Gwiritsani Ntchito Mabrosha Kuti Mukope Maganizo ndi Mtima Womwe
1 Choonadi cha Baibulo chiyenera kuperekedwa mwa njira yakuti chizikopa zonse, maganizo ndi mtima. Pamene Yesu anali kulongosolera omvetsera ake choonadi, anali kusankha nkhani zimene zinali zowakondweretsa ndi zowasonkhezera. (Luka 24:17, 27, 32, 45) Kuti tikhale achipambano mu utumiki wathu zimadalira kwambiri pa kuyesayesa kwathu kuzindikira zosoŵa zauzimu za omvetsera athu.
2 Mabrosha angakhale zida zamphamvu zosonkhezerera maganizo ndi kufikira pamtima anthu amene timakumana nawo mu utumiki. Lingalirani pasadakhale amene angamvetsere uthenga umene uli m’brosha lililonse lomwe likugaŵiridwa mu August:
—Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Anthu amene ali ndi mavuto azachuma kapena amene akumanapo ndi tsoka angayamikire uthenga wotonthoza umenewu wonena za tsogolo lopanda mavuto.
—Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani? Achinyamata amene amaganizira kwambiri za tsogolo lawo angapindule ndi mayankho ochokera m’Baibulo omwe ali m’broshali.
—Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Ana ndi awo amene saŵerenga bwino angathandizidwe ndi zithunzi ndi malemba ochuluka osonyezedwawo kuti amvetse zifuno za Mulungu.
—Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso. Aliyense amene amagwirizana ndi boma angamvetsere uthenga umenewu wonena za mmene Ufumu wa Mulungu udzathetsera mavuto a mtundu wa anthu.
—Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Anthu amene okondedwa awo anamwalira adzalikonda broshali. Ambiri sakudziŵa ngati pali chiyembekezo chilichonse kwa anthu akufa. Momveka bwino Baibulo limanena za lonjezo la Mulungu la chiukiriro. (Yoh. 5:28, 29) Broshali limalongosola chifukwa chake tingakhale otsimikizira kuti imfa idzathetsedwa potsirizira pake. Malonjezo a Mulungu amatothoza ndiponso amakhutiritsa.
—Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? Munthu wokonda kwambiri chipembedzo angamvetsere choonadi cholongosoledwa bwino chimenechi chotsutsa chiphunzitso chachikulu cha Dziko Lachikristu.
3 Lidziŵeni bwino brosha lililonse, ndipo onani mmene mungaligwiritsire ntchito bwino m’gawo lanu. Onani tsamba lothera la Utumiki Wathu Waufumu wa July 1998 kuti muone maulaliki achitsanzo. Yehova adalitsetu zoyesayesa zanu zakuti mukhudze maganizo ndi kufika mitima ya anthu.—Marko 6:34.