuthandiza munthu kuphunzira mosavuta. Sungani kope la mphatika imeneyo kuti muzipenda njira ndi maluso ophunzitsira amene akhala ogwira mtima. Malingaliro ena omwe ikufotokoza ngonena za mmene munthu angasonyezere kuti akukondwera nayedi wophunzirayo, kuchuluka kwa ndime zoyenera kuphunzira panthaŵi imodzi, mochitira ndi mafunso osakhudzana ndi nkhaniyo, mmene onse aŵiri, mphunzitsi ndi wophunzira angakonzekere phunzirolo pasadakhale, ndi mmene munthu angatsogolere wophunzira ku gulu la Yehova. Mwa kutsatira malingaliro amenewo, ambirife, kuphatikizapo achatsopano, tidzakhoza kuchititsa maphunziro opita patsogolo.

12 Malipoti Ochokera Kumunda Akuti Zinthu Zikuyenda Bwino: Brosha lakuti Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso lakhala lothandiza kwenikweni pakufulumiza ntchito yopanga ophunzira. Mbale wina wa ku Bolivia atangolandira brosha lakuti Mulungu Amafunanji, analigwiritsira ntchito nthaŵi yomweyo nkuyamba phunziro ndi munthu wina. Patapita miyezi inayi, pamsonkhano wachigawo, wophunzira ameneyo anali wina mwa opita ku ubatizo achimwemwe!

13 Ambiri akusonkhezereka kupatulira miyoyo yawo kwa Yehova atangotsiriza kuphunzira buku la Chidziŵitso. Mumpingo wina ku Angola, chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo amene ofalitsa amachititsa, chinawonjezeka kuchoka pa 190 mpaka 260, ndipo chiŵerengero cha opezeka pamsonkhano chinaŵirikiza kuchoka pa 180 mpaka 360 pa miyezi inayi yokha, chiyambire kugwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso m’dera limenelo. Pasanathe nthaŵi, anaona kuti nkofunika kungokhazikitsa mpingo wina.

14 Mbale wina atayamba kuphunzitsa ndi buku la Chidziŵitso, anati kuchititsa phunziro “nkosavuta ngati wochititsayo azingofunsa mafunso, nkumaŵerenga malemba ogwirizana ndi nkhani, nkumatsimikiza kuti wophunzirayo akumvetsetsa.” Ngakhale kuti ankaganiza kuti omwe angathe kuchititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo anali ofalitsa odziŵa bwino kwenikweni, anazindikira kuti nayenso angathe. Anadzati: “Ngati ineyo ndingathe, aliyense angathe.”

15 Timakwaniritsa cholinga chopanga ophunzira mwa kuchititsa maphunziro a Baibulo monga mbali ya utumiki wathu. Amene akulitsa luso lochitira utumiki umenewu apeza kuti ngwokhutiritsa zedi ndipo ngwopindulitsa kwenikweni. Tiyenitu nafe tidzanenedwe kuti “tikulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbika konse [“momasuka kwambiri,” NW].”—Mac. 28:31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena